Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilichonse Chili ndi Nthawi

Chilichonse Chili ndi Nthawi

Chilichonse Chili ndi Nthawi

Baibulo limati: “Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake.” Mfumu yanzeru Solomo, yomwe inalemba mawu amenewa, inalembanso kuti pali mphindi ya kubadwa ndi mphindi ya kumwalira, mphindi ya kumanga ndi ya kupasula, mphindi ya kukonda ndi mphindi ya kudana. Ndipo potsiriza inati: “Wogwira ntchito aona phindu lanji m’chom’sautsacho?”​—Mlaliki 3:1-9.

ANTHU ena akawerenga mawu amenewa, amaganiza kuti Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu analemberatu zinthu zonse zimene zimachitika. Koma kodi Baibulo limaphunzitsadi zimenezi? Popeza kuti “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu,” zimene timapeza mbali ina ya Baibulo ziyenera kugwirizana ndi zimene timapeza m’mbali zinanso. Motero, tiyeni tione zimene malemba ena m’Mawu a Mulungu amanena pankhaniyi.​—2 Timoteyo 3:16.

Nthawi ndi Zotigwera Mwadzidzidzi

M’buku la Mlaliki, Solomo analembanso kuti: “Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m’liwiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima.” N’chifukwa chiyani zili choncho? Solomoyo anayankha kuti: “Yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.”​—Mlaliki 9:11.

Pamenepatu Solomo sanali kutanthauza kuti zochitika pamoyo wa munthu zinalembedweratu, koma amanena kuti anthu sangathe kudziwiratu zotsatira za zinthu zimene akuchita chifukwa “yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.” Nthawi zambiri munthu amakumana ndi mwayi chifukwa choti anali pamalo oyenerera komanso panthawi yoyenerera, kapena amakumana ndi tsoka chifukwa choti anali pamalo olakwika panthawi yolakwika.

Mwachitsanzo, taganizirani za mawu akuti: “Omwe athamanga msanga sapambana m’liwiro.” N’kutheka kuti munamvapo za nkhani yodabwitsa imene inachitika pa mpikisano wina wa akazi, wothamanga mamita 3,000. Uwu unali mpikisano wa masewera otchuka (a Olympics) womwe unachitika mu 1984 mumzinda wa Los Angeles, ku California, m’dziko la United States. Panali othamanga awiri, wina wa ku Britain ndi wina wa ku America, omwe ankaoneka kuti apambana pampikisanowo n’kulandira mendulo ya golidi. Koma mpikisanowo uli mkati, atathamanga theka la mtundawo, anthu awiriwa anawombana. Mmodzi anagwa n’kulephera kudzuka kuti apitirize mpikisanowo ndipo winayo anagwa mphwayi kwambiri moti anakhala nambala seveni.

Kodi tingati zimene zinachitikazi n’zoti zinalembedweratu? Ena amaganiza choncho. Komatu n’zoonekeratu kuti kuwombanako n’kumene kunalepheretsa anthuwa kupambana ndipo palibe aliyense amene akanadziwiratu za ngozi imeneyi. Komano kodi zinalembedweratu kuti adzawombana? Apanso ena amaganiza choncho. Komatu akatswiri onenerera masewera anati anthuwa anawombana chifukwa choti aliyense anali pa liwiro la mtondowadooka poyesetsa kuti apose mnzakeyo. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena, zakuti “yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.” Ngakhale munthu atakonzekera bwanji, n’zotheka kuti chinachake chingachitike mwadzidzidzi n’kusokoneza zinthu, ndipo sikuti zimenezi zimachita kulembedwa ayi.

Ndiyeno kodi Baibulo limatanthauza chiyani ponena kuti “kanthu kali konse kali ndi nthawi yake”? Kodi tingachite chilichonse chimene chingakhudze tsogolo lathu?

Chilichonse Chili ndi Nthawi Yake Yabwino Kwambiri

Ponena kuti kalikonse kali ndi nthawi yake, sikuti wolemba Baibuloyu ankatanthauza kuti Mulungu anakonzeratu zochitika za pa moyo wa munthu aliyense, koma anali kunena za cholinga cha Mulungu ndi mmene chidzakhudzire anthu. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Tikudziwa zimenezi chifukwa cha zimene nkhaniyo ikunena. Atatchula zinthu zambiri zokhala ndi “nthawi yake,” Solomo anati: “Ndaona vuto [zochita, NW] limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti avutidwe nalo. Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake.”​—Mlaliki 3:10, 11.

