Mayina Atanthauzo
Mayina Atanthauzo
Mayi wina wa ku Ethiopia anabala mwana wa mwamuna. Koma kusangalala kwake kunatha ataona kuti mwanayo sakutakataka. Agogo a mwanayo atamunyamula kuti amusambitse, mwadzidzidzi mwanayo anayamba kutakataka, kupuma ndiponso kulira. Dzina la bambo ake a mwanayo linkatanthauza kuti “Chozizwitsa,” choncho makolo ake anatenga dzina limeneli n’kuliphatikiza ndi dzina lina la Chiamuhariki ndi kumupatsa mwanayo. Ndipo dzinalo linali lakuti Chozizwitsa Chachitika.
Ku Burundi, mnyamata wina amathawa asilikali amene ankafuna kumupha. Atabisala pathengo linalake, mnyamatayo anapemphera kwa Mulungu kuti ngati angam’pulumutse, adzam’patsa mwana wake woyamba dzina lakuti Manirakiza, kutanthauza kuti “Mulungu ndi Mpulumutsi.” Patatha zaka zisanu, anaperekadi dzina limeneli kwa mwana wake woyamba, poyamikira kuti ali ndi moyo.
KUPATSA ana mayina okhala ndi tanthauzo ndi kwachilendo kwa anthu ena, koma zimenezi zakhala zikuchitika kuyambira kalekale. Ndipotu, m’Baibulo muli mayina ambiri okhala ndi tanthauzo. Kudziwa matanthauzo a mayina a anthu ena kungatithandize kupindula kwambiri tikamawerenga Baibulo. Onani zitsanzo zingapo.
Mayina Atanthauzo a m’Malemba Achiheberi
Limodzi la mayina oyambirira kulembedwa m’Baibulo ndi la Seti, lotanthauza “Kupatsa.” Hava, amene ndi amayi ake a Seti, anafotokoza chifukwa chake anasankha dzina limeneli. Iwo anati: “Mulungu wandilowezera [kapena kuti wandipatsa] ine mbewu ina m’malo mwa Abele amene Kaini anamupha.” (Genesis 4:25) Lameki, amene ndi mbadwa ya Seti, anapatsa mwana wake dzina lakuti Nowa, kutanthauza “Mpumulo” kapena “Chitonthozo.” Lameki ananena kuti anapereka dzina limeneli kwa mwana wake chifukwa “adzatonthoza mtima wathu pa ntchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova.”—Genesis 5:29.
Mulungu anasinthanso mayina a anthu ena pofuna kulosera chinthu chinachake. Mwachitsanzo, anasintha dzina la Abulamu, lotanthauza “Atate Akwezeka” kukhala Abulahamu, kutanthauza kuti “Tate wa Khamu la Anthu.” Ndipo mogwirizana ndi dzina lake, Abulahamu anakhaladi tate wa mitundu yambiri. (Genesis 17:5, 6) Anachitanso zimenezi ndi mkazi wa Abulahamu, dzina lake Sarai, lomwe linkatanthauza “Wolongolola.” Iye ayenera kuti anasangalala kwambiri Mulungu atamusintha dzina kukhala Sara, kutanthauza kuti “Mfumukazi,” posonyeza kuti adzakhala kholo la mafumu.—Genesis 17:15, 16.
Mulungu anaperekanso mayina kwa ana ena. Mwachitsanzo, iye anauza Abulahamu ndi Sara kuti adzamutche mwana wawo kuti Isake, kutanthauza “Kuseka.” Nthawi zonse dzina limeneli linkakumbutsa banja lokhulupirikali momwe linachitira litauzidwa kuti lidzakhala ndi mwana panthawi yawo yaukalamba. Isake atakula n’kukhala mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, Genesis 17:17, 19; 18:12, 15; 21:6.
dzina lake liyenera kuti linapitirizabe kusangalatsa Abulahamu ndi Sara akamacheza ndi mwana wawo wokondedwa.—Rakele, mpongozi wake wa Isake, anapereka dzina kwa mwana wake womaliza pa chifukwa china. Atatsala pang’ono kumwalira, Rakele anatchula mwana wake kuti Ben-oni, kutanthauza kuti “Mwana wa kulira kwanga.” Mwamuna wake, Yakobo, anadzasintha pang’ono dzinali kukhala Benjamini, kutanthauza kuti “Mwana wa ku Dzanja la Manja.” Dzina limeneli linkasonyeza kuti ndi wokondedwa ndiponso wothandiza.—Genesis 35:16-19; 44:20.
