Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaopa Akufa?

Kodi Mumaopa Akufa?

Kodi Mumaopa Akufa?

ANTHU ambiri amayankha funso limeneli kuti, “Ayi, palibe chifukwa choopera anthu akufa.” Iwo amakhulupirira kuti munthu akafa wafa basi. Komabe, anthu ena amakhulupirira kuti munthu akafa, amakhalabe ndi moyo kwinakwake ngati mzimu.

Anthu ambiri m’dziko la Benin, ku West Africa, amakhulupirira kuti anthu akufa angaphe achibale awo. Pachifukwa chimenechi, anthu amagulitsa katundu kapena kulowa m’ngongole kuti apeze ndalama zogulira nyama zoti apereke nsembe kapena achitire miyambo yokondweretsa achibale awo amene anamwalira. Anthu ena okhulupirira zamizimu amanena kuti munthu akamwalira mzimu wake umakakhala kwinakwake ndipo umatha kulankhulana ndi anthu amoyo. Ndipo ena akumana ndi zinthu zoopsa zimene amati zinachitika chifukwa cha mizimu ya anthu akufa.

Agboola yemwe amakhala pafupi ndi malire a Benin ndi Nigeria ndi mmodzi mwa anthu amene zinthu ngati zimenezi zinawachitikira. Iye anati: “Anthu ambiri m’dera lathu amakonda zamizimu. Iwo amachita mwambo wosambitsa maliro n’cholinga chakuti mtembowo ukhale woyenera kukakhala kumalo amizimu. Nthawi zambiri ndinkatenga sopo wosambitsira maliro ndi kumusakaniza ndi masamba enaake. Ndikatero, ndinkapaka zimenezi ku mfuti imene ndinkasakira nyama, uku ndikutchula mokweza nyama imene ndikufuna kuti ndikaphe. Miyambo ngati imeneyi ndi yofala kwambiri ndipo anthu ambiri amaona kuti imathandiza. Komabe, zochitika zambiri zokhudza mizimu n’zoopsa.

“Ana anga awiri atamwalira mosadziwika bwino, ndinaganiza kuti alodzedwa. Pofuna kudziwa kuti afa bwanji, ndinapita kwa mkulu wina wotchuka ndi zamizimu. Iye anavomereza kuti ana angawo anachitadi kulodzedwa. Chinandikhumudwitsa kwambiri n’chakuti, iye anandifotokozera kuti ana angawo ali kudziko lamizimu kudikirira kudzatumikira munthu amene anawaphayo akadzamwalira. Ndipo mkuluyu ananena kuti mwana wanga winanso amwalira. Patapita nthawi pang’ono, mwanayo anamwaliradi.”

Ndiyeno Agboola anakumana ndi John, yemwe ndi wa Mboni za Yehova wa ku Nigeria. Zimene John anafotokoza pankhani ya anthu akufa zinali zochokera m’Baibulo. Zimene anafotokozazo zinasintha moyo wa Agboola ndipo zingasinthenso moyo wanu.

Kodi Akufa Amakhalanso ndi Moyo Kwinakwake?

Kodi ndani angayankhe bwino funso limeneli? Anthu sangayankhe, ngakhale atakhala otchuka kwambiri. Koma amene angayankhe bwino funso limeneli ndi Yehova, amene analenga zamoyo zonse “za kumwamba ndi pa dziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka.” (Akolose 1:16) Iye analenga angelo kuti azikhala kumwamba koma analenga anthu ndi nyama kuti azikhala padziko lapansi. (Salmo 104:4, 23, 24) Ndipo zinthu zonse zimadalira iyeyo kuti zikhale ndi moyo. (Chivumbulutso 4:11) Ndiyeno taonani zimene Mawu a Mulungu, Baibulo, amanena pankhani ya anthu akufa.

Yehova ndi amene anayamba kutchula za imfa. Iye anachenjeza Adamu ndi Hava kuti adzafa ngati samumvera. (Genesis 2:17) Kodi zimenezi zinatanthauzanji? Yehova anati: “Ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Munthu akafa amaola ndipo amabwerera ku fumbi.

