Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wokonda Chilungamo

Wokonda Chilungamo

Yandikirani Mulungu

Wokonda Chilungamo

Aheberi 10:26-31

KODI munthu wina anakuchitiranipo nkhanza kapena zinthu zina zopanda chilungamo ndipo sanalangidwe komanso sizinam’khudze n’komwe? Zimakhala zovuta kupirira zinthu zoterezi, makamaka ngati amene wachita zimenezo ndi munthu yemwe afunika kukukondani ndi kukusamalirani. Mungadabwe kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu amalola zinthu zoterezi?’ * Zoona zake n’zakuti Yehova Mulungu amadana ndi zinthu zonse zopanda chilungamo. Mawu ake, Baibulo, amatitsimikizira kuti anthu ouma mitima amene ndi chizolowezi chawo kuchita zoipa, sadzathawa chilango cha Mulungu. Tiyeni tikambirane mawu a mtumwi Paulo amene ali pa Aheberi 10:26-31.

Paulo analemba kuti: “Ngati timachita uchimo dala pambuyo podziwa choonadi molondola, sipatsalanso nsembe ina ya machimo athu.” (Vesi 26) Anthu omwe amachimwa mwadala amakhala ndi mlandu waukulu. Chifukwa chiyani? Choyamba, sikuti iwo amangochita tchimo kamodzi chifukwa cha kufooka, zomwe tonsefe nthawi zina timachita popeza tinabadwa ochimwa. M’malo mwake, ndi chizolowezi chawo kuchita tchimo. Chachiwiri, iwo amachimwa mwadala. Malinga ndi Baibulo lina, iwo “amachita zoipa ndi cholinga.” (The Bible in Basic English) Mitima yawo yopotoka ndi yodzaza ndi zoipa zokhazokha. Chachitatu, sikuti amachita machimowo chifukwa cha umbuli. Iwo ‘amadziwa choonadi molondola’ ponena za chifuniro cha Mulungu ndi njira zake.

Kodi Mulungu amaona bwanji anthu osalapa, amene mitima yawo ndi yoipa? Paulo anati: “Sipatsalanso nsembe ina ya machimo.” Nsembe ya Khristu, yomwe ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu, imaphimba machimo amene timachita chifukwa chobadwa ochimwa. (1 Yohane 2:1, 2) Koma anthu amene ali ndi chizolowezi chochimwa ndipo salapa, amasonyeza kuti sayamikira mphatso yamtengo wapatali imeneyi. Mulungu amaona kuti iwo ‘amapondaponda Mwana wa Mulungu . . . ndipo amayesa ngati chinthu wamba magazi a’ Yesu. (Vesi 29) Mwa zochita zawo, amanyoza Yesu ndipo amaona magazi ake ngati “chinthu chachabe” chopanda phindu mofanana ndi magazi a munthu wochimwa. (Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) Anthu osayamika amenewa sapindula ndi nsembe ya Khristu.

Ndiyeno kodi anthu oipa zidzawayendera bwanji? Mulungu wachilungamo akuyankha kuti: “Kubwezera ndi kwanga; ndidzabwezera ndine.” (Vesi 30) Onse amene ali ndi chizolowezi chochimwa n’kumavutitsa ena asamale. Munthu sangamaswe mwadala malamulo olungama a Mulungu popanda kulangidwa. Pajatu choipa chitsata mwini. (Agalatiya 6:7) Kaya papite nthawi yaitali bwanji, iwo m’tsogolomu adzaweruzidwa ndi Mulungu, nthawi ikadzakwana yakuti iye achotse zinthu zonse zopanda chilungamo padziko lapansi pano. (Miyambo 2:21, 22) Paulo akuchenjeza kuti: “Ndi chinthu choopsa kugwa m’manja mwa Mulungu wamoyo.”​—Vesi 31.

Kudziwa kuti Yehova Mulungu salekerera tchimo ladala kumatonthoza komanso kumalimbikitsa, makamaka anthu amene anachitiridwa zinthu zopweteka ndi munthu woipa wouma mtima. Choncho, nkhani yobwezera tiyenera kuisiya ndi mtima wonse m’manja mwa Mulungu, amene amadana ndi zinthu zonse zopanda chilungamo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Ngati mukufuna kudziwa chifukwa chimene Mulungu walolera kuvutika, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? masamba 106-114, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.