Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amasamala za Ine?

Kodi Mulungu Amasamala za Ine?

Kodi Mulungu Amasamala za Ine?

Ambiri amanena kuti:

▪ “Mulungu ndi wapamwamba kwambiri moti sangaganizire mavuto anga.”

▪ “Sindikukhulupirira kuti amasamala za ine.”

Kodi Yesu anati chiyani?

▪ “Mpheta zisanu amazigulitsa makobili awiri ochepa mphamvu, si choncho nanga? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imaiwalika kwa Mulungu. Ndipo ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu analiwerenga. Musachite mantha; ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” (Luka 12:6, 7) Ndithudi, Yesu ankaphunzitsa kuti Mulungu amatisamalira.

▪ “Musamade nkhawa n’kumati, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ Pakuti amitundu akufunafuna mwakhama zinthu zonse zimenezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti zinthu zonsezi inu mukuzisowa.” (Mateyo 6:31, 32) Yesu ankadziwa kuti Mulungu amadziwa zimene timafunika pamoyo wathu.

BAIBULO limanena mwachindunji kuti Mulungu amatisamalira. (Salmo 55:22; 1 Petulo 5:7) Komano n’chifukwa chiyani timavutika kwambiri masiku ano? Ngati Mulungu amatikonda komanso ndi wamphamvuyonse, n’chifukwa chiyani sakuthetsa mavutowa?

Yankho lake likukhudza mfundo imene anthu ambiri samaidziwa, yakuti Satana Mdyerekezi ndiye wolamulira wa dziko loipali. Pomuyesa Yesu, Satana anamuuza kuti amupatsa maufumu onse adzikoli. Iye anati: “Ndikupatsani ulamuliro wonsewu ndi ulemerero wake wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.”​—Luka 4:5-7.

Kodi ndani anamuika Satana kukhala wolamulira wa dzikoli? Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, atamvera Satana ndi kukana malamulo a Mulungu, anasonyeza kuti asankha Satana kukhala wolamulira wawo. Kuchokera panthawiyi, Yehova Mulungu walola kuti papite nthawi yosonyeza kuti ulamuliro wa Satana ndi wolephera. Yehova sakakamiza anthu kuti azimutumikira koma wapereka mwayi woti tibwerere kwa iye.​—Aroma 5:10.

Popeza Mulungu amatisamalira, wakonza zoti Yesu atipulumutse ku ulamuliro wa Satana. Posachedwapa, Yesu ‘awononga iye amene ali ndi njira yochititsa imfa, ndiye Mdyerekezi.’ (Aheberi 2:14) Mwakuchita zimenezi, iye ‘adzawononga ntchito za Mdyerekezi.’​—1 Yohane 3:8.

Paradaiso adzabwezeretsedwa padziko pano. Panthawi imeneyo, Mulungu “adzapukuta msozi uliwonse m’maso [mwa anthu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4, 5. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Kuti mumve zambiri pankhani ya chifukwa chake Mulungu walolera kuti tizivutika, onani buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? mutu 11.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Paradaiso adzabwezeretsedwa padziko pano