Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Analemberatu Zomwe Zidzachitikire Munthu Aliyense?

Kodi Mulungu Analemberatu Zomwe Zidzachitikire Munthu Aliyense?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Mulungu Analemberatu Zomwe Zidzachitikire Munthu Aliyense?

Anthu ena amati Mulungu analemberatu tsiku limene munthu aliyense adzafe. Ndiponso ena amakhulupirira kuti zimene zimatichitikira pamoyo zinakonzedweratu moti sizingasinthidwe. Kodi inuyo mumakhulupirira zimenezi?

Mwina mungadzifunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani tifunika kumapemphera ngati zilidi zoona kuti sitingasinthe zimene zingadzatichitikire m’tsogolo, komanso ngati Mulungu analemberatu tsogolo lathu? Ndipo ngati tsogolo lathu linalembedweratu, n’chifukwa chiyani timayesetsa kuteteza moyo wathu? N’chifukwa chiyani timamanga lamba tikakwera galimoto? Ndiponso n’chifukwa chiyani timapewa kuyendetsa galimoto titamwa mowa?’

Baibulo silivomereza ngakhale pang’ono makhalidwe olakwikawa. N’chifukwa chake Aisiraeli anauzidwa kuti azichita zinthu zowathandiza kupewa ngozi, m’malo moganiza kuti zimene zingawagwere ndi zimene Mulungu anakonzeratu. Mwachitsanzo, Mulungu anawauza kuti azimanga kampanda padenga la nyumba zawo. Cholinga cha kampandako chinali choti munthu asagwe mwangozi akakhala padenga la nyumbazo. Zikanakhala kuti Mulungu anakonzeratu zoti munthu adzagwe padenga, kodi akanawapatsa malangizo amenewa?​—Deuteronomo 22:8.

Nanga bwanji za anthu amene amafa ndi masoka achilengedwe, kapena ngozi zina? Kodi zinali zolembedweratu kuti “adzafa tsiku limenelo”? Ayi, chifukwa Solomo, yemwe analemba nawo Baibulo anati “koma yense angoona zomgwera m’nthawi mwake [kapena kuti mosayembekezereka NW].” (Mlaliki 9:11) Choncho, kaya tikumane ndi zinthu zoopsa chotani, tisamaganize kuti n’zimene Mulungu analemberatu.

Anthu ena amaganiza kuti mawu amenewa akutsutsana ndi zimene Solomo ananena kuti: “Kanthu kali konse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake; mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira.” (Mlaliki 3:1, 2) Kodi pamenepa Solomo ankalimbikitsa mfundo yoti Mulungu anakonzeratu tsogolo la munthu aliyense? Tiyeni tione zimene ankatanthauza.

Solomo sankatanthauza kuti Mulungu anakonzeratu tsiku loti munthu aliyense adzabadwe ndi kufa. M’malomwake, iye ankatsindika mfundo yakuti anthu ena amabadwa, ena n’kumafa. Zimenezi zikutanthauza kuti munthu aliyense amakumana ndi zabwino komanso mavuto pamoyo wake. N’chifukwa chake Solomo analemba kuti pali “mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka.” Solomo anasonyeza kuti zinthu zomwe zimachitika pamoyo wa munthu sizachilendo ndipo zimachitikira “chilichonse cha pansi pa thambo.” (Mlaliki 3:1-8; 9:11, 12) Choncho, mfundo yake inali yakuti tikamachita chilichonse pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku, tisamaiwale Mlengi wathu.​—Mlaliki 12:1, 13.

Ngakhale kuti Mlengi wathu amadziwa bwino kwambiri nkhani zokhudza moyo ndiponso imfa, iye samakonzeratu zomwe zidzatichitikire munthu aliyense m’tsogolo. Baibulo limanena kuti Mulungu anapereka mwayi woti tonse tidzathe kupeza moyo wosatha. Koma iye satikakamiza kupeza moyo wosathawo. M’malomwake, Mawu ake amati: “Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.”​—Chivumbulutso 22:17.

Indedi, tiyenera kufunitsitsa ‘kumwa madzi amoyo.’ Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu sanalemberetu zimene zidzatichitikire m’tsogolo. Koma zimene timasankha, maganizo athu ndiponso zochita zathu n’zimene zimakhudza kwambiri tsogolo lathu.