Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mboni za Yehova Zimathetsa Maukwati a Anthu?

Kodi Mboni za Yehova Zimathetsa Maukwati a Anthu?

Kodi Mboni za Yehova Zimathetsa Maukwati a Anthu?

“NGATI mkazi kapena mwamuna walowa chipembedzo china, ukwati umatha.” Izi n’zimene anthu ambiri amanena. Nthawi zina chenjezo limeneli limapita kwa mkazi kapena mwamuna amene wasankha kukhala wa Mboni za Yehova. Koma kodi mfundo imeneyi imakhala yoona nthawi zonse?

Munthu wapabanja akayamba kusonyeza chidwi ndi chipembedzo china kapena kusintha zimene wakhala akukhulupirira kwa nthawi yaitali, mwamuna kapena mkazi wake zingamuvute kumvetsa ndipo m’pake kutero. Mnzakeyo angade nkhawa, angakhumudwe kapena kuipidwa kumene.

Nthawi zambiri amene amayamba kuganiza zosintha chipembedzo amakhala mkazi. Ngati mkazi wanu akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, kodi ukwati wanu ungakhudzidwe bwanji? Ngati ndinu mkazi ndipo mukuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, kodi mungachite chiyani kuti muchepetse nkhawa imene mwamuna wanu angakhale nayo?

Zimene Mwamuna Wina Ananena

Mark ndi mkazi wake amakhala ku Australia. Atatha zaka 12 ali m’banja, mkazi wa Mark anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mwamunayu anati: “Banja lathu linali losangalala ndipo ndinali ndi ntchito yabwino. Moyonso unali wokoma. Kenako mkazi wanga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mwadzidzidzi ndinaona kuti moyo wanga usokonekera. Poyamba, chidwi chimene mkazi wanga anali nacho pa Baibulo chinkandisowetsa mtendere. Koma atandiuza kuti wasankha kubatizidwa kuti akhale wa Mboni za Yehova, nkhawa yanga inakula kwambiri.”

Mark anayamba kuda nkhawa kuti mwina chipembedzo chimene mkazi wake wayamba chithetsa ukwati wawo. Poopa zimenezi, iye anaganiza zoletsa mkazi wake kuphunzira Baibulo komanso kucheza ndi Mboni. Mark sanapupulume, koma anadikira kuti papite nthawi. Kodi ukwati wawo unatani?

Mark mwiniwakeyo akuti: “Ndikusangalala chifukwa ukwati wathu panopa ndi wolimba kuposa kale. Kungoyambira pamene mkazi wanga anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova zaka 15 zapitazo, ukwati wathu wakhala ukulimbiralimbirabe.” Kodi n’chiyani chathandiza kuti ukwati wawo uziyenda bwino? Mark akuti: “Ndikayang’ana m’mbuyo, ndikuona kuti chathandiza kwambiri n’chakuti mkazi wanga amatsatira malangizo abwino amene amapezeka m’Baibulo. Iye wakhala akuyesetsa kundilemekeza.”

Malangizo Ochokera kwa Akazi Amene Zinthu Zawayendera Bwino

Ngati ndinu mkazi ndipo mukuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, kodi mungachite chiyani kuti muchepetse nkhawa imene mwamuna wanu angakhale nayo? Tamverani zimene akazi ena a m’mayiko osiyanasiyana ananena.

Sakiko, wa ku Japan: “Ndakhala m’banja kwa zaka 31 ndipo ndili ndi ana atatu. Papita zaka 22 kuyambira pamene ndinakhala wa Mboni za Yehova. Kukhala m’banja ndi mwamuna amene si wachipembedzo chako kumavuta nthawi zina. Koma ndimayesetsa kutsatira uphungu wa m’Baibulo wakuti tizikhala ‘ofulumira kumva, odekha polankhula, osafulumira kukwiya.’ (Yakobe 1:19) Ndimayesetsa kuchita zinthu mokoma mtima kwa mwamuna wanga ndiponso kugonjera zofuna zake ngati sizikusemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zathandiza kuti banja lathu liziyenda bwino.”

Nadezhda, wa ku Russia: “Ndakhala m’banja kwa zaka 28 ndipo papita zaka 16 kuyambira pamene ndinabatizidwa kukhala wa Mboni. Ndisanaphunzire Baibulo, sindinkaganiza kuti mwamuna wanga ndiye mutu wa banja. Nthawi zambiri ndinkachita zinthu popanda kumufunsa. Koma m’kupita kwa nthawi, ndinapeza kuti kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kunathandiza kuti banja lathu likhale lamtendere ndi losangalala. (1 Akorinto 11:3) Pang’onopang’ono ndiyamba kugonjera mosavuta, ndipo mwamuna wanga waona mmene ndasinthira.”

Marli, wa ku Brazil: “Ndili ndi ana awiri ndipo ndakhala m’banja kwa zaka 21. Ndinabatizidwa kukhala wa Mboni zaka 16 zapitazo. Ndinaphunzira kuti Yehova Mulungu amafuna kuti anthu okwatirana asalekane. Choncho ndimayesetsa kukhala mkazi wabwino, ndipo ndimalankhula ndi kuchita zinthu zimene zingakondweretse Yehova komanso mwamuna wanga.”

