Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsiku Limene Anasiya Karate

Tsiku Limene Anasiya Karate

Kalata Yochokera ku Ghana

Tsiku Limene Anasiya Karate

SINDINKAGANIZA kuti ndi mmene munthu wake alili. Anali atavala mkanjo wake woyera, m’chiuno mwake atamangamo lamba wakuda wamkulu masentimita asanu. Anaima mokonzekera ndewu, atakunga manja ake. Sanavale nsapato ndipo anaima motang’adza. Nkhope yake inali yoopsa, pamphumi pake panali matsinya ndipo maso ake anali olowa mkati. Iye ankaoneka kuti sangachitire chifundo munthu.

Iye anayamba kuyenda, ndipo mwadzidzidzi anafuula kuti “Hiya!” Kenako anaponya mkono wake m’mwamba kuti vuu! Thabwa kuti thyo! n’kugwera pansi. Anachitanso kapidigoli, tsopano anadumphira m’mwamba kwambiri uku akuponya manja ndi miyendo yake molunjika bwino n’kumenya mdani wake modzidzimutsa. Ndinadzifunsa kuti, kodi munthu ameneyu ndi amenedi anapempha kuphunzira Baibulo?

Ndinamuyandikira nditatambasula dzanja langa kuti ndim’patse moni. “Uyenera kuti ndiwe Kojo, eti? Ndamva kuti ukufuna kuphunzira Baibulo.” Anandigwira chanza uku akumwetulira kwambiri ndipo nkhope yake inaoneka yaubwenzi ndi yansangala. Maso ake sanalinso oopsa, koma anali kuoneka kuti ali ndi chidwi. Iye anayankha kuti: “Ee ndinedi, ndipo ndikufuna kwambiri kuphunzira. Tiyamba liti?”

Tinatenga Mabaibulo ndi mabuku athu n’kukhala pa kakhonde ka nyumba yake. Malo ake anali ozizira bwino, a phee, komanso tikanatha kuphunzira popanda wotisokoneza. Tinalipo atatu: Ineyo, Kojo, ndi kanyani kake. Kanyaniko kanali kakatali masentimita 35, kanali ndi tsumba lofiira ndi tindevu toyera motero kuti kamaoneka koseketsa komanso kofuntha. Kanali kosangalatsa, kokonda kusewera, ndiponso kachidwi ndi zinthu moti kankangoyendayenda. Kanyaniko kanali kuyenda pa mapepala athu, kutilanda zolembera, kutipisa m’matumba a malaya poyesa kuti kapezamo chinthu choti kadye. Mofanana ndi kholo lozolowera phokoso ndi kutakataka kwa ana, Kojo sanasamale zochita za kanyaniko. Iye chidwi chake chinali pa zimene tinkaphunzira. Anali kufunsa mafunso ambiri, zomwe zinasonyeza kuti ankaganiza komanso kuti anali wofunitsitsa kuphunzira. Mwina karate inamuchititsa kukhala watcheru ndi wosamala, chifukwa sanali kungovomereza zinthu popanda umboni wa m’Malemba.

Phunziro lathu linali kuyenda bwino. Komano, n’kupita kwanthawi ndinaona kuti akulimbananso ndi chinachake. Iye anandiuza kuti: “Chomwe ndimakonda kwambiri pamoyo wanga ndi karate basi.” Ndinatha kuona kuti mtima wake wonse unali pa kumenyana, anadzipereka kwambiri pophunzira masewera amenewa. Moti pofika zaka 26 zakubadwa, sanali kungoikonda chabe karate koma anali kuidziwa bwino kwambiri. Mpaka anafika popatsidwa lamba wakuda amene amasonyeza kuti munthuyo ndi katswiri wa masewerawa. Ndipo ndi anthu ochepa okha amene amafika pamenepa.

Sindinadziwe kuti Kojo adzatani. Koma ndinaona kuti iye wazindikira zoti kukhala munthu wa karate, n’kumavulaza ena ndi manja komanso miyendo yake, ndi kosagwirizana ndi chifundo, kukoma mtima, ndi kuganizira ena, makhalidwe amene Akhristu oona amakhala nawo chifukwa cha chikondi. Koma ndinali kudziwa kuti choonadi cha m’Baibulo chinasintha anthu ouma mitima kuposa iyeyo. Ndinkaganiza kuti ngati Kojo nayenso mtima wake unali wabwino, mphamvu ya Mawu a Mulungu idzamuthandiza kusintha mwapang’onopang’ono. Choncho ndinayenera kuleza mtima.

Tsiku lina masana kukutentha, tili pafupi kumaliza phunziro lathu, tinawerenga lemba lina m’Baibulo lomwe linamukhudza kwambiri Kojo moti anangokhala ngati kuti mdani wake wamumenya mwamphamvu. Iye anawerenga kuti: “Yehova ayesa wolungama mtima: koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Kenako ndinamumva akubwereza chapansipansi kuti, “Iye wakukonda chiwawa.” Maso ake ofiirira, omwe kale anali kuoneka oopsa ndi opanda chifundo, anayamba kusintha. Anandiyang’anitsitsa n’kuyamba kumwetulira, kenako anati: “Basi tsopano ndadziwa zochita.”

