Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kudziwa Zoona Zake za Helo Kungakuthandizeni Bwanji?

Kodi Kudziwa Zoona Zake za Helo Kungakuthandizeni Bwanji?

Kodi Kudziwa Zoona Zake za Helo Kungakuthandizeni Bwanji?

ANTHU amene amaphunzitsa kuti helo ndi malo ozunzirako anthu amalakwira kwambiri Yehova Mulungu chifukwa si zimene iye amachita ndiponso n’zosiyana ndi makhalidwe ake. N’zoona kuti Baibulo limanena kuti Mulungu adzawononga anthu oipa. (2 Atesalonika 1:6-9) Koma kukwiya kwa Mulungu chifukwa chotsata chilungamo sindilo khalidwe lake lalikulu.

Mulungu si wankhanza kapena wokonda kulipsira. Ndipotu iye amachita kufunsa kuti: “Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa?” (Ezekieli 18:23) Ngati Mulungu sakondwera nayo imfa ya oipa, zingatheke bwanji kuti iye azisangalala kuona anthu akuzunzika kwamuyaya?

Khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. (1 Yohane 4:8) Indedi, “Yahve [Yehova] ngwabwino kwa onse, ndi wozicitira cisoni nchito zake zonse.” (Salmo 144:9, Malembo Oyera; [Salmo 145:9, Buku Lopatulika]) Mulungu amafunanso kuti ifeyo tizimukonda kuchokera pansi pa mtima.​—Mateyo 22:35-38.

Kodi Mumatumikira Mulungu Chifukwa Chomukonda Kapena Choopa Helo?

Chiphunzitso chakuti mizimu imazunzika kuhelo chimalimbikitsa anthu kuopa Mulungu mosayenera. Mosiyana ndi zimenezi, munthu amene waphunzira choonadi cha Mulungu ndi kuyamba kumukonda amamuopa m’njira yoyenera. Lemba la Salmo 111:10 limati: “Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma.” Kuopa Mulungu kumeneku sikuli ngati kuopa nyama yolusa, koma ndi kupereka ulemu waukulu kwa Mlengi. Chifukwa cha ulemu umenewu, timakhala ndi mantha oyenera ndipo timapewa kuchita zinthu zomwe iye sakondwera nazo.

Taganizirani zimene zinachitikira mayi wazaka 32, dzina lake Kathleen, atadziwa zoona zake za helo. Iye poyamba ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo pamoyo wake ankangokhalira mapwando, chiwawa, kudzida komanso chiwerewere. Iye anati: “Ndimati ndikayang’ana mwana wanga wamkazi wachaka chimodzi ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndikuchitira mwana wangazi n’zabwino? Inetu ndidzapsa ku helo chifukwa cha zimenezi.’” Kathleen anayesa njira zosiyanasiyana kuti asiye mankhwala osokoneza bongo, koma palibe inathandiza. Iye anati: “Ndinkafuna kukhala munthu wabwino, koma zinthu pamoyo wanga ndi m’dzikoli sizinali kuyenda. Ndinkaona kuti palibe chifukwa chilichonse chokhalira munthu wabwino.”

Kenako Kathleen anakumana ndi Mboni za Yehova. Iye anati: “Ndinaphunzira kuti kulibe moto wa helo. Umboni wa m’Malemba umene ndinapatsidwa unali womveka. Nditadziwa kuti sindikapsa m’moto wa helo, mtima wanga unakhala pamtendere.” Kathleen anaphunziranso za lonjezo la Mulungu lakuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi popanda anthu oipa. (Salmo 37:10, 11, 29; Luka 23:43) Iye ananena mosangalala kuti: “Apa ndinakhala ndi chiyembekezo chenicheni chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso.”

Kodi Kathleen akanatha kusiya mankhwala osokoneza bongo popanda mantha akuti akapsa ndi moto kuhelo? Mwiniwakeyo anati: “Ndikayamba kufuna kwambiri mankhwala osokoneza bongo, ndinkapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova Mulungu kuti andithandize. Ndinkakumbukira kuti Mulungu amadana ndi zizolowezi zodetsa ngati zimenezi, ndipo sindinafune kumukhumudwitsa. Iye anamva mapemphero anga.” (2 Akorinto 7:1) Chifukwa choopa kukhumudwitsa Mulungu, Kathleen anagonjetsa vuto lake la mankhwala osokoneza bongo.

Zoonadi, kukonda Mulungu ndi kumuopa moyenera, osati kuopa kuzunzika kuhelo, kuyenera kutilimbikitsa kuchita chifuniro cha Mulungu kuti tikhale osangalala mpaka kalekale. Wamasalmo analemba kuti: “Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m’njira zake.”​—Salmo 128:1.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 9]

KODI NDANI AMENE ADZAMASULIDWA KU HELO?

Mabaibulo ena amasokoneza anthu pomasulira mawu awiri osiyana a Chigiriki, Geʹen·na ndi Haiʹdes, ngati mawu amodzi akuti “helo.” M’Baibulo, mawu akuti Geʹen·na amanena za chiwonongeko chotheratu, popanda chiyembekezo chakuti munthu adzaukanso. Mosiyana ndi zimenezi, pali chiyembekezo chakuti anthu amene ali mu Haiʹdes, kapena kuti Hade, adzaukitsidwa.

N’chifukwa chake Yesu atamwalira ndi kuukitsidwa, mtumwi Petulo anatsimikizira omvera ake kuti Yesu “sanasiyidwe mu helo.” (Machitidwe 2:27, 31, 32; Salmo 16:10, King James Version) Mawu amene anawamasulira kuti “helo” pavesi limeneli ndi mawu a Chigiriki akuti Haiʹdes. Yesu sanapite ku malo amoto. Hade kapena “helo” kumene Yesu anapitako ndi kumanda. Koma kuwonjezera pa Yesu, anthu enanso adzamasulidwa ndi Mulungu kuchokera ku Hade.

Ponena za kuuka kwa akufa, Baibulo limati: “Imfa ndi helo zinapereka akufa amene anali mmenemo.” (Chivumbulutso 20:13, 14, King James Version) Kuchotsa akufa ku “helo” kumatanthauza kubwezeretsa moyo kwa onse amene Mulungu akuona kuti ndi oyenera kuukitsidwa. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Kunena zoona, tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri, pamene tidzaona okondedwa athu amene anamwalira akubwerako amoyo kumanda. Yehova, Mulungu wa chikondi chopanda malire, adzachita zimenezi.