Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

2 Dziwani Zoona Zake Zokhudza Mulungu

2 Dziwani Zoona Zake Zokhudza Mulungu

2 Dziwani Zoona Zake Zokhudza Mulungu

“Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona.”​—Yohane 17:3.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA ZIMAWAVUTA KUDZIWA MULUNGU MOLONDOLA? Anthu ena amati kulibe Mulungu ndipo ena amanena kuti iye si munthu weniweni koma ndi mphamvu chabe. Enanso amakhulupirira kuti kuli Mulungu koma iwo amaphunzitsa zinthu zotsutsana pankhani ya mmene Mulungu alili.

KODI MUNGATANI KUTI MUDZIWE MULUNGU MOLONDOLA? Njira imodzi imene tingam’dziwire bwino Mulungu ndiyo kuona zimene iye analenga. Mtumwi Paulo anati: “Chilengedwere dziko kumka m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino lomwe. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Mukhoza kuphunzira zambiri zokhudza nzeru ndi mphamvu za Mlengi wathu ngati mutayang’anitsitsa zimene Mulungu analenga.​—Salmo 104:24; Yesaya 40:26.

Komabe, kuti mudziwe zoona zenizeni zokhudza mmene Mulungu alili, muyenera kufufuza mosamala kwambiri m’Baibulo. Musalole anthu ena kukusankhirani zimene muyenera kukhulupirira. Koma muzitsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Musamatengere nzeru za dongosolo lino la zinthu, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Mwachitsanzo, taonani mfundo zotsatirazi zimene Baibulo limanena zokhudza Mulungu.

Mulungu ali ndi dzina. Dzina la Mulungu linkapezeka kambirimbiri m’mabaibulo oyambirira. Ndipo m’mabaibulo ambiri masiku ano, dzinali limapezeka m’malo ambiri monga pa Salmo 83:18. Lembali limati: “Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”

Yehova Mulungu amakhudzidwa ndi zochita za anthu. Ngakhale kuti Yehova anapulumutsa mtundu wa Aisiraeli mu ukapolo wa ku Iguputo, iwo nthawi zina ankanyalanyaza malangizo ake. Zimenezi ‘zinkam’mvetsa chisoni’ kwambiri ‘Woyera wa Isiraeli.’​—Salmo 78:40, 41.

Yehova amatisamalira aliyense payekhapayekha. Nthawi ina polankhula ndi ophunzira ake, Yesu anati: “Kodi mpheta ziwiri samazigulitsa kakobili kamodzi kochepa mphamvu? Koma palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa. Koma tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga. Choncho musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.”​—Mateyo 10:29-31.

Mulungu sakondera anthu a mtundu winawake. Mtumwi Paulo anauza Agiriki a ku Atene kuti, “kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale pa nkhope yonse ya dziko lapansi.” Iye ananenanso kuti Mulungu “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:26, 27) Nayenso mtumwi Petulo ananena kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu ulionse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:34, 35.

KODI TIDZAPEZA MADALITSO OTANI? Baibulo limati anthu ena ndi akhama “potumikira Mulungu; koma mosam’dziwa molondola.” (Aroma 10:2) Mukadziwa zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza Mulungu, si mudzasocheretsedwa ndipo mudzatha ‘kuyandikira Mulungu.’​—Yakobe 4:8.

Kuti mudziwe zambiri, onani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * mutu 1 wakuti, “Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 6]

Njira imodzi imene tingam’dziwire bwino Mulungu ndiyo kuona zimene iye analenga