Ndikusangalala Ngakhale Kuti Ndine Wolumala
Ndikusangalala Ngakhale Kuti Ndine Wolumala
Yosimbidwa ndi Paulette Gaspar
Nditangobadwa kumene, ndinkaoneka wathanzi moti ndinkalemera pafupifupi makilogalamu atatu, komabe madokotala anaona kuti ndili ndi vuto linalake lalikulu. Pomwe ndinkabadwa mafupa anga ena anathyoka chifukwa ndinabadwa ndi matenda ena ake, omwe amachititsa kuti mafupa akhale ofewa kwambiri. Ndipo nthawi yomweyo anandipititsa kuchipinda chochitira opaleshoni koma madokotala ankaona kuti ndimwalira pasanathe tsiku limodzi.
NDINABADWA pa June 14, 1972 mu mzinda wa Canberra, womwe ndi likulu la dziko la Australia. Tsiku loyamba linadutsa ndili ndi moyo ngakhale kuti madokotala ankaganiza kuti ndimwalira. Koma kenako ndinayamba kudwala chibayo. Madokotala sanandipatse mankhwala aliwonse chifukwa ankaona kuti ndimwalirabe basi. Ngakhale kuti iwo ankaganiza chonchi, sindinamwalire.
Nthawi imeneyi iyenera kuti inali yovuta kwambiri kwa makolo anga. Madokotala ena omwe ankaoneka ngati akuwafunira zabwino anawauza kuti asavutikane nane kwambiri chifukwa iwo ankaona kuti ndifabe basi. Ndipotu pa miyezi itatu imene ndinakhala m’chipatala, makolo anga sankaloledwa ngakhale n’kundigwira komwe. Madokotalawo anachita zimenezi poopa kuti makolo angawo akhoza kundivulaza ngati atamandigwira. Kenako madokotala ataona kuti mwina sindifa, anauza makolo anga kuti akandisiye kunyumba yosungira ana olumala.
Koma makolo anga sanalole zimenezi ndipo ananditengera kunyumba kwathu. Panthawiyi n’kuti mayi anga atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Choncho zimene ankaphunzira zinawathandiza kudziwa kuti ndi udindo wawo kundisamalira. Komabe zinali zovuta kuti iwo azipeza nthawi yocheza nane chifukwa choti ankathera nthawi yawo yambiri akundisamalira komanso kundipititsa ku chipatala. Mafupa anga ankathetheka ndi zinthu zazing’ono monga akamandisambitsa ngakhalenso ndikangoyetsemula.
Ndinayamba Kuvutika Maganizo
Nditayamba kukula, ndinkangokhala panjinga ya anthu olumala ndipo zinali zosatheka kuti ndiphunzire kuyenda. Ngakhale kuti panali mavuto amenewa, makolo anga ankandisamalira mwachikondi kwambiri.
Ndiponso mayi anga ankandiuza uthenga wotonthoza wa m’Baibulo. Mwachitsanzo, iwo anandiphunzitsa kuti m’tsogolomu, Mulungu adzasandutsa dziko lapansili kukhala paradaiso, ndipo anthu adzakhala ndi thanzi labwino komanso adzakhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Salmo 37:10, 11; Yesaya 33:24) Komabe, mayi anga anandiuza mosapita m’mbali kuti panopa n’zosatheka kupeza moyo umenewu mpaka dziko lapansi latsopano lidzabwere.
Kenako, ndinayamba kuphunzira pasukulu ina ya ana olumala. Koma aphunzitsi anga sanandilimbikitse kuti ndikhale ndi zolinga zilizonse pamoyo ndipo inenso ndinalibe zolinga zilizonse. Komanso zinali zovuta kupirira mavuto omwe ndinkakumana nawo chifukwa ana ambiri kusukuluko ankandichitira nkhanza. Kenako anandipititsa kusukulu ya ana abwinobwino. Ngakhale zinali choncho ndinaona kuti zinali zondivuta kwambiri kuti ndiyambe kucheza ndi anthu ena. Komabe ndinachita khama mpaka kumaliza sukulu.
Panthawi imene ndinali ku sekondale, ndinkaona kuti moyo wa ana asukulu anzanga unali wopanda tanthauzo. Ndinkaganiziranso mfundo za m’Baibulo zimene mayi anga anandiphunzitsa. Ndinkadziwa ndithu kuti zimene anandiphunzitsazo zinalidi zoona. Koma panthawiyi, mfundo za m’Baibulozi zinali zisanandifike mumtima. Kwa kanthawi ndithu ndinkangochita zinthu zoti ndizingosangalala ndi moyo basi ndipo sindinkaganizira n’komwe za tsogolo langa.
Nditakwanitsa zaka 18, ndinachoka panyumba pathu n’kumakakhala kunyumba inayake ndi anzanga olumala. Ndinasangalala kwambiri ndi kusamukaku ngakhale kuti ndinkachitanso mantha. Ndinali ndi ufulu wochita zinthu pandekha, kucheza ndi anzanga ndipo ndinkaona kuti ndikusangalala ndi moyo. Patapita nthawi, anzanga ambiri anakwatiwa ndipo inenso ndinayamba kulakalaka kukwatiwa. Koma zinali zovuta kupeza mwamuna chifukwa cha vuto langali ndipo zimenezi zinandikhumudwitsa kwambiri.