Inde, Mulungu anapatsa anthu zochita zambirimbiri ndipo Solomo anatchulapo zingapo. Mulungu anatipatsanso ufulu wosankha tokha zochita. Komano chilichonse chili ndi nthawi yake yabwino kwambiri yochichitira. Mwachitsanzo, taganizirani mawu a Solomo akuti “mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo” omwe ali pa Mlaliki 3:2. Alimi amadziwa kuti mbewu iliyonse ili ndi nthawi yabwino yobzalira. Ndiye kodi chingachitike n’chiyani ngati mlimi atanyalanyaza mfundo imeneyi n’kubzala mbewu panyengo yolakwika? Kodi zingakhale zomveka ngati mlimiyo atanena kuti walephera kukolola bwino chifukwa choti zinalembedweratu? Ayi n’zosamveka. Vuto n’lakuti iyeyo sanabzale mbewuzo panthawi yoyenera. Mlimiyo akanachita bwino akanatsatira dongosolo lobzalira mbewu limene Mlengi anakhazikitsa m’chilengedwe.

Motero, tingathe kuona kuti Mulungu sanakonzeretu zochitika pa moyo wa munthu kapena zotsatirapo za zinthu zonse zimene zimachitika, koma anakonzeratu mfundo zinazake zothandiza kuti zochita za anthu zigwirizane ndi cholinga chake. Motero, kuti zochita za anthu ziwayendere bwino, iwo ayenera kudziwa cholinga cha Mulungu ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi cholingacho. Choncho cholinga cha Mulungu n’chimene chinakonzedweratu ndipo sichingasinthidwe koma osati zochitika za pa moyo wa munthu. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anati: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka mkamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:11.

Ndiyeno kodi “mawu” a Mulungu kapena kuti cholinga chake chimene anatchula m’Baibulo, chokhudza dziko lapansi ndiponso tsogolo la anthu, chimene ‘chidzakule’ kapena kuti kukwaniritsidwa, n’chiyani kwenikweni?

M’pofunika Kumvetsa Nthawi ya Mulungu

Mawu a Solomo angatithandize kumvetsa nkhaniyi. Iye atanena kuti “chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake” anatinso “ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.”​—Mlaliki 3:11.

Pali zambiri zimene zalembedwa pofotokozera lemba limeneli. Koma mfundo ndi yakuti, tonsefe panthawi inayake tinadzifunsapo kuti, ‘Kodi cholinga cha moyo n’chiyani nanga tsogolo lathu n’lotani?’ Kuyambira kalekale, anthu akhala akuvutika kumvetsa kuti n’chifukwa chiyani timavutika kugwira ntchito mwakhama pamoyo wathu koma kenako n’kumwalira. Ndi anthu okha amene amaganiza za moyo wawo panopo komanso za tsogolo lawo. Anthufe timalakalakanso kukhala ndi moyo wamuyaya. Timatero chifukwa Malemba amafotokoza kuti, Mulungu “waika zamuyaya m’mitima” ya anthu.

Chifukwa cha mtima wofuna moyo wamuyayawu, anthu akhala akudzifunsa kuti, ‘Kodi palinso moyo wina umene munthu amakhala nawo pambuyo pa imfa?’ Ena amanena kuti pali chinachake chimene chimakhalabe ndi moyo munthu akamwalira. Ena amakhulupirira kuti munthu akafa amakabadwanso kwina monga munthu kapena chamoyo chinachake, ndipo zimenezi zimapitirira kuchitika kwamuyaya. Palinso anthu ena amene amakhulupirira kuti chilichonse chimene chimachitika pa moyo chinakonzedweratu ndi Mulungu ndipo kuti palibe zimene munthu angachite kuti asinthe zimenezi. N’zomvetsa chisoni kuti mfundo zonsezi n’zosakhutiritsa. Zili choncho chifukwa choti Baibulo limanena kuti, anthu paokha sangathe ‘kulondoloza ntchito zimene Mulungu wazipanga kuyambira pachiyambi mpaka chitsiriziro.’

Kuyambira kale, akatswiri oganiza mozama komanso akatswiri a maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba alephera kupeza mfundo zokhutiritsa pankhani imeneyi. Komano, pakuti Mulungu ndiye anaika chikhumbo chimenechi mumtima mwathu, kodi sipomveka kunena kuti iyeyu ndi amene angatipatse mfundo zokhutiritsa pankhaniyi? Ndipotu Baibulo limanena za Yehova kuti: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Salmo 145:16) Mwa kuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo, tingapeze mfundo zokhutiritsa zokhudza moyo ndiponso imfa. Tingaphunzirenso za cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi komanso anthu.​—Aefeso 3:11.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

“Omwe athamanga msanga sapambana m’liwiro.”​—Mlaliki 9:11

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Ngati mlimi atapanda kukolola bwino chifukwa chobzala mbewu panyengo yosayenera, kodi anganene kuti zinalembedweratu?

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Timaganizira za moyo ndi imfa chifukwa Mulungu ‘anaika zamuyaya m’mitima mwathu’