Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tinaunikiridwa ndi Nyenyezi Pamsonkhano”

“Tinaunikiridwa ndi Nyenyezi Pamsonkhano”

“Tinaunikiridwa ndi Nyenyezi Pamsonkhano”

M’chaka cha 2003, umodzi mwa misonkhano ya chinenero chamanja unayenera kuchitika pa August 22 mpaka 24, mumzinda wa Stavropol ku Caucasia. Anthu ochokera m’mizinda 70 ya ku Russia anafika pamalo a msonkhanowo. Komabe, msonkhanowu unatsala pang’ono kulephereka chifukwa akuluakulu a mzindawu sankafuna kuti uchitike. Kutatsala tsiku limodzi kuti msonkhanowu uyambe, woyang’anira malowo anasintha maganizo n’kunena kuti sizitheka kuti msonkhano uchitike pamalowo. Koma litafika Lachisanu pa August 22, abale anakambirana ndi oyang’anira malo ochitira zisudzo kuti msonkhano uchitikire m’chinyumba chawo.

Msonkhano unayamba nthawi ya 3 koloko madzulo, koma nthawi yopuma itangotha, anthu ena anazimitsa magetsi. Zitatero anthu onse amene anali pamalo a msonkhanowo anangokhala m’mipando yawo mpaka pamene msonkhano unayambiranso patatha ola limodzi. Pulogalamu ya tsiku loyamba inatha cha m’ma 9:30 madzulo.

Tsiku lachiwiri msonkhano unayamba cha m’ma 9:30 m’mawa koma kunalibenso magetsi. Kenako anthu aja anadulanso madzi. Zinali zovuta kwambiri kuti abale apitirize msonkhano popanda madzi ndiponso magetsi. Pofika cha m’ma 10:50 m’mawa, abale a m’komiti ya msonkhanowo anaganiza zotsegula zitseko zonse kuti kuwala kwa dzuwa kuzifika m’chinyumbacho. Kenako anaganizanso nzeru ina yabwino kwambiri. Anatenga magalasi akuluakulu n’kuika kunja m’njira yoti kuwala kwa dzuwa kukafika pa magalasiwo kuzikhota n’kufika m’chinyumbacho n’kumaunikira wokamba nkhani. Anthu onse tsopano ankatha kuona wokamba nkhani. Komabe kuwalako kunkamuthobwa m’maso wokamba nkhaniyo moti sankaona bwino manotsi ake. Choncho, abale anaika m’nyumbayo magalasi ena amene ankathandiza kuti kuwala kuzikhota n’kupita kumagalasi ozungulira amene anali kudenga la chinyumbacho. Izi zinachititsa kuti m’nyumba monsemo muziwala bwino moti aliyense ankaika maganizo pamsonkhanowo. Chifukwa cha kuwala kwa magalasi akudengawo, anthu opezeka pamsonkhanowu ananena kuti “tinaunikiridwa ndi nyenyezi pamsonkhano.”

Kenako meya wa mzindawu limodzi ndi akuluakulu ena anafika pamalowo. Iwo anadabwa kwambiri kuona kuti Mboni zikupitirizabe msonkhano wawo. Anachitanso chidwi kwambiri ndi khalidwe la anthu amene anali pamsokhanowo. Palibe amene anakwiya kapena kudandaula. Onse chidwi chawo chinali pa nkhani zomwe zinkakambidwa. Mkulu wa apolisi amene poyamba ankadana ndi Mboni anakhudzidwa kwambiri ndi zimene anaona moti ananena kuti: “Anthu inutu sindidana nanu ndipo ndilibe nanu chifukwa, kungoti tikukhala m’dziko limene limakudani.”

Akuluakuluwo atangochoka, magetsi anayaka. Masiku awiri oyambirira msonkhano unkatha mochedwa, koma palibe amene anachoka mpaka pemphero lomaliza. Ngakhale kuti panali zovuta, chiwerengero cha anthu pa msokhanowu chinkawonjezereka tsiku lililonse. Lachisanu panali anthu okwana 494, Loweruka 535, ndipo Lamlungu panali anthu 611. M’bale amene anapereka pemphero lomaliza anathokoza Yehova chifukwa chowalola kuti achite msonkhano wochititsa chidwiwu. Anthu onse anabalalika ali ndi chimwemwe chodzaza tsaya komanso atatsimikiza mtima kutumikira Atate wawo wakumwamba ndi kutamanda dzina lake.