Kodi Mukudziwa?
Kodi Mukudziwa?
Kodi zimene Yesu analosera kuti adani adzamanga mpanda wa zisonga kuzungulira Yerusalemu zinachitikadi?
Mu ulosi wake wonena za kuonongedwa kwa Yerusalemu, Yesu ananena kuti: “Masiku adzakufikira iwe pamene adani ako adzamanga mpanda wa zisonga kukuzungulira, nadzakutsekereza ndi kukusautsa kuchokera kumbali zonse.” (Luka 19:43) Zimene Yesu ananenazi zinachitikadi mu 70 C.E. pamene asilikali a Roma, motsogozedwa ndi Titus anamanga mpanda kuzungulira mzinda wa Yerusalemu. Panali zifukwa zitatu zimene Titus anamangira mpandawo. Iye ankafuna kuti Ayuda alephere kuthawa, avomereze kuti agonja ndiponso kuti asatuluke kukafunafuna chakudya.
Katswiri wina wolemba mbiri yakale wa m’nthawi ya atumwi, dzina lake Flavius Josephus, anafotokoza kuti panthawi yomanga mpandawo, asilikali a Roma anagawidwa m’magulu ndipo ankapikisana kuti aone gulu limene lingamalize msanga mbali imene lagawiridwa. Asilikaliwo anadula mitengo yomangira mpandawo m’dera lalikulu lokwana makilomita 16 kuzungulira mzinda wa Yerusalemu. Mpanda womwe anamangawo unali wa makilomita 7 ndipo anamaliza kuumanga m’masiku atatu okha. Josephus ananena kuti asilikaliwo atachita zimenezi, “Ayuda analibiretu mpata wothawa.” Ndipo chifukwa cha zimenezi, chakudya chonse cha Ayuda chinatha ndipo anayamba kuphana okhaokha. Kenako patapita miyezi isanu, asilikaliwo anagonjetsa mzinda wa Yerusalemu.
Kodi Mfumu Hezekiya anamangadi ngalande yamadzi yolowa mu mzinda wa Yerusalemu?
Hezekiya anakhala mfumu ya Yuda kuyambira m’chaka cha 745 B.C.E. mpaka mu 717 B.C.E., ndipo panthawiyi ufumu wa Asuri, womwe unali wamphamvu kwambiri padziko lonse unali paudani ndi ufumu wa Yuda. Baibulo limatiuza kuti Hezekiya anayesetsa kuchita zinthu zoteteza mzinda wa Yerusalemu ndipo anaonetsetsanso kuti mu mzindawu muzikhala madzi okwanira nthawi zonse. Zina mwa ntchito zimene iye anagwira ndizo kukumba ndi kumanga ngalande yotalika mamita 533, yoti izibweretsa mu mzindawu madzi ochokera pakasupe.—2 Mafumu 20:20; 2 Mbiri 32:1-7, 30.
M’zaka za m’ma 1800, akatswiri ofukula zinthu zakale anatulukira ngalande imeneyi ndipo anayamba kuitchula kuti Ngalande ya Hezekiya kapena Ngalande ya Siloamu. Mkati mwa ngalandeyi, anapeza malo ena amene panalembedwa zina ndi zina zokhudza gawo lomalizira la ntchito yomanga ngalandeyi. Akatswiri ambiri a maphunziro amakhulupirira kuti kalembedwe ka zilembo zimene zinapezeka m’ngalandeyo ndi ka m’nthawi ya Hezekiya. Komabe, zaka 10 zapitazo, akatswiri ena anena kuti mwina ngalandeyi inamangidwa patapita zaka 500 kuchokera m’nthawi ya Hezekiya. Koma mu 2003, gulu la asayansi a ku Israel linatulutsa zotsatira za kafukufuku wawo yemwe cholinga chake chinali kupeza nthawi yeniyeni imene ngalandeyo inamangidwa. Kodi akatswiriwa anapeza zotani?
Dr. Amos Frumkin wa pa Hebrew University ku Yerusalemu anati: “Takhala tikupanga kafukufuku poyeza tizinthu topezeka m’makoma ndiponso m’miyala ya ngalande ya Siloamu, ndipo tapeza kuti ngalandeyi inakumbidwa m’nthawi ya Hezekiya.” Poikira ndemanga pa nkhani yomweyi, magazini ya Nature, yomwe imafotokoza za sayansi inati: “Umboni umene akatswiriwa apeza, zilembo za m’ngalandeyi, ndiponso nkhani zakale zokhudza ngalandeyi, zikutsimikizira kuti ngalandeyi inakumbidwa m’zaka za m’ma 700 BC. Zimenezi zachititsa kuti nthawi imene ngalande ya Siloamu inamangidwa ikhale yodziwika bwino kwambiri poyerekezera ndi zinthu zina zonse zomangamanga zotchulidwa m’Baibulo.”