Kufufuza Munthu Mwakhama
Kalata Yochokera ku Ireland
Kufufuza Munthu Mwakhama
PATSIKULI kunkagwa kamvula kamawawa moti sindinkatha kuona patali chifukwa madzi amvulayo anali kuyenderera pagalasi lakutsogolo kwa galimoto yanga. Nditayenda makilomita 16 ndinafika paphiri lina ndipo ndinkatha kuona bwinobwino tauni ina yotchedwa Westport imene ili kumadzulo kwa dziko la Ireland. Kenako dzuwa litawala, ndinayamba kuona bwinobwino tizilumba tambirimbiri tomwe tinkangooneka ngati miyala yamtengo wapatali pa kansalu ka buluu. Anthu ambiri sakhala m’zilumbazi koma nthawi zina amangodyetserako ziweto zawo.
Chakum’mwera, mphepete mwa nyanjayi ndinkangoona mapiri okhaokha. M’mapiri onsewa munali zomera zamitundumitundu zimene zinkachititsa kuti nthawi ya madzulo mapiriwo azioneka ngati matanthwe a mkuwa. Komanso chapatali pankaoneka phiri losongoka (lotchedwa Croagh Patrick) ndipo anthu a kuderali analipatsa dzina loti Reek. Kenako ndinayendabe m’misewu ing’onoing’ono yodzaza ndi anthu kupita kudera lina kumene a Mboni za Yehova safikafikako.
Munthu amene ndinkamufufuza sankadziwa za ulendo wangawu. Ndinalandira kalata yoti munthuyo anasamukira kuderali ndipo ankafuna kupitiriza kuphunzira Baibulo ndi a Mboni. Ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi pano ndi wamkulu bwanji? Kodi anakwatira? Ndipo kodi amakonda zinthu zotani?’ Ndinayang’ananso m’chikwama kuti nditsimikizire ngati ndatenga Baibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo. Ndinayambanso kuganizira zimene ndinganene kuti ndikulitse chidwi chake chofuna kudziwa uthenga wa Ufumu.
Kenako ndinadutsa phiri la Reek lija. M’malire a minda yambiri imene inakafika m’nyanja munali mipanda ya miyala ndipo mipanda yambiri yamtunduwu inamangidwa cha m’ma 1800, panthawi imene kunali njala yoopsa. Mbalame ina ya mtundu wa dokowe inkauluka monyadira kudutsa pamwamba pa galimoto yathu. Chapatali ndithu tinkaona mitengo ina ya minga itawerama ngati nkhalamba n’kutsamirana.
M’derali nyumba zake zilibe manambala ndipo misewu yake ilibe maina. Moti ndinangouzidwa za maonekedwe a nyumba yake komanso za dzina la tawuniyo basi. Ndiyeno ndinaganiza zokafunsa kwa munthu wogwira ntchito ku positi ofesi, podziwa kuti m’derali a positi ofesi amafika panyumba ya munthu aliyense pokapereka makalata. Kenako ndinafika panyumba ina yamdadada imene munali positi ofesi. Pachitseko cha positi ofesiyo panali chikwangwani choti “Tatseka.” Sindinagwe mphwayi, m’malomwake ndinapita kusitolo ina ndipo mwini sitoloyo anandipatsa mapu a nyumba imene ndinkaifuna m’deralo.
Nditayenda makilomita asanu ndinafika pamalo ena pamene msewu unakhotera kumanja ndipo ndinaona kamsewu kakang’ono kolowera chakumanzere. Ichi ndi chizindikiro chimene ndinauzidwa. Kenako ndinagogoda pachitseko cha nyumba ina yapafupi. Mayi ena achikulire anatuluka n’kundiuza kuti iwo ndi mkhalakale wa deralo koma sankadziwa kumene munthu amene ndinkamufunayo ankakhala. Iwo anandiuza kuti ndilowe m’nyumba yawo poyembekeza kuti ayese kuimba mafoni.
