Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo

Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo

YONA anayenera kuganiza mozama chifukwa anafunika kuyenda ulendo wautali kwambiri, wa makilomita 800. Ulendowu ukanam’tengera pafupifupi mwezi wathunthu kapena kuposerapo. Panali njira ziwiri ndipo iye anafunika kusankha imodzi. Ina inali yaifupi koma yoopsa kwambiri pomwe ina inali yosaopsa koma yaitali kwambiri. Komabe njira zonsezi zinali zodutsa m’zigwa zambiri ndi m’mapiri ochuluka. Yona anafunika kudutsa m’dera la chipululu cha Asuri, n’kuwoloka mitsinje ikuluikulu monga Firate. Komanso anafunika kupeza malo ogona m’matawuni ndi m’midzi ya ku Suriya, Mesopotamiya ndi Asuri. Atayenda ulendowu kwa masiku ambiri, anayamba kuganizira za mzinda wa Nineve umene anali kupitako ndipo anayamba kuchita mantha kwambiri.

Ngakhale zinali choncho, Yona ankadziwa mfundo yakuti sangathe kuzemba ntchito imene anapatsidwa. Tikutero chifukwa choti nthawi ina anayesapo kuchita zimenezi. Nthawi yoyamba imene Yehova anamutuma kukapereka uthenga wa chiweruzo kumzinda wa Nineve, womwe unali waukulu ndiponso wotchuka m’dziko la Asuri, Yona anazemba n’kukwera sitima yopita kudera lina. Ali m’sitimayo, Yehova anachititsa chimphepo cha mkuntho ndipo Yona anadziwa kuti zimene anachitazo zikanaphetsa aliyense amene anali m’sitimayo. Pofuna kupulumutsa anthuwo, Yona anauza oyendetsa sitimayo kuti am’ponye m’madzi. Ndipo anam’ponyadi m’madzimo ngakhale kuti iwo anachita zimenezi asakufuna. Panthawiyi Yona ankaganiza kuti afa. Komabe Yehova anatumiza chinsomba chomwe chinam’meza, kenako patatha masiku atatu chinakamulavula kumtunda ali bwinobwino. Chifukwa cha zimenezi, iye anayamba kuopa Mulungu ndiponso kumumvera kwambiri. *​—Yona chaputala 1 ndi 2.

Yehova atalamula Yona kachiwiri kuti apite ku Nineve, mneneriyo anamvera n’kuyamba ulendo wopita ku mzindawo. (Yona 3:1-3) Komabe, kodi iye anali ataphunzirapodi kanthu pa zimene Yehova anam’chitira? Mwachitsanzo, iye anamuchitira chifundo pom’pulumutsa kuti asafe, sanam’patse chilango pa zimene anachita ndipo anam’patsanso mwayi wina woti akagwire ntchito imene anam’patsa poyamba ija. Kodi Yona anaphunzira kuchitira ena chifundo pambuyo poti Yehova wamuchitira zonsezi? Zikuoneka kuti anthu opanda ungwirofe zimativuta kwambiri kuphunzira kuchitira ena chifundo. Komabe tiyeni tione zimene tingaphunzire pa zimene zinachitikira Yona.

Anasintha Modabwitsa Atamva Uthenga Wachiweruzo

Yona sankaona mzinda wa Nineve ngati m’mene Yehova ankauonera. Pamfundoyi, Baibulo limati: “Koma Nineve ndiwo mudzi waukulu pamaso pa Yehova.” (Yona 3:3) Ndipo Yehova ananena katatu konse m’buku la Yona kuti “Nineve ndiwo mudzi waukulu.” (Yona 1:2; 3:2; 4:11) N’chifukwa chiyani Yehova ananena kuti mzindawu ndi “waukulu” kapena kuti ndi wofunika?

Mzinda wa Nineve unali wakale kwambiri ndipo unali umodzi mwa mizinda yoyambirira imene Nimrode anakhazikitsa pambuyo pa Chigumula. Mzindawu unali waukulu kwambiri ndipo unali ndi matauni ena. Zinkatenga masiku atatu kuti munthu awudutse, kuchokera mbali ina kukafika mbali ina. (Genesis 10:11; Yona 3:3) Komanso mzindawu unali wokongola kwambiri ndipo unali ndi akachisi akuluakulu, mipanda ikuluikulu ndiponso nyumba zochititsa chidwi. Yehova Mulungu ankaona kuti mzindawu unali wofunika kwambiri, osati chifukwa cha kukongola ndi kutchuka kwake koma chifukwa cha anthu a mu mzindawu. Panthawiyi mumzindawu munali anthu ambiri kuposa mzinda wina ulionse. Ngakhale kuti anthuwa anali ochita zoipa, Yehova ankawasamalira. Iye amakonda munthu aliyense payekha ndipo amaona kuti munthu aliyense akhoza kulapa ndi kuphunzira kuchita zinthu zoyenera.

