Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ukhondo Uli Wofunika?

N’chifukwa Chiyani Ukhondo Uli Wofunika?

N’chifukwa Chiyani Ukhondo Uli Wofunika?

Anthu akhala akuvutika ndi matenda ndiponso miliri kwa zaka zambiri. Anthu ena amaganiza kuti chimenechi ndi chizindikiro chakuti Mulungu wakwiya ndipo akuwalanga chifukwa cha zoipa zawo. Koma patapita zaka zambiri, khama komanso nzeru za ofufuza zathandiza kudziwa kuti chimene chimayambitsa matenda ndicho tizilombo tofalitsa matenda timene timakhala m’nyumba zathu.

Akatswiri ofufuza anazindikira kuti makoswe, mbewa, mphemvu, ntchentche ndi udzudzu ndi zimene zimayambitsa matenda. Anapezanso kuti uve umachititsa anthu kuti azidwala. Zikuoneka kuti ukhondo ungapangitse anthu kukhala ndi moyo wautali.

Ukhondo umasiyanasiyana malinga ndi malo ndiponso chikhalidwe cha anthu. M’madera amene mulibe mitsinje kapena zimbudzi zabwino, ukhondo umavuta. Komabe, Mulungu anapatsa Aisiraeli malangizo okhudza ukhondo paulendo wawo wa m’chipululu, ngakhale kuti zinali zovuta chifukwa chakuti analibe zinthu zokwanira zowathandiza kuti akhale aukhondo.

N’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti tikhale aukhondo? Nanga tingasonyeze bwanji ukhondo? Kodi mungachite zinthu zotani kuti inuyo ndi banja lanu musamadwaledwale?

MAX, * yemwe amakhala ku Cameroon, waweruka kusukulu ndipo wafika panyumba. Ali ndi njala komanso ludzu ndipo akulowa m’nyumba, kusisita galu wake, kuponya chikwama chake pa tebulo, kukhala pansi ndipo akudikirira chakudya.

Mayi ake, omwe panthawiyi ali kukhitchini, adziwa kuti Max wafika ndipo akubweretsa mbale ya mpunga ndi nyemba kuti iye adye. Koma nkhope ya mayiwo ikusintha ataona chikwama cha mwana wawo chili patebulo pomwe iwo anakonzapo bwino. Iwo akumuyang’anitsitsa Max ndi kunena kuti, “Koma iwe Max!” Mwana wawoyo wazindikira zimene mayiwo akutanthauza ndipo akuchotsa chikwamacho, n’kuthamanga kukasamba m’manja. Posakhalitsa akulowanso m’nyumbamo kuti adye chakudya chomwe wakhala akuchiyembekezera. Akupepesa mayi akewo kuti: “Amayi, pepani ndinaiwala.”

Mayi wachikondi amayesetsa kuti banja lake likhale ndi moyo wabwino ndiponso waukhondo. Koma kuti zimenezi zitheke, pamafunika kuti anthu ena pabanjapo amuthandize. Monga mmene nkhani ya Max yasonyezera, zimatenga nthawi yaitali kuti munthu aphunzire ukhondo chifukwa ukhondo umafuna khama komanso ana amafunika kuwakumbutsa nthawi ndi nthawi kuti azikhala aukhondo.

Mayi a Max amadziwa kuti chakudya chingalowe tizilombo toyambitsa matenda m’njira zosiyanasiyana. Choncho, iwo samangosamba m’manja basi, komanso amavindikira chakudyacho kuti ntchentche zisaterepo. M’nyumba mwawo mulibe makoswe ndi mphemvu chifukwa chakuti amavindikira chakudya chawo ndiponso amasesa.

Chifukwa chachikulu chimene chimachititsa mayi a Max kuti akhale aukhondo ndicho kufuna kusangalatsa Mulungu. Iwo anati: “Baibulo limati anthu a Mulungu ayenera kukhala oyera chifukwa Mulunguyo ndi woyera.” (1 Petulo 1:16) Iwo anatinso: “Anthu aukhondo nthawi zambiri amakhalanso oyera. Choncho ndimafuna kuti nyumba yanga ikhale yaukhondo ndipo ndimafunanso kuti anthu a m’banja langa akhale aukhondo. Koma zimenezi zimatheka chifukwa anthu onse m’banja lathu amandithandiza.”

Mgwirizano Pabanja Ndi Wofunika Kwambiri

Malinga ndi zimene mayi a Max ananena, kuti banja likhale laukhondo pamafunika kugwirizana. Nthawi ndi nthawi, mabanja amafunika kukhala pansi kuti akambirane zimene akufunikira komanso zimene angachite kuti nyumba yawo izioneka bwino, mkati ndi kunja komwe. Zimenezi zimathandizanso kuti banjalo likhale logwirizana komanso aliyense amakumbukira kuti ali ndi udindo wosamalira banjalo. Mwachitsanzo, mayi angauze ana ake aakulu ubwino wosamba m’manja akachoka kuchimbudzi, akagwira ndalama kapena asanadye. Anawonso angaonetsetse kuti ang’ono awo akuchitanso zimenezi.