Larisa, wa ku Russia: “Nditakhala wa Mboni za Yehova zaka pafupifupi 19 zapitazo, ndinazindikira kuti ndifunika kusintha kwambiri moyo wanga. Mwamuna wanga panopa amatha kuona kuti Baibulo landithandiza kuti ndizimulemekeza ndi kumuyamikira kwambiri. Poyamba, sitinkagwirizana pa nkhani ya mmene tingalerere ana, koma panopa vuto limeneli linatha. Mwamuna wanga amalola kuti ndizipita ndi ana athu ku misonkhano yathu yachipembedzo chifukwa chakuti iye akudziwa kuti anawo akuphunzitsidwa zinthu zimene zingawathandize.”

Valquíria, wa ku Brazil: “Ndili ndi mwana mmodzi ndipo ndakhala m’banja kwa zaka 19. Papita zaka 13 kuyambira pamene ndinakhala wa Mboni za Yehova. Poyamba, mwamuna wanga sankafuna kuti ndizilalikira. Koma ndinaphunzira kumuyankha modekha akamandifotokozera nkhawa zake komanso kumuthandiza kuona kuti Baibulo likundithandiza kukhala munthu wabwino. Pamapeto pake, mwamuna wanga anayamba kumvetsa ubwino wakuti ndizilalikira. Masiku ano, amandithandiza kwambiri pa ntchito yanga yauzimu. Ndikapita kumadera akumidzi kukaphunzira Baibulo ndi anthu, iye amandiperekeza pagalimoto yake ndipo amandiyembekeza moleza mtima mpaka kumaliza maphunzirowo.”

Baibulo Limathandiza

Ngati mkazi kapena mwamuna wanu akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, musaope kuti zimenezi zithetsa ukwati wanu. Amuna ndi akazi ambiri padziko lonse apeza kuti Baibulo limathandiza muukwati.

Mwamuna wina amene si wa Mboni za Yehova ananena moona mtima kuti: “Poyamba ndinkavutika maganizo mkazi wanga atayamba chipembedzo cha Mboni za Yehova, koma tsopano ndimaona kuti kupirira kwanga kwandipindulitsa.” Mwamuna winanso anati: “Kukhulupirika kwa mkazi wanga, khama lake pochita zinthu ndiponso kusaphwanya kwake mfundo zomwe amatsatira, kwandichititsa kulemekeza Mboni za Yehova. Banja lathu lapindula kwambiri chifukwa cha mfundo zachipembedzo zimene mkazi wanga amatsatira. Timamvetsetsana ndipo timaona kuti ukwati wathu ndi mgwirizano wa moyo wathu wonse.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 13]

Kodi Mboni za Yehova Zimauona Bwanji Ukwati?

Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu owuziridwa ndi Mulungu. Choncho izo siziona mopepuka zimene Baibulo limanena pankhani ya ukwati. Taonani zimene Baibulo limanena poyankha mafunso otsatirawa:

Kodi Mboni za Yehova zimalimbikitsa anthu achipembedzo chawo kuthetsa ukwati ndi munthu yemwe si wa Mboni? Ayi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati pali m’bale amene ali ndi mkazi wosakhulupirira, ndipo mkaziyo akulola kukhala naye, asam’siye mkaziyo; ndipo mkazi amene mwamuna wake ndi wosakhulupirira, koma mwamunayo akulola kukhala naye, asam’siye mwamuna wakeyo.” (1 Akorinto 7:12, 13) Choncho, Mboni za Yehova zimamvera lamulo limeneli.

Kodi mkazi yemwe ndi wa Mboni za Yehova amauzidwa kuti asamamvere zofuna za mwamuna wake yemwe si wa Mboni? Ayi. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Inu akazi, muzigonjera amuna anu, kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.”​—1 Petulo 3:1, 2.

Kodi Mboni za Yehova zimaphunzitsa kuti mwamuna ali ndi ulamuliro wopanda malire pa mkazi wake? Ayi. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna; ndi mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Mkazi wachikhristu amalemekeza mwamuna wake monga mutu wa banja. Komabe ulamuliro wa mwamuna uli ndi malire ndipo adzadziyankhira yekha kwa Mulungu ndi Khristu. Choncho, ngati mwamuna akufuna kuti mkazi wake achite zinthu zosemphana ndi malamulo a Mulungu, mkazi wachikhristu ‘ayenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.’​—Machitidwe 5:29.

Kodi Mboni za Yehova zimaphunzitsa kuti kuthetsa ukwati ndi koletsedwa? Ayi. Yesu Khristu ananena kuti: “Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosudzula mkazi wake ndi kukwatira wina achita chigololo, kupatulapo ngati am’sudzula chifukwa cha dama [kugonana ndi munthu amene sunakwatirane naye].” (Mateyo 19:9) Choncho Mboni za Yehova zimagwirizana ndi mfundo imene Yesu ananena yakuti ukwati ungathe ngati wina wachita chigololo. Komabe, iwo amakhulupiriranso kwambiri kuti ukwati suyenera kutha pa zifukwa zazing’ono. Iwo amalimbikitsa anthu achipembedzo chawo kumvera mawu a Yesu akuti: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi. . . . Choncho, chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”​—Mateyo 19:5, 6.