Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Machiritso a Masiku Ano Amachokera kwa Mulungu?

Kodi Machiritso a Masiku Ano Amachokera kwa Mulungu?

Kodi Machiritso a Masiku Ano Amachokera kwa Mulungu?

M’MAYIKO ena, si zachilendo kuona anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana akupita ku malo opatulika kumene ambiri akapita kumeneko amanena kuti achiritsidwa matenda awo “osachiritsika.” Pamene m’mayiko enanso anthu ochiritsa amanena kuti amachiritsa anthu pogwiritsa ntchito mphamvu zozizwitsa. Komanso m’madera ena, mumachitika misonkhano yachipembedzo yachikoka kumene anthu odwala amasiya njinga zimene amagwiritsa ntchito ndipo ena amataya ndodo zawo n’kumanena kuti achiritsidwa.

Anthu ochiritsa mozizwitsa amakhala a zipembedzo zosiyanasiyana ndipo ena amanena anzawo kuti ndi ampatuko, abodza komanso kuti amachita zachikunja. Ndiye funso lingakhale lakuti, Kodi Mulungu amachita zozizwitsa kudzera mwa magulu otsutsana? Ndipotu Baibulo limanena kuti: “Mulungu, si Mulungu wa chisokonezo, koma wa mtendere.” (1 Akorinto 14:33) Ndiyeno kodi machiritso amenewa amachokeradi kwa Mulungu? Ochiritsa ena amanena kuti amachiritsa mu mphamvu ya Yesu. Tiyeni tione mmene Yesu ankachiritsira anthu.

Mmene Yesu Anachiritsira Anthu

Yesu anachiritsa anthu odwala mosiyana kwambiri ndi mmene anthu amachiritsira masiku ano. Mwachitsanzo, Yesu anachiritsa aliyense amene anabwera kwa iye kuti athandizidwe. Pakakhala gulu la anthu, iye sanali kuchita kusankha anthu oti awachiritse n’kusiya ena osawachiritsa. Ndipo matenda a anthu amene Yesu anawachiritsa anali kutheratu komanso nthawi zambiri anthuwo anali kuchira nthawi yomweyo. Baibulo limanena kuti: “Onse m’khamulo anali kuyesetsa kuti am’khudze, chifukwa mphamvu zinali kutuluka mwa iye ndi kuchiritsa onsewo.”​Luka 6:19.

Nthawi zambiri anthu ochiritsa mwa mapemphero akalephera kuchiritsa munthu, amaimba mlandu wodwalayo kuti alibe chikhulupiriro. Komatu Yesu anachiritsa ngakhale anthu amene sanali kumukhulupirira. Mwachitsanzo, nthawi ina Yesu anangopita kwa munthu wakhungu asanaitanidwe n’komwe ndi kumuchiritsa. Kenako Yesu anafunsa munthuyo kuti: “Kodi ukukhulupirira mwa Mwana wa munthu?” Munthuyo anayankha kuti: “Kodi ameneyo ndani ndimudziwe Bambo, kuti ndikhulupirire mwa iye?” Yesu anamuuza kuti: “Ndi amene akulankhula nawe tsopano.”​—Yohane 9:1-7, 35-38.

Mwina mungadabwe kuti, ‘Ngati chikhulupiriro sichinali chofunika kuti munthu achiritsidwe ndi Yesu, n’chifukwa chiyani nthawi zambiri Yesu anali kuuza anthu amene anawachiritsa kuti: “Chikhulupiriro chako chakuchiritsa”?’ (Luka 8:48; 17:19; 18:42) Pamene Yesu ananena zimenezi, ankatanthauza kuti anthu amene anapita kwa iye chifukwa chomukhulupirira anachiritsidwa, pamene anthu amene sanafune kupita kwa iye anataya mwayi woterowo. Amene anachiritsidwa sanachiritsidwe chifukwa cha chikhulupiriro chawo, koma chifukwa cha mphamvu ya Mulungu. Ponena za Yesu Baibulo limati: ‘Mulungu anam’dzoza ndi mzimu woyera ndi mphamvu. Ndi kuti popeza Mulungu anali naye, anayendayenda m’dziko nachita zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.’​—Machitidwe 10:38.

Kawirikawiri anthu amene amachiritsa masiku ano amaoneka kuti amafuna ndalama. Maumboni akusonyeza kuti anthu amene amachiritsa mwa mapemphero ndi akatswiri posonkhetsa ndalama. Akuti munthu wina wochiritsa mozizwitsa, anapeza ndalama zokwana madola 89 miliyoni a ku United States m’chaka chimodzi chokha chifukwa cha machiritso amene anapanga pa dziko lonse. Nawonso mabungwe a matchalitchi amapeza phindu kuchokera kwa anthu ochokera ku mayiko ena amene amapita ku malo opatulika pofuna kuchiritsidwa. Mosiyana ndi zimenezi, Yesu sanali kusonkhetsa ndalama kuchokera kwa anthu amene anawachiritsa. Panthawi ina iye anapereka ngakhale chakudya kwa anthu amene anawachiritsa. (Mateyo 15:30-38) Pamene Yesu anatumiza ophunzira ake kukalalikira, anawauza kuti: “Chiritsani odwala, ukitsani anthu akufa, yeretsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyo 10:8) Nanga n’chifukwa chiyani zochita za ochiritsa a masiku ano n’zosiyana kwambiri ndi za Yesu?