Anthu pabanja angagawane ntchito zosiyanasiyana. Banja lingakonze zoti liziyeretsa nyumbayo Mulungu uliwonse ndiponso kuti kamodzi kapena kawiri pachaka lizikhala ndi ntchito yoyeretsa paliponse m’nyumbamo. Nanga bwanji panja pa nyumbayo? Ponena za ku United States, katswiri wina woteteza zachilengedwe, dzina lake Stewart L. Udall, anati: “Tikukhala m’dziko limene kukongola kwake kukutha, likuwonjezereka kuipa, malo akuchepa, ndipo zachilengedwe zikuonongeka tsiku ndi tsiku chifukwa cha zinthu zowononga malo ndiponso phokoso ndi zinthu zina zoipa.”

Kodi ndi mmenenso zilili m’dera lanu? Kale pankakhala munthu amene ankaliza belu mumsewu pofuna kulengeza zinthu. Zimenezi zimachitikanso ngakhale masiku ano m’matauni ena a ku Central Africa. Munthuyo amalengeza mokuwa pouza anthu kuti azisamala mzindawo, azichotsa zonyansa komanso zinyalala m’ngalande, kudulira mitengo, ndiponso azitchetcha udzu.

M’mayiko ambiri zinyalala zimangopezeka paliponse ndipo oyang’anira mizinda m’mayikowa akuda nkhawa ndi zimenezi. M’misewu yambiri mumakhala zinyalala mbwee, moti oyang’anira mizinda amalephera kuzichotsa mofulumira chifukwa cha kuchuluka. Anthu okhala m’deralo angaitanidwe kudzathandiza. Popeza Akhristu ndi nzika zabwino ndipo amamvera malamulo a boma, sazengereza akaitanidwa kukathandiza. (Aroma 13:3, 5-7) Akhristu oona amakhala okonzeka kuchita zoposa pamenepa. Iwo amasangalala kugwira ntchito yoyeretsa ndipo sachita kudikira kuti wina achite kulengeza. Akhristuwa amaona kuti ukhondo umasonyeza kuti munthu anaphunzitsidwa bwino ndiponso kuti ali ndi khalidwe labwino. Koma ukhondo umayambira panyumba. Anthu akamayesetsa kukhala aukhondo pakhomo pawo, sadwaladwala ndipo dera lonselo limaoneka bwino.

Tikakhala Aukhondo Timalemekeza Mulungu Amene Timam’lambira

Tikamaoneka aukhondo ndiponso tikavala modzilemekeza timasonyeza kuti timalambira Mulungu m’njira yoyenerera ndipo anthu amakopeka ndi kulambira kwathu. Tsiku lina achinyamata pafupifupi 15 analowa mu lesitilanti atamaliza msonkhano wawo wa Mboni za Yehova ku Toulouse, m’dziko la France. Chapafupi panali mwamuna ndi mkazi wake achikulire amene atangoona gululi anaganiza kuti pakhala chiphokoso kwambiri. Koma iwowa anagoma kwambiri kuona kuti achinyamata ovala bwinowa ankangocheza bwinobwino popanda chisokonezo. Moti achinyamatawo atangotsala pang’ono kuchoka, mwamuna ndi mkazi uja anawayamikira kwambiri chifukwa cha khalidwe limene anaonetsalo ndipo anauza mmodzi wa achinyamatawo kuti masiku ano n’zovuta kupeza achinyamata akhalidwe lotero.

Anthu ambiri amene amapita kukaona maofesi a nthambi, malo osindikizira mabuku, komanso nyumba zina za Mboni za Yehova, amagoma ndi ukhondo wa m’malo amenewa. Anthu onse odzipereka kugwira ntchito kumeneku amayenera kuvala zovala zoyera ndipo amafunikanso kuti azisamba nthawi zonse. Kungodzola mafuta kapena kudzifayira perefyumu sizokwanira kuti munthu akhale waukhondo. Anthu ogwira ntchito mongodziperekawa, omwe ndi atumiki a nthawi zonse, amalalikira madzulo kapena Loweruka ndi Lamlungu, ndipo maonekedwe awo aukhondo amagwirizana ndi uthenga umene amalalikirawo.

“Khalani Otsanzira Mulungu”

Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti “khalani otsanzira Mulungu.” (Aefeso 5:1) M’masomphenya amene mneneri Yesaya anaona, mngelo anafotokoza Mlengi kuti: “Woyera, Woyera, Woyera.” (Yesaya 6:3) Mawu amenewa amasonyeza kuti Mulungu ndi woyera ndiponso waukhondo mosayerekezereka. N’chifukwa chake amafunanso kuti atumiki ake azikhala oyera. Iye anati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”​—1 Petulo 1:16.

Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti ‘azivala modzilemekeza.’ (1 Timoteyo 2:9, The New English Bible) N’zosabwitsa kuti ponena za makhalidwe abwino a anthu amene Mulungu amawaona kuti ndi oyera, buku la Chivumbulutso limanena zoti ‘avala zonyezimira, ndi zofewa.’ (Chivumbulutso 19:8) Komano, nthawi zambiri Malemba amayerekezera uchimo ndi thotho kapena zoipa.​—Miyambo 15:26; Yesaya 1:16; Yakobe 1:27.

Masiku ano anthu ambiri amakhala m’madera amene n’zovuta kukhala munthu waukhondo, wamakhalidwe abwino ndiponso wokonda zinthu zoyera pamaso pa Mulungu. Amene adzathetseretu vutoli ndi Mulungu chifukwa ‘adzapanga zinthu zonse kukhala zatsopano.’ (Chivumbulutso 21:5) Lonjezo limenelo likadzakwaniritsidwa, uve wa mtundu wina uliwonse udzatheratu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Dzina talisintha.

[Bokosi patsamba 10]

Mulungu Amatilamula Kuti Tikhale Aukhondo

Paulendo wawo wam’chipululu Aisiraeli analangizidwa kuti azisamala kwambiri pankhani yotaya zonyansa. (Deuteronomo 23:12-14) Imeneyi iyenera kuti inali ntchito yovuta kwambiri, chifukwa choti msasawo unali waukulu, komabe inkathandiza kupewa matenda monga tayifodi ndiponso kolera.

Panali lamulo lakuti anthuwo azichapa kapena kutaya chilichonse chimene chinakhudzana ndi mtembo. Ngakhale kuti mwina Aisiraeli sanamvetse chifukwa chimene Mulungu anawauzira kuchita zimenezi, zinawathandiza kuti apewe matenda.​—Levitiko 11:32-38.

Ansembe ankayenera kusamba m’manja ndi m’miyendo asanayambe kugwira ntchito yawo kuchihema. Mulungu anawalamula kuti azisamba ngakhale kuti kudzadzitsa madzi m’beseni la mkuwa inali ntchito yaikulu ndithu.​—Eksodo 30:17-21.

[Bokosi patsamba 11]

Malangizo a Dokotala

Madzi ndi ofunika kwambiri pamoyo, koma madzi oipa angathe kudwalitsa anthu mwinanso matenda oti angathe kufa nawo. Akufunsidwa mafunso, Dr. J Mbangue Lobe, yemwe ndi mkulu wa dipatimenti yoona zachipatala pa doko la Douala, Cameroon, anatchulapo mfundo zina zothandiza.

Iye anati: “Ngati madzi anu akumwa ali okayikitsa, awiritseni.” Koma anachenjeza kuti: “Ngakhale kuti kugwiritsa ntchito mankhwala amphamvu ochapira kapena kutsukira zinthu n’kwabwino, dziwani kuti mankhwala oterewa ndi oopsa mukapanda kuwagwiritsa ntchito bwino. Nthawi zonse muzisamba m’manja musanadye chakudya ndiponso mukangochoka kuchimbudzi. Sopo si okwera mtengo kwambiri, moti ngakhale anthu osauka angathe kukwanitsa kugula sopo. Muzichapa zovala zanu kawirikawiri, ndipo muzigwiritsira ntchito madzi otentha ngati muli ndi mavuto enaake kapena matenda a pakhungu.”

Dokotalayo ananenanso kuti: “Anthu onse pakhomo ayenera kuchita zinthu mwaukhondo. Nthawi zambiri zimbudzi zokumba sizisamalidwa ayi moti kumadzazana mphemvu ndi ntchentche.” Ponena mfundo imodzi yokhudza ana, iye anachenjeza kuti: “Musamasambe m’timakhwawa tachabechabe. M’malo oterewa mumakhala tizilombo toopsa toyambitsa matenda. Nthawi zonse musanagone, muzisamba ndiponso kutsuka mkamwa, ndipo muzigona mu neti yokutetezani ku udzudzu.” Mfundo yaikulu pa mawu onsewa ndi yakuti tiyenera kuganizira zam’tsogolo, n’kuchitapo kanthu kuti tipewe mavuto.

[Chithunzi patsamba 10]

Kuchapa zovala kumakuthandizani kupewa mavuto ndiponso matenda

[Chithunzi patsamba 10]

Akhristu amaonetsetsa kuti malo amene akukhala ndi aukhondo

[Chithunzi patsamba 10]

Mayi wosamala banja lake amayesetsa kuti pakhomo pakhale paukhondo