Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumakwaniritsa Zinthu Zotani?

Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumakwaniritsa Zinthu Zotani?

Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumakwaniritsa Zinthu Zotani?

N’CHIFUKWA chiyani Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “kubadwa mwa . . . mzimu” polankhula za kubatizidwa ndi mzimu woyera? (Yohane 3:5) Mawu akuti “kubadwa” akagwiritsidwa ntchito mophiphiritsira, amatanthauza “kuyambika,” monga ngati mawu akuti “kubadwa kwa fuko.” Motero, mawu akuti “kubadwa mwatsopano” amatanthauza “kuyambika kwatsopano.” Choncho, mawu ophiphiritsa akuti “kubadwa” ndiponso “kubadwa mwatsopano,” akutsindika mfundo yakuti pamakhala kuyambika kwatsopano kwa ubwenzi wa pakati pa Mulungu ndi anthu amene amabatizidwa ndi mzimu woyera. Kodi kusintha kwakukulu kumeneku kumachitika motani?

Pofotokoza mmene Mulungu amathandizira anthu kukonzekera kukalamulira kumwamba, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito fanizo lokhudza banja. Iye analembera Akhristu a m’nthawi yake kuti Mulungu ‘adzawatenga iwo kukhala ana ake.’ Zimene zikusonyeza kuti azidzachita nawo zinthu ‘ngati ana ake.’ (Agalatiya 4:5; Aheberi 12:7) Tiyeni tiganizirenso za fanizo la mwana wofuna kulembedwa sukulu uja, kuti timvetse mmene Mulungu adzatengere anthu amenewa kukhala ana ake. Zimenezi zitithandizanso kumvetsa kusintha kumene kumachitika munthu akabatizidwa ndi mzimu woyera.

Kutengedwa Ngati Ana a Mulungu Kumasintha Zinthu

M’chitsanzo chija, mwana uja sanaloledwe kulembetsa sukulu chifukwa si wochokera kudziko lina. Ndiyeno tayerekezerani kuti tsiku lina zinthu zikusintha chifukwa bambo wina wochokera kudziko lina akutenga mwanayo m’njira yovomerezeka ndi lamulo kuti akhale mwana wake. Zimenezi zingachititse kuti mwanayo aloledwe kuphunzira pasukulu ija, popeza kuti tsopano ali ndi ufulu wofanana ndi wa ana ochokera kumayiko ena. Choncho, kutengedwa ngati mwana wa bambo wadziko lina, kwachititsa kuti mwanayo azionedwa kuti ndi wadziko lina.

Zimenezi zikusonyeza zimene zimachitikira anthu amene abadwa mwatsopano. Taonani kufanana komwe kulipo. Mwana wam’chitsanzo chija angaloledwe kuphunzira pasukulupo pokhapokha ngati ali woyenerera mwalamulo, kutanthauza kuti ayenera kukhala wochokera kudziko lina. Koma iye sangakwanitse kuchita zimenezi payekha. Ndi mmenenso zilili ndi anthu amene adzalamulire mu Ufumu wa Mulungu kapena kuti boma la kumwamba. Iwo angakhale oyenerera pokhapokha ngati ‘atabadwanso.’ Koma iwo sangakwanitse kuchita zimenezi paokha chifukwa Mulungu ndi amene amachititsa kuti munthu abadwe mwatsopano.

Kodi n’chiyani chimene chinathandiza kuti mwana uja alembedwe sukulu? N’chifukwa choti anatengedwa ndi bambo wochokera kudziko lina n’kukhala ngati mwana wake. Komabe zimenezi sizinasinthe maonekedwe a mwanayo. Ngakhale zili choncho, mwanayo atatengedwa ndi bamboyo anayamba kuonedwa ngati wadziko lina. Pamenepa tinganene kuti mwanayo anayamba moyo watsopano, ndipo anakhala ngati wabadwa mwatsopano. Iye anakhala mwana wa bamboyo, ndipo zimenezi zinam’thandiza kuti akhale ndi ufulu woyamba kuphunzira pasukulu ija.

Mofanana ndi zimenezi, Yehova anachititsa kuti anthu ena opanda ungwiro asinthe n’kuyenerera kukhala ana ake. Mtumwi Paulo, yemwe anali m’gulu la anthu amenewa, analembera okhulupirira anzake kuti: “Munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene tifuula nawo kuti: ‘Abba, Atate!’ Pakuti mzimuwo uchitira umboni pamodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.” (Aroma 8:15, 16) Choncho, Akhristu amenewo anakhala mbali ya banja la Mulungu, kapena kuti “ana a Mulungu” chifukwa iye anawatenga n’kukhala ana ake.​—1 Yohane 3:1; 2 Akorinto 6:18.

Komabe anthu amene anatengedwa kukhala ana a Mulungu sanasinthe matupi awo, iwo anakhalabe opanda ungwiro. (1 Yohane 1:8) Ndipo monga mmene Paulo anafotokozera, anthuwa amasintha n’kukhala ana a Mulungu iye akawatenga mwalamulo. Ndipo nthawi yomweyo, mzimu wa Mulungu unawachititsa kukhulupirira mwamphamvu kuti akakhala ndi Khristu kumwamba. (1 Yohane 3:2) Mzimu woyera ndi umene unachititsa kuti akhale ndi chikhulupiriro chimenecho, chomwe chinasintha kwambiri moyo wawo. (2 Akorinto 1:21, 22) Motero tinganene kuti iwo anakhala ndi chiyambi chatsopano, kapena kuti anabadwa mwatsopano.

Ponena za anthu amene Mulungu wawatenga kukhala ana ake, Baibulo limati: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.” (Chivumbulutso 20:6) Ana a Mulungu amenewa adzalamulira monga mafumu pamodzi ndi Khristu mu Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma lakumwamba. Ndipo mtumwi Petulo analembera okhulupirira anzake kuti adzalandira “cholowa chosawonongeka ndi chosadetsedwa ndi chosasuluka,” chimene Mulungu ‘anawasungira kumwamba.’ (1 Petulo 1:3, 4) Kunena zoona, cholowa chimenechi ndi chamtengo wapatali kwambiri.

Komabe, nkhani ya ulamuliroyi ikubweretsa funso lina lakuti: Ngati anthu obadwanso adzalamulire monga mafumu kumwamba, kodi iwo adzalamulira ndani? Tikambirana funso limeneli m’nkhani yotsatirayi.

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi Paulo ananena zotani pankhani ya anthu otengedwa kukhala ana a Mulungu?