Yona atangolowa mumzindawu, ayenera kuti anachita mantha kwambiri ataona kuti munali anthu ochuluka zedi, oposa 120, 000. * Anayenda kwa tsiku limodzi n’kufika mkatikati mwa mzindawo, mwina pofunafuna malo abwino kuti ayambe kulengeza uthenga wake. Koma kodi iye akanalalikira bwanji uthengawo? Kodi iye ankadziwa chinenero cha Asuri? Kapena kodi Yehova anam’thandiza kuti alankhule chinenerocho mozizwitsa? Sitikudziwa. Koma n’kutheka kuti iye ankalengeza uthengawo m’Chiheberi ndipo munthu wina ankamasulira m’chinenero cha ku Nineve. Mulimonse mmene zinalili, uthenga wake unali wosavuta kumva ndiponso iye sankalalikira n’cholinga choti atchuke. Uthengawo unali wakuti: “Atsala masiku makumi anayi ndipo Nineve adzapasuka.” (Yona 3:4) Iye ankalalikira uthengawu molimba mtima ndiponso mobwerezabwereza zomwe zinasonyezanso kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba. Masiku anonso Akhristu akufunika kuyesetsa kwambiri kukhala ndi makhalidwe amenewa.

N’zodziwikiratu kuti Yona atayamba kulalikira kwa anthu a ku Nineve, anali ndi maganizo oti anthuwo sangasangalale ndi uthenga wake komanso kuti mwina angam’chitire zachiwawa. Koma zimene zinachitika si zimenezi, chifukwa anthu anamvetsera uthenga wake ndipo uthengawo unafalikira mofulumira kwambiri. Pasanapite nthawi, anthu onse mumzindawo anayamba kukambirana za uthenga wachiweruzowu. Nkhani ya Yona imatiuza kuti: “Anthu a Nineve anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli, kuyambira wamkulu kufikira wamng’ono wa iwowa.” (Yona 3:5) Anthu onse, kaya olemera ndi osauka, athanzi labwino ndi ofooka, akulu ndi ana omwe, anachita zinthu zosonyeza kulapa. Posakhalitsa, mfumu ya mzindawu inamva kuti anthu ayamba kulapa.

Mfumu nayonso inayamba kuopa Mulungu, ndipo inachoka pampando wake wachifumu, n’kuvula chovala chake chachifumu ndipo inavala chiguduli, “nikhala m’mapulusa.” Mfumuyi limodzi ndi “nduna zake” inakhazikitsa lamulo lakuti anthu onse apitirize kusala. Inalamulanso kuti anthu onse ndi nyama zomwe avale ziguduli. * Mfumuyi inavomereza modzichepetsa kuti anthu ake anali ochimwa chifukwa ankakonda kuchita zinthu zoipa ndiponso zachiwawa. Komanso, mfumuyi inkakhulupirira kuti Mulungu angawakhululukire ngati iwo atalapa. N’chifukwa chake inanena kuti: “Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.”​—Yona 3:6-9.

Anthu ena amatsutsa zoti anthu a ku Nineve anasintha mofulumira chonchi. Komabe, akatswiri a Baibulo amanena kuti zimenezi zinachitikadi chifukwa anthu akumeneko ankakhulupirira kwambiri za mizimu komanso sankachedwa kusintha maganizo chifukwa cha mantha. N’chifukwa chake Yesu Khristu anatchulanso za kulapa kwa anthu a ku Nineve. (Mateyo 12:41) Iye ankadziwa zomwe ankanena chifukwa panthawi yomwe anali kumwamba, iye ankaona zonse zimene zinali kuchitika ku Nineve. (Yohane 8:57, 58) Koma kodi Yehova anachita chiyani anthuwo atalapa?

Kusiyana kwa Chifundo cha Mulungu ndi Kuuma Mtima kwa Anthu

Patapita nthawi Yona analemba kuti: “Mulungu anawona ntchito zawo, kuti anabwera kuleka njira yawo yoipa; ndipo Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita.”​—Yona 3:10.

Koma kodi zimenezi zikusonyeza kuti Yehova anaona kuti analakwitsa pokonza zowononga anthu a ku Nineve? Ayi, chifukwa Baibulo limati: “Ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo.” (Deuteronomo 32:4) Motero, zimenezi zikungosonyeza kuti mkwiyo wolungama wa Yehova unali utasiya. Iye anaona kuti anthuwo anali atasintha moti sanafunikirenso kupatsidwa chilango. Ndipotu Mulungu anaona kuti imeneyi inali nthawi yoti awasonyeze chifundo.