Adamu ndi Hava anafuna okha kusamvera Mulungu ndipo chifukwa cha zimenezi anafa. Koma amenewa si anthu oyamba kufa. Mwana wawo Abele ndi amene anali woyamba. Iye anaphedwa ndi mchimwene wake, Kaini. (Genesis 4:8) Kaini sankaopa kuti mng’ono wake amene anamuphayo adzabwezera. Koma iye ankaopa zimene anthu amoyo akanachita.​—Genesis 4:10-16.

Patapita zaka zambiri, Mfumu Herode anakwiya kwambiri, okhulupirira nyenyezi atamuuza kuti m’dera lake mwabadwa “mfumu ya Ayuda.” Herode anafuna kwambiri kupha mfumuyi, motero anakonza zopha ana onse aamuna mu Betelehemu azaka zosapitirira ziwiri. Koma mngelo anauza Yosefe kuti atenge Yesu ndi Mariya ndipo ‘athawire ku Aigupto.’​—Mateyo 2:1-16.

Herode atamwalira, mngelo anauza Yosefe kuti akhoza kubwerera ku Isiraeli, “chifukwa amene anali kufuna moyo wa mwana wamng’onoyu anafa.” (Mateyo 2:19, 20) Mngeloyo, yemwe ndi mzimu, ankadziwa kuti Herode sangavulazenso Yesu. Yosefe sanaope mfumu Herode amene anali atafa. Komabe, Yosefe ankaopa zimene Arikelao, mwana wankhanza wa Herode akanachita. Choncho, Yosefe anakakhala ndi banja lake ku Galileya, dera lina osati limene Arikelao ankalamulira.​—Mateyo 2:22.

Nkhani zimenezi zikutithandiza kuona kuti akufa alibe mphamvu. Nanga pankhani ya Agboola ndi zinthu zina zokhudza mizimu zimene anthu ena amakumana nazo, kodi chimachitika n’chiyani?

“Ziwanda,” Kapena Kuti Mizimu Yoipa

Yesu atakula anakumana ndi mizimu yoipa. Mizimu imeneyi inkamudziwa Yesu ndipo inkamutchula kuti “Mwana wa Mulungu.” Yesu nayenso ankaidziwa bwino ndipo ankadziwa kuti sinali mizimu ya anthu akufa. Ndipo iye ankaitchula kuti “ziwanda,” kapena kuti mizimu yoipa.​—Mateyo 8:29-31; 10:8; Maliko 5:8.

Baibulo limanena za mizimu yokhulupirika kwa Mulungu komanso imene inam’pandukira. Buku la Genesis limanena kuti Yehova atathamangitsa anthu osamverawo Adamu ndi Hava m’munda wa Edene, anaika akerubi, kapena kuti angelo, kum’mawa kwa mundawo kuti munthu wina aliyense asalowe. (Genesis 3:24) Imeneyi inali nthawi yoyamba anthu kuona zolengedwa zauzimu.

Patapita nthawi, angelo ena anavala matupi a anthu ndipo anabwera ku dziko lapansi. Yehova sanawatume kudzagwira ntchito ina iliyonse. Koma “anasiya malo awo okhala” kumalo a mizimu. (Yuda 6) Anali ndi zolinga zadyera. Iwo anakwatira akazi ndi kubala ana omwe anatchedwa Anefili, kapena kuti zimphona. Ana amenewa pamodzi ndi angelo opandukawo anadzaza dziko lapansi ndi chiwawa komanso zoipa zina. (Genesis 6:1-5) Yehova anakonza zinthu mwa kubweretsa Chigumula cha dziko lonse m’masiku a Nowa. Chigumulachi chinawononga amuna ndi akazi oipa pamodzi ndi zimphona. Nanga n’chiyani chinachitikira angelowo?

Ataona Chigumulachi anabwerera kumalo a mizimu. Koma Yehova sanawalole kuti akhale ku “malo awo oyambirira.” (Yuda 6) Baibulo limanena kuti: “Mulungu sanalekerere angelo amene anachimwa aja osawapatsa chilango, koma mwa kuwaponya mu Tatalasi, anawaika m’maenje a mdima wandiweyani, kuwasungira chiweruzo.”​—2 Petulo 2:4.

