Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Kuti Ndiwo Okha Amene Adzapulumuke?

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Kuti Ndiwo Okha Amene Adzapulumuke?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Kuti Ndiwo Okha Amene Adzapulumuke?

Mboni za Yehova zimaona kuti chipembedzo chawo ndi choona. Chifukwa ngati si choncho, akanasintha chipembedzo. Mofanana ndi anthu a zipembedzo zina, Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti zidzapulumuka. Komabe iwo amakhulupiriranso kuti ntchito yoweruza kuti ndi ndani amene adzapulumutsidwe si yawo. Mulungu ndiye Woweruza Wamkulu. Iye ndi amene amasankha anthu oti awapulumutse.​—Yesaya 33:22.

Mawu a Mulungu amanena kuti anthu amene adzapulumuke sayenera kungofuna kupulumuka, koma ayeneranso kumvera zimene wowapulumutsa akuwauza kuti achite. Mwachitsanzo, yerekezerani kuti munthu wina akuyenda mu nkhalango ndiye kenaka wasochera. Iye akusowa chochita ndipo akulakalaka munthu wina atamupulumutsa. Kodi iye atapatsidwa thandizo, angapulumuke kapena ayi? Zingadalire mmene iye angachitire ndi thandizolo. Ngati iye ndi wonyada, mwina angakane kumvera zimene womupulumutsa akumuuza. Koma ngati ndi wodzichepetsa, angachite zimene womupulumutsayo akumuuza kuti achite ndipo angapulumuke.

Mofanana ndi zimenezi, anthu amene adzapulumuke ndi okhawo amene amamvera zimene Yehova Mulungu, Mpulumutsi wa anthu, amanena. Chipulumutso ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, koma si anthu onse amene adzailandire. Yesu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu, anati: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wa kumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wa kumwamba.”​—Mateyo 7:21.

Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Mulungu adzapulumutsa anthu okhawo amene amakhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu ndiponso kutsatira ziphunzitso zake. (Machitidwe 4:10-12) Mawu a Mulungu amatchula zinthu zitatu zofunika kwambiri zimene zingathandize munthu kuti adzapulumutsidwe. Zinthuzo ndi izi:

(1) “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” Yesu anauza zimenezi ophunzira ake. (Yohane 13:35) Yesu anapereka moyo wake m’malo mwa ena, ndipo zimene anachitazi zimasonyeza kufunika kwa chikondi. Motero anthu omwe amakonda anzawo, ndiye kuti amasonyeza khalidwe limene limafunika kwambiri kuti munthu adzapulumuke.

(2) “Dzina lanu ndalidziwitsa kwa iwo.” Yesu ananena zimenezi popemphera kwa Atate wake. (Yohane 17:26) Yesu anadziwa kuti dzina la Mulungu lakuti Yehova ndi lofunika kwambiri kwa Atate wakeyo. Iye anapemphera kuti dzina la Atate wake “liyeretsedwe.” (Mateyo 6:9) Kuyeretsa dzina la Mulungu kumaphatikizapo kulidziwa dzinalo komanso kuliona kuti ndi lofunika ndiponso loyera. Mofanana ndi Yesu, anthu amene akufuna kudzapulumuka ayenera kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu. Ayeneranso kuphunzitsa ena za dzinalo ndiponso makhalidwe a Mulunguyo. (Mateyo 28:19, 20) Ndipotu ndi anthu okhawo oitana pa dzina la Mulungu amene adzapulumuke.​—Aroma 10:13.

(3) “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” Yesu ananena mawu amenewa kwa Pontiyo Pilato. (Yohane 18:36) Masiku ano ndi anthu ochepa chabe amene amakhulupirira Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma limene Yesu ndiye Mfumu yake. M’malo mwake, anthu ambiri amakhulupirira mabungwe a anthu. Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene adzapulumuke amachirikiza mokhulupirika Ufumu wa Mulungu ndipo amaphunzitsa ena za mmene Ufumuwo udzamasulire anthu onse okhulupirika ku mavuto awo onse.​—Mateyo 4:17.

Atadziwa zinthu zina zofunika kuti munthu apulumuke, ophunzira a Yesu anafunsa kuti: “Ndiye angapulumuke ndani?” Iye anayankha kuti: “Zinthu zosatheka kwa anthu n’zotheka ndi Mulungu.” (Luka 18:18-30) Mboni za Yehova zimayesetsa mwakhama kukwaniritsa zinthu zofunika zimenezi kuti zidzapulumuke. Izo zimalimbikiranso kuthandiza ena kuti adzapulumuke.