Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Amene Anavutika ndi Chimphepo ku Myanmar Anathandizidwa

Anthu Amene Anavutika ndi Chimphepo ku Myanmar Anathandizidwa

Anthu Amene Anavutika ndi Chimphepo ku Myanmar Anathandizidwa

PA May 2, 2008, ku Myanmar kunabuka chimphepo (chotchedwa Cyclone Nargis) ndipo nkhaniyi inaulutsidwa pa dziko lonse. Chimphepochi chitawomba kuchigawo cha Irrawaddy, anthu pafupifupi 140,000 anafa ndipo ena mwa anthuwa sanaoneke n’komwe.

Koma chochititsa chidwi n’chakuti ngakhale kuti kuderali kuli a Mboni za Yehova ambiri, palibe ndi mmodzi yemwe amene anavulala ndi chimphepochi. Kwenikweni izi zinachitika chifukwa chakuti ambiri anakabisala m’Nyumba za Ufumu zimene zinamangidwa bwino kwambiri. Kumalo ena, a Mboni za Yehova 20 limodzi ndi anthu ena 80 anakhala padenga la Nyumba ya Ufumu kwa maola 9 panthawi imene madzi osefukira anakwera n’kufika pafupifupi mamita 5. Anthu 300 a m’mudziwo anafa koma onse amene anali padengali anapulumuka. M’midzi yambiri kumapezeka kuti nyumba zonse zagwa n’kungotsala Nyumba ya Ufumu yokha.

Patangopita masiku awiri chichitikireni chimphepochi, ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ku Yangon inatumiza gulu la anthu kuti likapereke chithandizo kumpingo wa ku Bothingone m’derali. Gululi linadutsa m’malo osakazidwa ndi chimphepochi, komanso linkayenda mosamala kuti lisafwambidwe, ndipo mumsewu ankangoona mitembo ili ngundangunda. Kenako anakafika ku Bothingone ndi mpunga, makandulo, madzi ndi zinthu zina zofunika. Gululi linali loyamba kukapereka chithandizo kuderali, lomwe linali pachilumba. Atapereka chithandizochi abale anakamba nkhani zolimbikitsa zochokera m’Baibulo, ndipo anawapatsanso Mabaibulo ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo chifukwa katundu wawo yense anali atawonongeka.

Koma Mboni za Yehova zimene katundu wawo anasakazika zinasonyeza mtima wochititsa chidwi kwambiri. Mboni ina ya kumpingo wa m’derali inati: “Katundu wathu yense wapita. Nyumba zathu zaphwasuka. Mbewu zathu zasakazidwa. Chifukwa cha madzi osefukira, madzi oti munthu angathe kumwa sakupezekanso. Koma abale ndi alongo sakudandaula kwambiri monga anthu ena. Iwo akudalira Yehova ndi gulu lake. Titsatira malangizo aliwonse amene tingapatsidwe, kaya oti tikhalebe konkuno kapena oti tisamuke.”

Gulu la Mboni zokwana 30, zomwenso zinalibiretu chilichonse, linayenda ulendo wa maola 10 popita kumalo amene limakalandira chithandizo cha chakudya, zovala ndi malo ogona. Paulendowu gululi linkaimba nyimbo za Ufumu. Gululi lisanafike kumalo olandirira chithandizochi linamva kuti ku tawuni ina yapafupi kukuchitika msonkhano wadera wa Mboni za Yehova ndipo linaganiza zopita kaye kumsonkhanoko. Iwo anatero pofuna kuti akalandire chakudya chauzimu komanso kuti akacheze ndi Akhristu anzawo.

M’chigawo chonse chimene chinakhudzidwa ndi chimphepochi, nyumba 35 za a Mboni zinaphwasulidwa, nyumba 125 zinawonongedwa pang’ono, ndipo Nyumba za Ufumu 8 zinangowonongeka pang’ono mwina ndi mwina. Koma maofesi a nthambi sanakhudzidwe kwenikweni ndi chimphepochi.

Chimphepochi chinagwetsa mitengo yambiri ndipo mitengoyi inatseka misewu yopita ku ofesi yanthambi. Patangopita maola ochepa chichitikireni chimphepochi, abale oposa 30 a ku ofesi ya nthambi anagwira nawo ntchito yochotsa mitengoyi m’misewuyo. Anthu amene ankadutsa pamalo amene abalewa ankagwira ntchito, ankadabwa kwambiri moti ankaima. Pasanapite nthawi yaitali, azimayi ena a Mboni anafika ndi zakumwa zoziziritsa kukhosi ndi zipatso kuti apatse anthu ogwira ntchitoyo komanso ena oyandikira. Ndipo anthu ambiri anagoma kwambiri ndi zimenezi. Moti mtolankhani wina anafunsa kuti: “Kodi ndi ndani amenewa? Akugwiratu ntchito modabwitsa kwabasi.” Atauzidwa kuti ndi a Mboni za Yehova iye anati: “Anthu onse akanakhala ogwirizana ngati Mboni za Yehova bwenzi zinthu zili bwino kwabasi.”

