Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizigwiritsa Ntchito Mafano Polambira?

Kodi N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizigwiritsa Ntchito Mafano Polambira?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizigwiritsa Ntchito Mafano Polambira?

Padziko lonse lapansi Ahindu, Abuda, Akatolika, ndiponso a Tchalitchi cha Orthodox amaona kuti n’kofunika kwambiri kugwiritsa ntchito mafano kapena zithunzi polambira. Ndipo m’mayiko ena a ku Africa, anthu amalambira mitengo kapena miyala yosema imene amaganiza kuti mumakhala mulungu kapena mzimu wake.

Koma Mboni za Yehova sizigwiritsa ntchito mafano ndi zithunzi polambira. Mutafika kumene a Mboni za Yehova amasonkhana, kumene amati Nyumba ya Ufumu, simudzapezako ziboliboli za Yesu, Mariya kapena zithunzi za amene anthu ena amawati oyera mtima. * N’chifukwa chiyani? Onani zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi.

Kodi Mulungu Ankafuna Kuti Aisiraeli Azimulambira Bwanji?

Atamasula Aisiraeli mu ukapolo ku Igupto, Yehova Mulungu anawapatsa malangizo omveka bwino a zimene ankafuna kuti azichita pomulambira. Lamulo lachiwiri pa malamulo amene anthu amawati Malamulo Khumi limati: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje.”​—Eksodo 20:4, 5.

Nthawi imene Mulungu ankapereka malamulo amenewa kwa Mose, n’kuti Aisiraeli akupanga fano la mwana wa ng’ombe, potengera nyama zimene Aigupto ankagwiritsa ntchito polambira. Fanolo sanalipatse dzina la mulungu wa Aigupto. Iwo ankaligwiritsa ntchito polambira Yehova. (Eksodo 32:5, 6) Kodi Mulungu anaziona bwanji zimenezi? Mulungu anakwiya kwambiri ndi anthu amene ankalambira fanolo ndipo Mose analiwononga.​—Eksodo 32:9, 10, 19, 20.

Kenako, Yehova Mulungu anafotokozera lamulo lachiwiri lija. Kudzera mwa Mose, Iye anawakumbutsa Aisiraeli kuti asadzipangire “fano losema, lakunga chifaniziro chilichonse, mafanidwe a mwamuna kapena mkazi; mafanidwe a nyama iliyonse ili pa dziko lapansi, mafanidwe a mbalame iliyonse yamapiko yakuuluka m’mlengalenga, mafanidwe a chinthu chilichonse chokwawa pansi, mafanidwe a nsomba iliyonse yokhala m’madzi pansi pa dziko.” (Deuteronomo 4:15-18) Ndithudi, Aisiraeli sankafunika kugwiritsa ntchito mafano polambira Mulungu.

Komabe, patapita nthawi Aisiraeli anayamba kulambira mafano. Pofuna kuwathandiza kuti asinthe, Yehova anatumiza aneneri amene anawachenjeza kuti adzalangidwa chifukwa cha kulambira kwawo mafano. (Yeremiya 19:3-5; Amosi 2:8) Mtundu wonse wa Isiraeli sunatsatire zimene Mulungu anawachenjeza. Choncho, mu 607 B.C.E., Yehova analola Ababulo kuwononga Yerusalemu ndi kutenga Aisiraeli ku ukapolo.​—2 Mbiri 36:20, 21; Yeremiya 25:11, 12.

Kodi Akhristu Oyambirira Ankakhulupirira Chiyani?

M’nthawi ya Atumwi, anthu amene sanali Ayuda akayamba Chikhristu, ankasiya kugwiritsa ntchito mafano polambira Mulungu. Onani zimene Demetiriyo, wosula siliva wa ku Efeso, amene ankapanga mafano ananena atamva za ulaliki wa mtumwi Paulo. Iye anati: “Amuna inu, mukudziwa bwino lomwe kuti chuma chathu chimachokera m’ntchito imeneyi. Komanso mukuona ndipo mukumva za Paulo ameneyu, kuti si mu Efeso mokha mmene wakopa anthu ambirimbiri ndi kuwapatutsira ku chikhulupiriro china. Wachita zimenezi pafupifupi m’chigawo chonse cha Asiya. Akumanena kuti yopangidwa ndi manja si milungu ayi.”​—Machitidwe 19:25, 26.

Ndipo zimene Paulo ananena zimatsimikizira kuti Demetiriyo ankanena zoona. Pamene ankalankhula ndi Agiriki ku Atene, Paulo anati: “Tisaganize kuti Mulunguyo ali ngati golide kapena siliva kapena mwala, kapena chilichonse chosemedwa mwa luso ndi nzeru za munthu. Inde, Mulungu analekerera nthawi ya kusadziwa koteroko, koma tsopano akuuza anthu kwina kulikonse kuti onse alape.” (Machitidwe 17:29, 30) Pankhani yomweyi, Paulo analembera Akhristu a ku Tesalonika kuti: “Inu munatembenukira kwa Mulungu, kusiya mafano anu.”​—1 Atesalonika 1:9.

Mofanana ndi Paulo, mtumwi Yohane nayenso anachenjeza Akhristu kuti asamagwiritse ntchito mafano polambira. Kumapeto kwa nthawi ya atumwi, Yohane anawauza motsindika kuti: “Pewani mafano.”​—1 Yohane 5:21.

Mboni za Yehova zimamvera malangizo a Mulungu omveka bwino akuti tisamagwiritse ntchito mafano pomulambira. Iwo amatsatira zimene Yehova Mulungu ananena. Iye anati: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.”​—Yesaya 42:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Nyumba za Ufumu zina zili ndi zithunzi za anthu a m’Baibulo. Komabe, zithunzi zimenezi n’zongokongoletsera nyumbayo, ndipo sizimalambiridwa. Mboni za Yehova sizigwiritsa ntchito zithunzi zimenezi popemphera komanso samazigwadira.

[Mawu Otsindika patsamba 31]

“Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.”​—Yesaya 42:8