Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chimachitika N’chiyani Kwenikweni Munthu Akamwalira?

Kodi Chimachitika N’chiyani Kwenikweni Munthu Akamwalira?

Kodi Chimachitika N’chiyani Kwenikweni Munthu Akamwalira?

“Mizimu yonse siifa, ngakhale ya anthu oipa . . . Kuzunzika kwake [sikutha] popeza imapatsidwa chilango cha moto wosazima ndipo siifa.”​—Clement of Alexandria, wolemba mabuku wa m’zaka za m’ma 100 ndi 200 C.E.

MOFANANA ndi Clement, anthu amene amalimbikitsa chiphunzitso chakuti helo ndi malo ozunzirako anthu amaganiza kuti munthu ali ndi mzimu umene suufa. Kodi Baibulo limaphunzitsa zimenezi? Taonani zimene Mawu a Mulungu amanena poyankha mafunso otsatirawa.

Kodi munthu woyamba, Adamu, anali wosakhoza kufa? Adamu atangolengedwa, Mulungu anam’patsa lamulo lakuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Adamu anali munthu wokhoza kufa.

Kodi chinachitika n’chiyani Adamu atachimwa? Chilango chimene Mulungu anapereka sichinali kuzunzika kosatha kuhelo. Baibulo la Katolika la Malembo Oyera limafotokoza chiweruzo chimene Mulungu anapereka kuti: ‘Uzidzadya cakudya cako pakudza thukuta, mpaka tsiku limene udzabwerere ku dothi, kumene unafumira’ko, cifukwa ndiwe dothi, ndipo udzasandukanso dothi.’ (Genesis 3:19) Apa chiweruzo cha Mulungu sichikusonyeza mwanjira iliyonse kuti mbali inayake ya Adamu siinafe.

Kodi pali munthu amene ndi wosakhoza kufa? Palibe munthu woteroyo. Baibulo limanena pa Mlaliki 3:20 kuti: “Onse apita ku malo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.” Mtumwi Paulo analemba kuti: “Cifukwa cake monga cakwaipa [uchimo] cinalowa m’dziko la pansi pano cifukwa ca munthu m’modzi [Adamu], ndi imfa cifukwa ca cakwaipa, ndipo conco imfa inalowa mwa anthu onse cifukwa anacimwa onse.” (Aroma 5:12, Malembo Oyera) Anthu onse ndi ochimwa, ndipo n’chifukwa chake onse amafa.

Kodi akufa amadziwa kapena kumva chilichonse? Mawu a Mulungu amati: “Amoyo adziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa kanthu.” (Mlaliki 9:5, Malembo Oyera) Pofotokoza zimene zimachitika munthu akamwalira, Baibulo limanena kuti: “Abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika,” kapena kuti amasiya kuganiza. (Salmo 146:4) Ngati akufa “sadziwa kanthu” ndipo amasiya kuganiza, angadziwe bwanji kuti akuzunzika kuhelo?

Yesu Khristu sananene kuti anthu akufa amazindikira chilichonse. M’malo mwake iye anayerekezera imfa ndi tulo chifukwa munthu amene ali m’tulo sazindikira chilichonse. * (Yohane 11:11-14) Koma mwina ena angatsutse ponena kuti Yesu anaphunzitsadi kuti helo ndi malo amoto ndipo anthu ochimwa adzaponyedwa m’motowo. Tiyeni tione zimene Yesu ananena zokhudza helo.

[Mawu a M’munsi]