Koma panthawi yonseyi maso awo anali pa ine ndipo n’zachidziwikire kuti ankadzifunsa kuti, ‘Kodi munthu ameneyu ndani ndipo akufuna chiyani?’ Ndinaona kuti pakhomo pawo anakolekapo kachifanizo ka Virigo Mariya komanso pakhoma panali chithunzi chachikulu cha Khristu. Patebulo la kukhitchini panali mikanda ya kolona. Pofuna kuti akhazikike maganizo ndinangowauza kuti, “Ndabweretsa uthenga umene ndatumidwa ndi anzake.”
Mwamuna wawo anatipeza n’kuyamba kundiuza mbiri ya deralo. Panthawiyi mayi aja anaimbira foni munthu woyamba koma sizinathandize ndipo anandiuza kuti ndidikirebe kuti afunse anthu ena pafoni. Zikuoneka kuti palibe aliyense amene ankadziwa munthuyu komanso nyumba imene ankakhala. Nditayang’ana wotchi ndinaona kuti nthawi yatha. Ndiye ndinaganiza zobwerera kuti ndidzayesenso ulendo wina. Ndinawayamikira chifukwa chondithandiza ndipo kenako ndinalowa m’galimoto n’kumabwerera.
Ndinabwererakonso mlungu wotsatira. Patsikuli ndinakumana ndi munthu wina wogwira ntchito mu positi ofesi ndipo anandipatsa mapu abwino. Patangotha mphindi 15 ndinafika pa majiga amene ananena pondipatsa mapu aja. Kenako ndinakhotera kumanzere n’kudutsa kamsewu ka zitunda zambiri pofunafuna chizindikiro china chimene anandiuza. Chizindikiro chake chinali mlatho wowakidwa ndi miyala koma sindinaupeze. Kenako ndinangozindikira kuti ndafika pa nyumba imene inali pamwamba pa phiri ndipo ichi chinali chizindikiro chomaliza chimene anandipatsa. Nyumbayi ndi imene ndinaifufuza kwanthawi yonseyi.
Ndinayamba kuganiza za mmene ndingamuuzire uthenga wabwino. Kenako bambo wina wachikulire anatsegula chitseko. Bamboyo anati: “Pepani achimwene nyumba yomwe mukufunayo ili uko.” Nyumba imene ankalozayo inali mkati mwa mitengo. Ndi chikhulupiriro chonse ndinapita kukagogoda panyumbayo. Podikira kuti atsegule ndinayang’ana nyanja ya Atlantic yomwe inali chapafupi. Kunali mphepo ndipo mafunde ankawomba m’mphepete mwa nyanja. Pakhomopo panangoti zii, ndipo panalibenso munthu wina aliyense pafupi.
Ndinabwererakonso maulendo ena awiri koma osamupeza. Kenako paulendo wina ndinapeza mnyamata wina amene anati: “Nyumba mukunenayo ndi yomweyi koma munthu amene mukumufunayo anasamuka kalekale ndipo sindidziwa kumene anapita.” Ndinamufotokozera mnyamatayo chimene ndinkamufunira munthuyo. Iye anandiuza kuti sanakumanepo ndi a Mboni za Yehova. Komabe ankadabwa chifukwa chimene Mulungu amalolera zinthu zoipa kuchitika chifukwa iye anakumanapo ndi achiwembu. Iye analandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, amene anali atangotuluka kumene, omwe ankafotokoza bwino nkhani imeneyi.
Malemba amatilimbikitsa kufufuza mwakhama anthu onga nkhosa. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti munthu amene ndinkamufufuzayo sindinam’peze. Ngakhale zinali choncho sindidandaula kuti ndinavutika pachabe. Ku Ireland anthu ambiri amafuna kuphunzira uthenga wa Ufumu. Ndi thandizo la Yehova, mbewu za choonadi zimene zinafesedwa mwa munthu ameneyu zidzabala zipatso tsiku lina.