Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Yesu ankapanga chiyani pantchito yake ya ukalipentala?

Bambo ake a Yesu omulera anali kalipentala. N’chifukwa chake nayenso anali kalipentala. Panthawi yomwe ankayamba utumiki wake, ali ndi “zaka pafupifupi 30,” anthu ankamutcha kuti “mwana wa mmisiri wamatabwa” komanso “mmisiri wa matabwa.”​—Luka 3:23; Mateyo 13:55; Maliko 6:3.

N’kutheka kuti kumene Yesu ankakhala, anthu ankafuna kwambiri zipangizo za ulimi zopangidwa ndi matabwa, monga mapulawo ndiponso goli. Komanso anthu ankakonda kupita kwa akalipentala, kukapangitsa zinthu ngati matebulo, mipando, mabokosi osungiramo zinthu, zitseko, mafelemu a mawindo, maloko a matabwa ndiponso nsanamira. Nthawi zina kalipentala ankatha kugwira ntchito yomanga nyumba.

M’chitsanzo chake china, Yohane M’batizi anatchula nkhwangwa, ndipo n’kutheka kuti Yesu ndiponso akalipentala ena ankagwiritsira ntchito chipangizo chimenechi podula mitengo. Akagwetsa mitengoyo, ankatha kupangira pompo zimene akufunazo, kapena ankatha kunyamula matabwawo kukapangira zinthuzo ku shopu. N’zosakayikitsa kuti ntchito imeneyi inkafunika munthu wamphamvu ndithu. (Mateyo 3:10) Yesaya anatchulanso zipangizo zina zimene akalipentala a m’nthawi imeneyo ankagwiritsira ntchito. Iye anati: “Mmisiri wa mitengo atambalitsa chingwe; nalilemba ndi cholembera, nalikonza ndi ncherero, nalilemba ndi zolinganizira, nalifanizira monga mawonekedwe a munthu, monga munthu wokongola, kuti likhale m’nyumba.” (Yesaya 44:13) Akatswiri a zinthu zakale amavomereza kuti kale kwambiri anthu ankagwiritsira ntchito mipeni yachitsulo yodulira matabwa, mahamala opangidwa ndi miyala ndiponso misomali ya mkuwa. (Eksodo 21:6; Yesaya 10:15; Yeremiya 10:4) Choncho, Yesu ayenera kuti ankagwiritsira ntchito zida ngati zimenezi.

Kodi anthu “osunga ndalama” amene Yesu anawatchula mu fanizo lake lina anali ndani, ndipo ankachita zotani?

Yesu ananena za mbuye amene anadzudzula kapolo woipa. Mbuyeyo anati: “Unayenera kukasungitsa ndalama zanga zasilivazo kwa osunga ndalama, ndipo ine pobwera ndikanalandira ndalama zangazo limodzi ndi chiwongoladzanja chake.”​—Mateyo 25:27.

M’nthawi ya Yesu kunalibe mabanki ngati a masiku ano. Komabe kunali anthu osunga ndalama amene ankapereka chiwongoladzanja kwa anthu amene asungitsa ndalama kwa iwo. Ndiyeno osunga ndalamawo ankabwereketsanso ndalamazo kwa anthu ena pa chiwongoladzanja chachikulu. Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limanena kuti pofika zaka za m’ma 300 B.C.E., anthu ambiri ku Greece ankabwereketsa ndalama pa chiwongoladzanja. (The Anchor Bible Dictionary) Ndipo m’nthawi ya mtendere wa Aroma, anthu obwereketsa ndalama ankafuna kuti munthu podzabweza apereke makobili 4 kapena 6 pa 100 alionse amene anabwereka.

Chilamulo cha Mose chinkaletsa Aisiraeli kubwereketsa ndalama pa chiwongoladzanja kwa Aisiraeli anzawo osauka. (Eksodo 22:25) Zikuoneka kuti lamulo limeneli linkagwira ntchito makamaka pokongoza ndalama anthu osauka. Komabe fanizo la Yesu likutithandiza kuona kuti nthawi zonse munthu akakongola ndalama kwa osunga ndalama, omwe anali ngati mabanki a nthawi imeneyi, ankayenera kupereka chiwongoladzanja. Motero, monga mwa nthawi zonse, Yesu m’fanizoli anagwiritsa ntchito chinthu chodziwika bwino kwa omvera ake.