Mwamsanga Mboni za Yehova zinakonza magulu awiri oyang’anira ntchito yopereka chithandizo m’dzikolo. A Mboni ambiri ongodzipereka anagwira nawo ntchito yopereka chithandizochi. Pasanapite masiku ambiri Mboni za Yehova zimene zinkasowa pokhala anazimangira nyumba zatsopano. Gulu lina litapita kukamanga nyumba ya mayi wina wa Mboni, anthu oyandikana nawo anangoti kakasi. Ndipo mayi wina anati: “Taonani mayi wa Mboniyu akumangiridwa nyumba ndi a Mboni anzake. Koma Abuda anzanga sanabwere n’komwe kudzandithandiza. Ndikanadziwa ndikanalola kukhala wa Mboni panthawi imene ankandilalikira ija.”

Gulu lina lomanga nyumba litapita kukaona nyumba ya bambo wina wa Mboni ku tawuni ya Thanlyn linadabwa ndi zimene mwini nyumbayo ananena. Nyumba yake inawonongedwa ndithu koma m’baleyo anati: “Musade nkhawa. Ifetu nyumba yathu sinawonongeke kwenikweni. Tikhoza kumakhala momwemu bwinobwino. Pali a Mboni anzathu ena amene nyumba zawo zawonongekeratu. Mwina mupite mukawathandize iwowo.”

Kudera lina m’tawuni ya Yangon, anthu anathamanga kuti akabisale m’tchalitchi china. Koma anapeza kuti chitseko ndi chokhoma ndipo analephera kulowa. Anthu anakhumudwa kwambiri moti anaganiza zongothyola chitseko cha tchalitchicho. Koma Mboni za Yehova zinathandiza anthu ambiri kuti abisale m’Nyumba za Ufumu panthawi ya chimphepoyi. Mwachitsanzo, ku tawuni ya Dala, banja lina la Mboni za Yehova linatenga anthu 20 amene anasowa mtengo wogwira n’kukabisala nawo m’Nyumba ya Ufumu. Kutacha m’mawa anthuwa anapeza kuti nyumba zawo zonse zaphwasuka ndipo analibiretu chakudya. Bambo wa m’banjali anapeza munthu akugulitsa mpunga ndipo anagula n’kukapatsa anthuwo.

Banja lina la ku Yangon ndi logawikana. Ena ndi a Mboni za Yehova pomwe achibale ena amapita ku zipembedzo zina. Chimphepochi chitangochitika, banja lonseli linapita kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. N’chifukwa chiyani anapita? Mmodzi wa anthu a m’banjalo anati: “Anthu a kutchalitchi kwathu analonjeza kuti adzabwera kudzationa pambuyo pa chimphepochi koma sanabwere. Ndi a Mboni nokha amene munabwera kudzationa. Munatipatsa mpunga ndi madzi. Ndinu osiyana kwambiri ndi matchalitchi enawa.” Achibale awo ambiri amene si Mboni anasangalala ndi nkhani ya mu Nsanja ya Olonda imene inali ndi mutu wakuti: “Yehova Amamva Kulira Kwathu Ndipo Amatithandiza.” Ndipo anayankha kwambiri paphunziroli.

Mayi wina amene ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova anafika kumsonkhano patangodutsa mlungu umodzi chichitikireni chimphepochi. Pamsonkhanopo anawerenga kalata yochokera ku ofesi ya nthambi. M’kalatayo anafotokoza mmene gulu lathandizira anthu ovutika chifukwa cha mphepoyi komanso zimene anthu opulumuka akumana nazo. Mmene kalatayo inkawerengedwa mayiyu anayamba kulira. Iye anakhudzidwa kwambiri atamva kuti Mboni za Yehova zonse zinathandizidwa ndipo palibe wa Mboni amene anasowa. Kenako nayenso anapatsidwa chithandizo komanso abale anakunga tenti pafupi ndi nyumba yake kuti mayiyo azigonamo. Iye anati waona kuti Mboni zamusamalira kwambiri.

Yesu ananena kuti: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Nayenso wophunzira wa Yesu, Yakobe anatsindika mfundo yakuti chikhulupiriro chenicheni chimadziwika ndi ntchito zabwino. (Yakobe 2:14-17) Mboni za Yehova zimatsatira mawu amenewa ndipo zimasonyeza chikondi mwa kuthandiza anthu amene akuvutika.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Baibulo limanena kuti chikhulupiriro chenicheni chimadziwika ndi ntchito zabwino