Mlengi Amene Tiyenera Kumutamanda
Yandikirani Mulungu
Mlengi Amene Tiyenera Kumutamanda
KODI munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘Kodi cholinga chamoyo n’chiyani?’ Anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusinthika kuchokera ku zinthu zina, sangapeze yankho la funso limeneli. Koma izi sizili choncho kwa anthu amene amakhulupirira mfundo yoona yakuti Yehova Mulungu ndi amene analenga zamoyo zonse. (Salmo 36:9) Iwo amadziwa kuti Mulungu anali ndi cholinga potilenga. Ndipo cholinga chimenechi chinalembedwa pa Chivumbulutso 4:11. Tiyeni tione mmene mawu olembedwa ndi mtumwi Yohane amenewa amafotokozera chifukwa chake Mulungu anatilenga.
Yohane analemba za nyimbo yotamanda Mulungu yomwe inaimbidwa kumwamba yakuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu, kulandira ulemerero, ndi ulemu, ndi mphamvu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo chifukwa cha chifuniro chanu, zinakhalapo, inde zinalengedwa.” Yehova yekha ndi amene ali woyenera kupatsidwa ulemu umenewu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa ‘analenga zinthu zonse.’ Ndiyeno, kodi zimenezi ziyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?
Baibulo limafotokoza kuti Yehova ayenera “kulandira” ulemerero, ulemu ndi mphamvu. N’zosakayikitsa kuti iye ndi munthu waulemerero ndiponso wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse. Komabe anthu ambiri savomereza kuti iye ndi amene analenga zinthu zonse. Ngakhale zili choncho, pali anthu ena amene amadziwa “makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso” akamaona zinthu zimene iye analenga. (Aroma 1:20) Ndipo pofuna kuyamikira zimenezi, iwo amapereka ulemu waukulu kwa Yehova. Iwo amalengeza kwa anthu onse amene angamvetsere umboni wokhutiritsa wakuti Yehova ndi amene analenga zinthu zonse ndiponso kuti tiyenera kum’patsa ulemu waukulu.—Salmo 19:1, 2; 139:14.
Kodi Yehova amalandira motani mphamvu kuchokera kwa olambira ake? N’zoona kuti palibe cholengedwa chimene chingamupatse mphamvu Mlengi wamphamvuyonse. (Yesaya 40:25, 26) Komabe popeza tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, tili ndi makhalidwe ake ena ndipo limodzi mwa makhalidwe amenewa ndi mphamvu. (Genesis 1:27) Ngati timayamikiradi zimene Mlengi wathu watichitira, tidzagwiritsa ntchito mphamvu zathu pomulemekeza. Ndipo m’malo mogwiritsa ntchito mphamvu zathu pa zofuna zathu zokha, tiyenera kum’tumikira Yehova Mulungu ndi mphamvu zathu zonse.—Maliko 12:30.
Komano, n’chifukwa chiyani iye anatilenga? Mbali yomaliza ya Chivumbulutso 4:11 imayankha kuti: “Chifukwa cha chifuniro chanu, [zinthu zonse] zinakhalapo, inde zinalengedwa.” Sitinalengedwe mwa kufuna kwathu. Tinalengedwa mwa chifuniro cha Mulungu. Motero, ngati munthu amangochita zofuna zake ndiye kuti moyo wake ulibe cholinga. Kuti tikhale ndi mtendere wamumtima komanso kuti tikhale osangalala, tiyenera kudziwa chifuniro cha Mulungu ndiyeno n’kumachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chakecho. Tikatero m’pamene tingadziwe cholinga chamoyo wathu.—Salmo 40:8.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
NASA, ESA, and A. Nota (STScI)