Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mulungu ankawaona bwanji Aisiraeli amene ankakhulupirira nyenyezi?

Buku lina lofotokoza matanthauzo a mawu linati kwenikweni kukhulupirira nyenyezi kumatanthauza “kuona mosamala kayendedwe ka zinthu za mumlengalenga monga dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi pokhulupirira kuti kuyenda kwa zinthu zimenezi kumatha kukhudza moyo wa anthu.” Chaka chilichonse dziko likamayenda pozungulira dzuwa, magulu a nyenyezi zimene zinayalana m’njira inayake amasinthasintha maonekedwe ake m’madera osiyanasiyana a padziko pano. Kuyambira kale, anthu akhala akuona kusintha kumeneku n’kumanena kuti kumatanthauza zinthu zosiyanasiyana.

Zikuoneka kuti amene anayambitsa zokhulupirira nyenyezi ndi Ababulo, ndipo iwowatu ankalambira nyenyezi. Aisiraeli anatengeranso kulambira kumeneku. Pofika mu ulamuliro wa Mfumu Yosiya, n’kuti kukhulupirira nyenyezi kutafala kwambiri m’dzikolo. Mulungu sanabise mmene ankaonera nkhaniyi. Zaka zambiri izi zisanachitike, Chilamulo cha Mose chinali chitaletsa kale kulambira nyenyezi. Munthu aliyense wolambira nyenyezi anayenera kuphedwa.​—Deuteronomo 17:2-5.

Pankhani ya kupembedza, chimodzi mwa zinthu zimene Mfumu Yosiya anachita pofuna kusintha zinthu pakati pa Ayudawo ndicho kuletsa zopereka nsembe ku “dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.” Baibulo limati Mfumuyi inachita zimenezi pofuna “kutsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake.” (2 Mafumu 23:3-5) Masiku ano anthu amene akufuna kulambira Mulungu “ndi mzimu ndi choonadi” amachitanso chimodzimodzi.​—Yohane 4:24.

Kodi “Ana a Zeu” otchulidwa pa Machitidwe 28:11 anali ndani?

Buku la Machitidwe limati mtumwi Paulo akupita ku Roma, anachoka ku Melita kukafika ku Potiyolo, pa ngalawa imene inali ndi dzina lakuti “Ana a Zeu.” (Machitidwe 28:11) Panthawi imeneyo anthu ambiri ankakonda kulemba mawu amenewa pangalawa zawo.

Agiriki ndi Aroma akale ankakhulupirira kuti Zeu (amene ankadziwikanso ndi dzina lakuti Jupita) ndiponso mkazi wake Leda, anali ndi ana aamuna amapasa, Kasitolo ndi Polakisi. Awa ndi amene ankatchewa kuti “Ana a Zeu” ndipo anthu ankawaona ngati akatswiri odziwa bwino kayendedwe ka panyanja, okhala ndi mphamvu zolamulira mafunde. Motero ankatengedwa kuti ndiwo milungu yoteteza anthu oyenda maulendo apanyanja. Anthu apaulendo ankapereka nsembe kwa milungu imeneyi ndipo ankaipembedza kuti iwateteze ku mafunde. Anthu ambiri akaona kuwala kwa mphamvu yangati ya magetsi, kumene ngakhale masiku ano kumaoneka pamwamba pa ngalawa panyanja pakaipa, ankaganiza kuti kuwalako kwenikweni ndi milungu iwiri imeneyi.

Kulambira Kasitolo ndi Polakisi kunali kofala kwambiri pakati pa Agiriki ndi Aroma, ndipo buku lina lakale linanena kuti kunali kofala kwambiri m’madera ozungulira Kurene, cha kumpoto kwa Africa. Ngalawa yotchulidwa m’buku la Machitidwe inali yochokera cha kufupi ndi kumeneku, mumzinda wa Alesandiriya, m’dziko la Aiguputo.

[Chithunzi patsamba 9]

Mwala wa ku Babulo Wosonyeza Mfumu Nazimaruttash ndi Magulu a Nyenyezi

[Chithunzi patsamba 9]

Ndalama ya Dinari Yokhala ndi Chithunzi cha “Ana a Zeu,” cha m’ma 114 Mpaka 113 B.C.E.

[Mawu a Chithunzi patsamba 9]

Stela: Réunion des Musées Nationaux/​Art Resource, NY; coin: Courtesy Classical Numismatic Group, Inc./​cngcoins.com