Nthawi zina munthu ankapatsidwa dzina malinga ndi maonekedwe ake. Mwachitsanzo, Isake ndi Rabeka anali ndi mwana yemwe anabadwa ndi tsitsi lofiira. Tsitsi limeneli linali lambiri moti amaoneka ngati wavala malaya aubweya, n’chifukwa chake anamutcha kuti Esau. Dzina limeneli m’chiheberi limatanthauza “Waubweya.” (Genesis 25:25) Buku la Rute limasonyeza kuti Naomi anali ndi ana aamuna awiri. Mmodzi anamupatsa dzina lakuti Maloni, lotanthauza kuti “Wodwaladwala” ndipo wina anamutcha kuti Kilioni, kutanthauza kuti “Wonyozoloka.” Sizikudziwika ngati anapatsidwa mayina amenewa atangobadwa kapena panthawi ina, komabe anali oyenera chifukwa ana onsewa anamwalira ali achinyamata.—Rute 1:5.
Chinanso chimene anthu ambiri ankachita chinali kusintha mayina. Pobwerera ku Betelehemu, atasauka kwambiri chifukwa cha imfa ya mwamuna wake ndiponso ana ake, Naomi sanafune kuti anthu azimutchulabe dzina lake loyamba lotanthauza “Chisangalalo changa.” Koma iye anati: “Musanditcha Naomi, munditche Mara [kutanthauza “Zowawa”]; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.”—Rute 1:20, 21.
Anthu ankakondanso kupatsa ana awo mayina amene angawathandize kukumbukira mwambo winawake wapadera. Mwachitsanzo, dzina la mneneri Hagai limatanthauza kuti “Wobadwa Tsiku la Chikondwerero.” *
Mayina Atanthauzo mu Nthawi ya Atumwi
Dzina la Yesu lili ndi tanthauzo logwirizana ndi udindo wake wam’tsogolo. Iye asanabadwe, makolo ake analangizidwa ndi Mulungu kuti: “Dzina lake udzamutche Yesu,” kutanthauza kuti “Yehova ndi Mpulumutsi.” N’chifukwa chiyani anapatsidwa dzina limeneli? Mngelo amene analankhula ndi Yosefe anati: “Adzapulumutsa anthu ake ku machimo Mateyo 1:21) Yesu atadzozedwa ndi mzimu paubatizo wake, dzina lake linaphatikizidwa ndi dzina lina lachiheberi lakuti “Mesiya.” M’chigiriki dzina limeneli amati “Khristu.” Ndipo mayina onsewa amatanthauza kuti “Wodzozedwa.”—Mateyo 2:4.
awo.” (Yesu nayenso anapatsa ophunzira ake ena mayina ofotokoza makhalidwe awo. Mwachitsanzo, Simoni anamupatsa dzina lachisemitiki lakuti Kefa, kutanthauza “Thanthwe.” Kefa ankadziwika kwambiri ndi dzina lakuti “Petulo,” limene ndi dzina lomweli m’chigiriki. (Yohane 1:42) Yesu anatchula abale achangu, Yakobe ndi Yohane, kuti “Boanege,” kutanthauza kuti “Ana a Bingu.”—Maliko 3:16, 17.
Ophunzira a Yesu anapitirizabe kupatsa anthu mayina malinga ndi khalidwe lawo. Chitsanzo chimodzi ndi wophunzira Yosefe amene atumwi anamutcha kuti Barnaba, kutanthauza kuti “Mwana wa Chitonthozo.” Mogwirizana ndi dzina lake, Barnaba ankatonthoza anthu ambiri mwauzimu ndiponso mwanjira zina.—Machitidwe 4:34-37; 9:27; 15:25, 26.
Kufunika Kokhala ndi Mbiri Yabwino
Sitingasankhe tokha dzina limene timapatsidwa pobadwa. Komabe, timapanga tokha mbiri imene timakhala nayo. (Miyambo 20:11) Bwanji osadzifunsa kuti: ‘Ngati Yesu kapena atumwi ake akanakhala ndi mwayi wondipatsa dzina, kodi akanandipatsa lotani? Kodi dzina labwino lofotokoza mbiri yanga kapena khalidwe langa lingakhale liti?’