Tsopano ine ndi Kojo timagwira ntchito imene timaikonda kwambiri. Ndife aphunzitsi odzifunira, timaphunzitsa Baibulo kwaulere anthu amene amafuna kumvetsera. Tsiku lina m’mawa tinafunika kukaonana ndi mnyamata wina dzina lake Luke.

Popita ku nyumba yake tinadzera kamsewu kodutsa mu msika kamene munkapita anthu ambiri. M’mbali mwa timisewu ta mumsikawo munali mabenchi a malonda komanso anthu ogulitsa zinthu zosiyanasiyana monga: tsabola wakupsa ndi wosapsa yemwe, tomato, therere lobala, mawailesi, maambulera, sopo, mawigi, ziwiya zophikira, komanso nsapato ndi zovala za kaunjika. Atsikana anali kugulitsa zakudya zothira bwino tsabola zomwe anatengera m’mbale zikuluzikulu zachitsulo zimene anadendekera pamitu yawo. Iwo anali kudutsa m’chigulu cha anthu mwaluso kwambiri potsatsa malonda awo, moti ankachititsa anthu anjala kufuna kugula nsomba zowamba, nkhanu ndi nkhono zophikidwa bwino zomwe anali kugulitsazo. Agalu, mbuzi ndi nkhuku zinali paliponse. Mumsikamo munali phokoso la mawailesi, mahutala a magalimoto, komanso la anthu.

Kuchokera pa msikapo tinatenga nsewu wafumbi ndipo tinafika pa nyumba inayake yakalekale yomwe inali ndi chikwangwani chosaoneka bwino cholembedwa kuti: “Malo Opumirapo Apaulendo.” Luke, mnyamata wa zaka za m’ma 20, anaima pakhomo n’kutiuza kuti tilowe tikhale mu mthunzi. M’nyumbamo munali modzaza matumba ndi mabokosi a mizu youma, mipukutu ya masamba, ndiponso makungwa ambirimbiri. Zonsezi zinali za achemwali awo a amayi ake omwe anali kuchita zausing’anga. Iwo anali achikulire ndipo amadziwa kusakaniza bwino mankhwala a zitsamba monga mmene mibadwo ya m’mbuyomo inali kuchitira. Anali kusinja ndi kuwiritsa mankhwalawo n’kumapatsa anthu odwala matenda osiyanasiyana. Luke anakonzekera zoti tikubwera. Anasunthira zinthuzo mbali imodzi n’kupeza malo oikapo timipando titatu. Tinakhala moyandikana kwambiri ndi kuyamba kuphunzira Baibulo.

Kojo ndiye anali kuphunzitsa Luke. Ndipo ine ndinangokhala n’kumamvetsera pamene anyamata awiriwo anali kukambirana mayankho a m’Baibulo ofotokoza chifukwa chake padzikoli pali mavuto ambiri. Kenako ndinaona Kojo akuthandiza Luke kupeza lemba lina m’Baibulo, ndipo ndinachita chidwi kuona manja ake amphamvu akuvundukula mosamala bwino mapepala opyapyala a m’Baibulo mpaka kupeza lembalo. Ndiyeno ndinakumbukira kuti si kale kwambiri pamene iye anali kugwiritsa ntchito manjawo kumenyera anthu. Mphamvu ya Mawu a Mulungu imatha kusintha anthu amene ali ndi makhalidwe oipa ovuta kuwasiya omwe afala kwambiri m’dzikoli, n’kuwachititsa kukhala ndi makhalidwe abwino monga chifundo ndi chikondi. Izi ndi zofunika kwambiri kuposa china chilichonse.

Pobwerera ku nyumba, tinalankhula ndi bambo wina amene anakhala pa mthunzi wa mtengo wamango. Bamboyo anangokhala chete n’kumamvetsera pamene Kojo anatsegula Baibulo ndi kuwerenga lemba. Koma atazindikira kuti ndife Mboni za Yehova, anaimirira n’kunena mokalipa kuti: “Anthu inu sindikufunani!” Kojo anaipidwa nazo, koma patapita kanthawi kochepa mtima wake unabwerera m’malo, ndipo anachokapo mwaulemu. Kenako tinapitiriza ulendo wathu.

Tikuyenda Kojo anandinong’oneza kuti: “Atangonena zimene zija, mtima wanga unagunda kwambiri. Kodi ukudziwa zimene ndikanamuchita bambo amene uja?” “Ee ndikudziwa,” ndinamuyankha ndikumwetulira. Nayenso anangomwetulira, basi ulendo n’kumapitirira.