Kodi Mphamvu “Yochiritsayo” Imachokera Kuti?

Kwa zaka zambiri, akatswiri ena azachipatala akhala akufufuza zonena za anthu achipembedzo amene amati amachiritsa anthu. Kodi iwo apeza zotani? Malinga ndi nyuzipepala ina ya ku London, dokotala wa ku England amene wakhala akufufuza nkhaniyi kwa zaka 20 anati: “Palibe umboni uliwonse wa chipatala umene umatsimikiza kuti nkhani zokopa za anthu ochiritsa mozizwitsa n’zoona.” (Daily Telegraph) Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amakhulupirira ndi mtima wonse kuti amachiritsidwa ndi mphamvu ya zinthu zakale zopatulika, ochiritsa achipembedzo, kapena mwa kupita ku malo opatulika. Kodi si zotheka kuti amangowapusitsa?

Mu ulaliki wake wotchuka wa paphiri, Yesu ananena kuti anthu onyenga achipembedzo adzanena kwa iye kuti: ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife . . . sitinachite zamphamvu zambiri m’dzina lanu?’ Koma iye adzawayankha kuti: “Sindinakudziweni konse chiyambire! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.” (Mateyo 7:22, 23) Pochenjeza za mphamvu imene anthu oterewa amakhala nayo, mtumwi Paulo anati: “Kukhalapo kwa wosamvera malamuloyo kukutheka mwa mphamvu za Satana. Adzachita ntchito iliyonse yamphamvu ndi zizindikiro zabodza ndi zodabwitsa, ndi kusalungama ndi chinyengo chilichonse.”​—2 Atesalonika 2:9, 10.

Ndiponso, “kuchiritsa” kogwiritsa ntchito zinthu zakale zopatulika, mafano ndi zifanizo sikungachokere kwa Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Mawu a Mulungu amanena momveka bwino kuti: “Thawani kupembedza mafano,” ndiponso kuti “pewani mafano.” (1 Akorinto 10:14; 1 Yohane 5:21) “Kuchiritsa” kwa njira imeneyi ndi machenjera ena a Mdyerekezi ofuna kupatutsa anthu pa kulambira koona. Ndipotu Baibulo limati: “Satana iye mwini amadzisandutsa mngelo wa kuwala.”​—2 Akorinto 11:14.

N’chifukwa Chiyani Yesu ndi Atumwi Ankachiritsa Anthu?

Machiritso enieni amene analembedwa m’Malemba Achigiriki Achikristu, anasonyeza kuti Yesu ndi atumwi anatumidwa ndi Mulungu. (Yohane 3:2; Aheberi 2:3, 4) Machiritso a Yesu analinso ogwirizana ndi uthenga umene anali kulalikira. Iye “anayendayenda m’Galileya yense, kuphunzitsa m’masunagoge mwawo ndi kulalikira uthenga wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa anthu matenda amtundu uliwonse.” (Mateyo 4:23) Kuwonjezera pa kuchiritsa, Yesu anadyetsa anthu ambirimbiri, analamulira mphepo, ndipo anaukitsa ngakhale anthu akufa. Ntchito zamphamvu zonsezi zinasonyeza zimene Yesu adzachitire anthu omvera pamene akulamulira mu Ufumu wake. Uwutu ndi uthenga wabwino kwambiri!

Pamene Yesu, atumwi ndi ena onse amene anapatsidwa mphatso za mzimu anafa, ntchito zamphamvu zoterozo kapena kuti mphatso za mzimu zinatha. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kaya pali mphatso za kunenera, zidzatha. Kaya kulankhula malilime [kozizwitsa], kudzatha; ngakhale mphatso ya kudziwa zinthu [mouziridwa ndi Mulungu], idzatha.” (1 Akorinto 13:8) Kodi zinatero chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti cholinga cha zimenezi chinali kudziwikitsa Yesu kuti ndi Mesiya wolonjezedwa ndiponso kuti Mulungu anali kuyanja mpingo wachikhristu. Ndiyeno cholinga chimenechi chitakwaniritsidwa, ntchito zamphamvu zoterozo, kuphatikizapo kuchiritsa, ‘zinatha’ ndipo n’zosafunikiranso.

Komabe, machiritso a Yesu ali ndi uthenga wofunikira kwa ife masiku ano. Tikamamvetsera ndi kukhulupirira zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu, tidzayembekeza mwachidwi nthawi imene ulosi wouziridwa uwu udzakwaniritsidwe mwauzimu ndiponso mwakuthupi: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”​—Yesaya 33:24; 35:5, 6; Chivumbulutso 21:4.