Atsogoleri achipembedzo amaphunzitsa anthu kuti Yehova ndi wouma mtima, koma zimenezi sizoona. Iye amachita zinthu moganiza bwino, m’njira yoyenera ndiponso mwachifundo. Yehova asanawononge anthu oipa, amawachenjeza kaye pogwiritsa ntchito atumiki ake a padziko lapansi pano. Amachita zimenezi chifukwa amafunitsitsa kuti anthu oipawo alape n’kusiya njira zawo ngati mmene anachitira anthu a ku Nineve. (Ezekieli 33:11) Yehova anauza mneneri wake Yeremiya kuti: “Mphindi imene ndidzanena za mtundu wa anthu, kapena za ufumu, kuti ndizule ndi kupasula ndi kuononga; ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka choipa chawo, ndidzaleka choipacho ndidati ndiwachitire.”​—Yeremiya 18:7, 8.

Ndiyeno kodi zimene Yona analosera zinali zabodza? Ayi, chifukwa ulosiwu unakwaniritsa cholinga chake chochenjeza anthu a ku Nineve. Anthuwa anachenjezedwa chifukwa cha khalidwe lawo loipa ndipo anasintha. Koma anthu a ku Nineve akanati ayambirenso makhalidwe awo oipawo, Mulungu akanawalanga. Ndipo zimenezi n’zimene zinachitikadi pambuyo pake.​—Zefaniya 2:13-15.

Kodi Yona anachita chiyani ataona kuti anthu a ku Nineve sanawonongedwe pa nthawi yomwe iye ankayembekezera? Baibulo limati: “Koma sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima.” (Yona 4:1) Yona anafika mpaka popemphera mokhala ngati akudzudzula Mulungu. Iye ananena kuti zikanakhala bwino akanangokhala kwawo m’malo mopita ku Nineve. Iye ananenanso kuti anali atadziwa kale kuti Yehova sangawononge mzinda wa Nineve ndipo ananena kuti zimenezi n’zimene zinam’chititsa kuthawira ku Tarisi paulendo woyamba uja. Kenako Yona anauza Yehova kuti kuli bwino angofa, kusiyana n’kuti apitirizebe kukhala ndi moyo.​—Yona 4:2, 3.

Kodi vuto la Yona linali chiyani? Sitingadziwe zonse zimene iye ankaganiza, koma chomwe tikudziwa n’choti iye anali atalengeza zoti anthu a ku Nineve adzawonongedwa. Anthuwo anakhulupirira uthenga wake n’kusintha ndipo sanawonongedwe. Kodi Yona ankaopa kuti azinyozedwa n’kumatchedwa kuti anali mneneri wonyenga? Mulimonse mmene zinalili, iye sanasangalale kuti anthuwo analapa ndiponso kuti Yehova anawachitira chifundo. M’malomwake, zikuoneka kuti iye anakwiya kwambiri, n’kumadzimvera chisoni kuti mbiri yake yaipa. Komabe, Mulungu yemwe ndi wachifundo kwambiri anaona zabwino mwa Yona. Yehova sanamulange chifukwa cha kupanda ulemu kumeneku, m’malomwake iye anam’funsa funso lomuthandiza kuganiza lakuti: “Uyenera kupsa mtima kodi?” (Yona 4:4) Kodi Yona anayankha funsoli? Baibulo silinena chilichonse pankhaniyi.

Zimene Yehova Anachita Pofuna Kuphunzitsa Yona

Mneneriyu, yemwe panthawiyi anali atakwiya, anauyamba ulendo wochoka ku Nineve ndipo m’malo mopita kwawo analowera kudera la mapiri cha ku m’mawa. Iye anamanga kamsasa n’kukhalamo kwinaku akuyang’anitsitsa mzinda wa Nineve. Mwina Yona anachita zimenezi chifukwa ankakhulupirirabe kuti mzindawo uwonongedwa. Kodi Yehova akanatani kuti aphunzitse munthu wouma mtimayu kuti adzichitira ena chifundo?

Mkati mwa usiku Yehova anameretsa msatsi ndipo Yona atadzuka n’kuona msatsi wophuka bwinowu, womwe unali ndi masamba akuluakulu, anasangalala kwambiri chifukwa unam’patsa mthunzi wabwino kwambiri kuposa msasa wake uja. Baibulo limati: “Yona anakondwera kwambiri” chifukwa cha msatsi womwe unamera mozizwitsawu. Mwina ankaganiza kuti chimenechi chinali chizindikiro choti Yehova akumudalitsa ndiponso kumuyanja. Komabe Yehova ankafuna kumuphunzitsa zambiri osati kungom’patsa mthunzi wokha, koma ankafuna kumuthandiza kuti mkwiyo wakewo uthe. Yehova anafuna kumufika Yona pamtima, choncho Mulungu anagwiritsa ntchito mphuchi yomwe inadya msatsiwo. Kenako Mulungu anatumiza “mphepo ya kum’mawa yotentha” yomwe ‘inam’lefula.’ Apanso Yona anakwiya kwambiri ndipo anapempha Mulungu kuti kuli bwino angofa.​—Yona 4:6-8. *

Kachiwirinso Yehova anafunsa Yona ngati anali ndi zifukwa zomveka zokwiyira pankhani ya kuuma kwa mtengo wa msatsi uja. M’malo mosonyeza kulapa, iye anayankha kuti: “Kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.” Iyi tsopano inali nthawi yabwino yoti Yehova aphunzitse Yona kufunika kochitira ena chifundo.​—Yona 4:9.