Funso limeneli tifunika kuliganizira mofatsa kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri.” (Miyambo 22:1) Ndithudi, ngati tili ndi dzina labwino kapena mbiri yabwino m’dera limene timakhala, ndiye kuti tili ndi chuma chamtengo wapatali. Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikakhala ndi dzina labwino ndi Mulungu ndiye kuti tidzapeza chuma chosatha. Kodi zimenezi zingachitike motani? Mulungu akulonjeza kuti adzalemba mu “buku la chikumbutso” mayina a anthu amene amamuopa ndipo adzawapatsa moyo wosatha.—Malaki 3:16; Chivumbulutso 3:5; 20:12-15.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 A Mboni za Yehova ambiri ku Africa ali ndi mayina ogwirizana ndi mitu ya misonkhano imene inachitika panthawi imene anabadwa.
[Mawu Otsindika patsamba 15]
Kodi dzina labwino lofotokoza mbiri yanga kapena khalidwe langa lingakhale liti?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 14]
Kodi Imanueli Anali Ndani?
Mayina a anthu ena m’Baibulo anali olosera zimene munthuyo adzachite. Mwachitsanzo, Mneneri Yesaya anauziridwa kulemba kuti: “Taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamucha dzina lake Imanueli.” (Yesaya 7:14) Dzina limeneli limatanthauza kuti “Mulungu Ali Nafe.” Akatswiri a Baibulo ena anena kuti ulosi umenewu unakwaniritsidwa koyamba pa mfumu ina ya Chiisiraeli kapena pa mwana wa Yesaya. Komabe, wolemba Uthenga Wabwino, Mateyo, anasonyeza kuti ulosi wonse wa Yesaya unakwaniritsidwa pa Yesu.—Mateyo 1:22, 23.
Ena amanena kuti ngati dzina la Imanueli limanena za Yesu, ndiye kuti Baibulo limaphunzitsa kuti Yesu ndi Mulungu. Koma ngati maganizo athu ali amenewa ndiye kuti Elihu, amene analimbikitsa ndi kudzudzula Yobu, nayenso anali Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa dzina lake limatanthauza “Ameneyu Ndiye Mulungu Wanga.”
Yesu sananenepo kuti iye ndi Mulungu. (Yohane 14:28; Afilipi 2:5, 6) Koma anasonyeza kwambiri makhalidwe a Atate ake ndipo anakwaniritsa zonse zimene Mulungu ananena zokhudza Mesiya. (Yohane 14:9; 2 Akorinto 1:20) Dzina lakuti Imanueli limafotokoza bwino kwambiri udindo wa Yesu monga Mesiya, mbadwa ya Davide amene amatsimikizira kuti Mulungu amayanja anthu amene amamulambira.
[Chithunzi]
IMANUELI “Mulungu Ali Nafe”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 15]
Dzina Lokhala Ndi Tanthauzo Lapadera Kwambiri
M’Baibulo, dzina lenileni la Mulungu limapezeka maulendo pafupifupi 7,000. Dzina limeneli, lomwe m’chiheberi limalembedwa ndi zilembo zinayi izi יהוה, nthawi zambiri m’chichewa limalembedwa kuti “Yehova.” Kodi dzina limeneli limatanthauza chiyani? Mose atafunsa kuti dzina la Mulungu ndi ndani, Yehova anati: “Ndidzakhala amene ndidzafune kukhala.” (Eksodo 3:14, NW) Choncho, dzina lenileni la Mulungu limatsimikizira kuti iye akhoza kukhala chilichonse chimene angafune kuti akwaniritse zolinga zake. (Yesaya 55:8-11) Mulungu akatilonjeza chinthu, tingakhulupirire kuti achikwaniritsa ndipo tingamachite zinthu mogwirizana ndi lonjezolo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa cha zimene dzina lake lakuti Yehova limatanthauza.
[Chithunzi patsamba 13]
ABULAHAMU “Tate wa Khamu la Anthu”
[Chithunzi patsamba 13]
SARA “Mfumukazi”