Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

N’chifukwa Chiyani Davide Sanachite Mantha?

N’chifukwa Chiyani Davide Sanachite Mantha?

KODI nthawi zina umachita mantha?​— * Tonsefe timachita mantha. Kodi ungatani ngati ukuchita mantha?​— Ungathe kuthawira kwa munthu wina wamkulu komanso wa mphamvu kuposa iweyo, mwina mayi ako kapena bambo ako. Tingaphunzirenso zambiri kwa Davide za kumene tingathawire. Poimba nyimbo yotamanda Mulungu iye anati: “Ndidzakhulupirira inu. . . . Ndakhulupirira Mulungu, sindidzawopa.”​—Salmo 56:3, 4.

Kodi ukuganiza kuti Davide anatengera ndani kulimba mtima?​— N’zosakayikitsa kuti iye anatengera kulimba mtima kwa makolo ake. Bambo ake, dzina lawo anali Jese. Iwo anali munthu wokhulupirika kwambiri ndipo anadzakhala mmodzi wa makolo a Yesu Khristu. Yesu ndi amene anali “Kalonga wa Mtendere” amene Mulungu analonjeza kuti adzabwera. (Yesaya 9:6; 11:1-3, 10) Bambo a Jese, anali Obedi ndipo iwowa anali agogo ake a Davide. M’Baibulo muli buku lina limene limadziwika ndi dzina la mayi ake a Obedi. Kodi umadziwa kuti mayi ake a Obedi anali ndani?​— Anali Rute. Iwowa anali mkazi wokhulupirika kwambiri ndipo amuna awo anali Boazi.​—Rute 4:21, 22.

Komabe mmene Davide ankabadwa n’kuti Rute ndi Boazi atafa kalekale. Mwinanso iweyo ukudziwa dzina la mayi ake a Boazi, omwe anali agogo a agogo ake a Davide. Mayiwa ankakhala mu mzinda wa Yeriko ndipo anathandiza Aisiraeli amene analowa mumzindawo kuti akafufuze zinthu mwachinsinsi. Mpanda wa Yeriko utagwa, iyeyu ndi abale ake anapulumuka chifukwa anakoleka kansalu kofiira pa windo. Kodi dzina lake anali ndani?​— Anali Rahabi. Iye anayamba kulambira Yehova, ndipo Akhristu amalimbikitsidwa kutengera kulimba mtima kwake.​—Yoswa 2:1-21; 6:22-25; Aheberi 11:30, 31.

Sitingakayikire kuti bambo ndi mayi a Davide anam’phunzitsa mwana wawoyo zonse zokhudza atumiki a Yehova okhulupirikawa, chifukwa makolo anapatsidwa lamulo lakuti aziphunzitsa ana awo zinthu ngati zimenezi. (Deuteronomo 6:4-9) Panthawi ina Mulungu anatuma mneneri Samueli kuti akasankhe Davide, mwana wamwamuna womaliza wa Jese, kuti adzakhale mfumu ya dziko la Isiraeli.​—1 Samueli 16:4-13.

Tsiku lina Jese anatumiza Davide kuti akapereke chakudya kwa achimwene ake atatu amene anali ku nkhondo yomenyana ndi Afilisti, omwe anali adani a Mulungu. Davide atafika anathamangira kumene kunali kuchitikira nkhondoyo ndipo anamva chimphona chotchedwa Goliati chikunyoza “makamu a Mulungu wamoyo.” Aliyense anachita mantha kukamenyana ndi Goliati. Koma Davide sanachite mantha. Mfumu Sauli itamva zoti Davide walolera kukamenyana ndi Goliati, inamuitanitsa. Ndipo Sauli ataona Davideyo, ananena kuti: “Iwe ndiwe mnyamata,” kapena kuti ndiwe mwana.

Davide anam’fotokozera Sauli kuti iyeyo nthawi ina anaphapo mkango ndiponso chimbalangondo chimene chinkafuna kupha nkhosa zawo. Kenaka Davide anati: Goliati “adzakhala ngati mmodzi wa izo.” Sauli anam’yankha kuti: ‘Pita, ndipo Yehova akhale nawe.’ Davide anatola miyala isanu yosalala ndipo anaiika m’kathumba. Kenako anatenga choponyera miyala kuti akamenyane ndi Goliati. Ataona Davide, yemwe amaoneka kuti ndi kamwana, Goliati anakuwa, amvekere: “Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga.” Koma Davide anamuyankha kuti: “Ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova. . . . Ndidzakukantha.”

Atangonena zimenezi, Davide anathamangira Goliati, n’kutulutsa mwala m’kathumba kaja ndipo anauika pa choponyera miyala, n’kumugenda nawo mwamphamvu pamphumi. Afilisti ataona kuti chimphona chija chafa, anachita mantha n’kuyamba kuthawa. Aisiraeli anawathamangitsa ndipo anapambana pankhondoyo. Werengani pamodzi ndi banja lanu nkhani yonseyi pa 1 Samueli 17:12-54.

Poti ndiwe mwana, nthawi zina mwina ungachite mantha kutsatira malamulo a Mulungu. Mwachitsanzo, Yeremiya anali wang’ono ndipo poyamba anachita mantha, koma Mulungu anamuuza kuti: “Usaope . . . chifukwa ine ndili ndi iwe.” Yeremiya analimba mtima ndipo analalikira mmene Mulungu anamuuzira. Mofanana ndi Davide ndiponso Yeremiya, ukamakhulupirira Yehova, iwenso ungathetse mantha.​—Yeremiya 1:6-8.

^ ndime 3 Ngati mukuwerengera ana nkhaniyi, kamzereko n’kokuuzani kuti muime kuti anawo ayankhe funsolo.