Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amaona Kuti Pali Chipembedzo Chimodzi Chokha Choona?

Kodi Mulungu Amaona Kuti Pali Chipembedzo Chimodzi Chokha Choona?

Nkhani ya Onse Yapadera

Kodi Mulungu Amaona Kuti Pali Chipembedzo Chimodzi Chokha Choona?

Anthu ambiri ali m’zipembedzo zimene anabadwiramo. Ena akakula, amadzasankha okha chipembedzo chimene akufuna. Ndipo pali zipembedzo zambirimbiri zimene munthu angasankhe. Koma mwina munadzifunsapo kuti, ‘Kodi palibe vuto lililonse ngati nditasankha chipembedzo chimene ndikufuna?’

Funso limeneli lidzayankhidwa mu Nkhani ya Onse ya mutu wakuti: “Kodi Mulungu Amaona Kuti Pali Chipembedzo Chimodzi Chokha Choona?” Nkhani ya m’Baibulo imeneyi idzakambidwa padziko lonse lapansi m’mayiko oposa 230. M’madera ambiri, nkhaniyi idzakambidwa pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, Lamlungu pa April 26, 2009. Mboni za Yehova za m’dera lanu zingasangalale kwambiri kukuuzani nthawi ndi malo kumene kukakambidwire nkhaniyi. Tikukulimbikitsani kuti mudzapezekepo patsikuli.