Tatalasi si malo enieni koma ndi moyo ngati wa kundende umene supatsa mizimu imeneyi mwayi wonse wochita zinthu. Ziwandazi sizingavalenso matupi a anthu komabe n’zamphamvu ndipo zimalamulira maganizo ndi moyo wa anthu. Zili ndi mphamvu pa anthu ndi nyama. (Mateyo 12:43-45; Luka 8:27-33) Zimanamizanso anthu mwakuyerekeza kukhala mizimu ya anthu akufa. Kodi n’chifukwa chiyani zimachita zimenezi? Zimafuna kuti anthu asamalambire Yehova m’njira imene iye amafuna komanso zimafuna kusokoneza anthu pankhani ya zimene zimachitika munthu akafa.

Zimene Mungachite Kuti Musamaope Ziwanda

Agboola anaona kuti zimene Baibulo limanena pankhani ya imfa ndiponso mizimu n’zomveka. Iye anazindikira kuti anafunika kuphunzira zochuluka. Choncho anayamba kuwerenga Baibulo ndi mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo amene John anali kum’patsa. Agboola analimbikitsidwa podziwa kuti ana ake anali m’tulo kumanda, osati kuti ali kumalo a mizimu kuyembekezera kukakhala akapolo a munthu amene anawapha uja.​—Yohane 11:11-13.

Agboola anazindikiranso kuti anafunika kusiyiratu kukhulupirira mizimu. Iye anawotcha katundu wake yense wokhudza zinthu zimenezi. (Machitidwe 19:19) Anthu ena m’deralo anamuopseza kuti kumeneku n’kuiputa dala mizimu, koma Agboola sanaope. Iye anatsatira malangizo opezeka pa Aefeso 6:11, 12 akuti: ‘Valani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu . . . chifukwa tikulimbana . . . ndi makamu a mizimu yoipa.’ Zida zankhondo zauzimu zimenezi ndi zinthu monga choonadi, chilungamo, uthenga wabwino wa mtendere, chikhulupiriro komanso lupanga la mzimu, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Zida zimenezi ndi zamphamvu ndipo zimachokera kwa Mulungu.

Anzake a Agboola limodzi ndi achibale ake ankamusala chifukwa chosiya miyambo ya mizimu. Koma anapeza mabwenzi ena ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, omwe amakhulupirira zimene Baibulo limaphunzitsa.

Tsopano Agboola akudziwa kuti posachedwapa Yehova achotsa zoipa ndipo adzaletsa ziwanda kuchita chilichonse. Ndipo pamapeto pake, iye adzaziwononga. (Chivumbulutso 20:1, 2, 10) Mulungu adzaukitsa “onse ali m’manda a chikumbutso” padziko lapansi pompano. (Yohane 5:28, 29) Anthu amenewa adzaphatikizapo Abele, ana osalakwa amene Mfumu Herode anapha, ndi anthu ena ambiri. Agboola akukhulupirira kuti ana ake atatu aja adzaukitsidwanso. Anthu amene mumawakonda amene anamwalira adzakhala m’gululi. Anthu onse amene adzaukitsidwewo adzanena okha kuti chimwalirireni kudzafika panthawi imene akuukitsidwa, samadziwa chilichonse ngakhale mwambo uliwonse umene unachitika chifukwa cha iwo.

Palibe chifukwa choopera akufa. Koma mungayembekezere kudzaonana ndi anthu amene mumawakonda omwe anamwalira. Bwanji osaphunzira Baibulo panopa kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu? Sonkhanani ndi anthu amene amakhulupirira zimene Baibulo limaphunzitsa. Ngati mumachita chinachake chokhudzana ndi mizimu, siyiranitu. Dzitetezeni ku ziwanda mwa kuvala “zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.” (Aefeso 6:11) Amboni za Yehova angasangalale kukuthandizani. Iwo amaphunzitsa Baibulo panyumba kwaulere pogwiritsa ntchito buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? *

Agboola saopanso akufa ndipo waphunzira zimene angachite kuti adziteteze ku ziwanda. Iye akuti: “Sindikudziwa amene anapha ana anga atatu aja. Koma kuchokera nthawi imene ndinayamba kutumikira Yehova ndakhala ndi ana ena 7. Ana amenewa sanavulazidwepo ndi aliyense wa kumalo a mizimu.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 25 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Agboola saopanso akufa ndipo waphunzira zimene angachite kuti adziteteze ku ziwanda

[Chithunzi patsamba 12]

Kaini sankaopa kuti mphwake amene anamuphayo adzabwezera