Yona anamva chisoni ndi kuuma kwa msatsi womwe unamera mu usiku umodzi wokha. Koma Mulungu anafotokoza kuti ndi iye amene anachititsa msatsiwu kumera ndiponso kukula, osati Yonayo. Pomalizira pake Mulungu anamuuza kuti: “Sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Nineve mudzi waukulu uwu; mmene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?”​—Yona 4:10, 11. *

Kodi mukuona kufunika kwa zimene Yehova anachita kuti aphunzitse Yona? Yona si amene anameretsa kapena kukulitsa msatsi uja. Yehova ndi amene anapatsa moyo anthu a ku Nineve ndipo ankawasamalira ngati mmene amasamalirira zolengedwa zake zonse padzikoli. Nanga n’chifukwa chiyani Yona ankaona kuti msatsi uja unali wofunika kwambiri kuposa anthu 120, 000 pamodzi ndi zoweta zawo zomwe? Kodi sichinali chifukwa choti iye ankaganiza modzikonda? Ndipotu iye ankadandaula chifukwa choti msatsi umene unkam’patsa mthunzi unali utauma. Kwenikweni Yona anakwiya chifukwa choti anali wodzikonda ndiponso sankafuna kuti anthu azimuona ngati mneneri wabodza.

Limenelitu ndi phunziro labwino kwambiri. Koma mwina mungadzifunse kuti: Kodi Yona anaphunzirapodi kanthu pa zimenezi? Buku la m’Baibulo limene iye analemba limamaliza ndi funso limene Yehova anamufunsa koma silinayankhidwe. Anthu ena otsutsa amanena kuti Yona sanayankhe chilichonse. Koma zoona zake n’zakuti yankho lilipo ndipo yankho limenelo ndi buku la Yonali. Tikutero chifukwa timadziwa kuti Yona ndi amene analemba bukuli lomwe lili ndi dzina lake. Ndiyeno yerekezerani kuti mukuona mneneriyu yemwe poyamba anali wouma mtima, wosafuna kumvera Mulungu komanso wopanda chifundo, akulemba zonse zimene zinachitika pa ulendo wake wa ku Nineve. Panthawiyi Yona anali atasintha ndipo ayenera kuti anali wachikulire, wanzeru komanso wodzichepetsa. N’zoonekeratu kuti Yona anaphunzirapo kanthu pa malangizo anzeru amene Yehova anam’patsa. Anaphunziranso kufunika kochitira anthu ena chifundo. Kodi nafenso pamenepa sitikuphunzira kufunika kochitira ena chifundo?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani nkhani yakuti: “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo​—Anaphunzira pa Zolakwa Zake,” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2009.

^ ndime 9 Zikuoneka kuti mzinda wa Samariya, womwe unali likulu la dziko la Isiraeli, unali ndi anthu 20,000 kapena 30,000 m’nthawi ya Yona. Chiwerengerochi chinali chochepa kwambiri pafupifupi nthawi zisanu kuyerekeza ndi chiwerengero cha anthu a ku Nineve. Panthawi imene mzinda wa Nineve unali wotukuka kwambiri, uyenera kuti unali waukulu kwambiri padziko lonse.

^ ndime 11 Zimenezi zingamveke ngati zodabwitsa, koma sizinali zachilendo m’nthawi imeneyo. Katswiri wina wachigiriki wolemba mbiri yakale, dzina lake Herodito, anafotokoza kuti panthawi ina Aperisi analira maliro a kazembe wina wake wotchuka, ndipo anachita mwambo wa malirowo limodzi ndi ziweto zawo zomwe.

^ ndime 22 Pa lembali, mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “msatsi” amatanthauza zomera zoyanga zimene zimabala zikho.

^ ndime 24 Ponena kuti anthuwo sankadziwa kusiyanitsa dzanja lawo la manja ndi la manzere, Mulungu ankatanthauza kuti iwo sankadziwa chilichonse chokhudza malamulo ake.

[Mawu Otsindika patsamba 16]

Mulungu amafunitsitsa kuti anthu oipa alape n’kusiya njira zawo ngati mmene anachitira anthu a ku Nineve

[Mawu Otsindika patsamba 17]

Mulungu anagwiritsa ntchito msatsi kuti aphunzitse Yona kufunika kochitira ena chifundo