Komabe, sindinaimbepo Mulungu mlandu chifukwa cha vutoli. Ndinaphunzira kuti n’zosatheka kuti Mulungu achitire anthu zinthu zoipa. (Yobu 34:10) Komanso ndinavomereza kuti ndili ndi vutoli ndipo sindingathe kuchita zinthu zina. Komabe ndinayamba kuvutika maganizo kwambiri.
M’kupita kwa Nthawi, Ndinayamba Kusangalala
Mayi anga anazindikira kuti ndayamba kuvutika maganizo, ndipo anadziwitsa m’bale wina yemwe anali mkulu mu mpingo wapafupi ndi kumene ndinkakhala. M’baleyu anandiyimbira foni n’kundilimbikitsa kuti ndizifika pamisonkhano yachikhristu ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Komanso mlongo wina anayamba kuphunzira nane Baibulo mlungu uliwonse.
Zimenezi zinandithandiza kukumbukira mfundo za choonadi cha m’Baibulo, zomwe mayi anga anandiphunzitsa ndipo moyo wanga unayamba kusintha. Ndinkasangalala kucheza ndi Akhristu anzanga. Koma kuyambira ndili mwana sindinkauza ena mmene ndikumvera chifukwa ndinkaopa kuti angandikhumudwitse. Ndikuganiza kuti zimenezi zinachititsa kuti ndisamakonde kwambiri Mulungu. Ngakhale zinali choncho, ndinaona kuti ndibwino kuti ndidzipereke kwa Yehova. Motero, mu December 1991, ndinabatizidwa posonyeza kuti ndinadzipereka kwa iye.
Kenako ndinachoka ku nyumba imene ndinkakhala ndi anzanga olumala aja n’kukakhala pandekha. Zimenezi zinali ndi ubwino komanso kuipa kwake. Mwachitsanzo, ndinkasowa wocheza naye komanso ndinkachita mantha kuti amuna akhoza kumadzandivutitsa. Posakhalitsa ndiyambiranso kuvutika maganizo kwambiri. Ngakhale kuti ndinkaoneka wosangalala, pansi pamtima ndinkavutika maganizo kwambiri ndipo ndinkafunitsitsa kupeza mnzanga wapamtima kuti ndizicheza naye.
Ndimaona kuti Yehova Mulungu anandipatsadi munthu wotero chifukwa akulu a mumpingo wathu anakonza zoti mlongo wina dzina lake Suzie apitirize kuphunzira nane Baibulo. Mlongoyu sanangokhala mphunzitsi wanga chabe, koma anakhalanso mnzanga wapamtima.
Suzie anandiphunzitsa mmene ndingalalikirire kwa anthu pa mpata uliwonse umene wapezeka kapenanso kunyumba ndi nyumba. Zimenezi zinandichititsa kuti ndiyambe kumvetsa bwino makhalidwe a Mulungu ndi kumukonda kwambiri. Komabe ngakhale kuti ndinali nditabatizidwa, ndinali ndisanayambe kukonda kwambiri Mulungu moti mpaka nthawi ina ndinaganiza zongosiya kumutumikira. Ndinafotokozera Suzie zimenezi
ndipo iye anandithandiza mmene ndingathetsere maganizo amenewa.Suzie anandithandizanso kuzindikira kuti ndinkakhala mosasangalala chifukwa chokonda kucheza ndi anthu osakonda kwambiri Yehova. Choncho, ndinayamba kucheza ndi anthu omwe ankakonda kwambiri Mulungu, makamaka achikulire. Komanso, popeza kuti sindinkagwirizana ndi mayi ndiponso mchimwene wanga, ndinayamba kuchita zinthu zoti ndiyambirenso kugwirizana nawo. Ndinadabwa kuona kuti kuchita zimenezi kunandithandiza kwambiri kuti ndikhale wosangalala kuposa kale. Abale ndi alongo anga auzimu ndiponso anthu a m’banja mwathu anandithandiza kuti ndizisangalala. Ndipo Yehova anandithandizanso kwambiri kuti ndikhale ndi mphamvu komanso wosangalala.—Salmo 28:7.
Ndinayamba Utumiki Wanthawi Zonse
Nditachoka ku msonkhano kumene ndinamvetsera nkhani imene inanena za mmene atumiki achikhristu anthawi zonse amasangalalira, ndinaona kuti inenso ndikhoza kuchita zimenezi. Ndinkadziwa ndithu kuti ntchito imeneyi ingakhale yovuta chifukwa cha kulumala kwangaku. Komabe, nditaiganizira mofatsa nkhaniyi ndinapemphera, kenako ndinalembetsa kuti ndiyambe utumikiwu ndipo ndinauyambadi mu April 1998.
Kodi ndikanatani kuti ndikwanitse kulalikira ngakhale kuti ndine wolumala? Mwachibadwa, ndimakonda kuchita zinthu pandekha ndipo sindifuna kuti ndizivutitsa anthu ena monga kumandiyendetsa kapena kundichitira zinthu zina. N’chifukwa chake Suzie ndi mwamuna wake Michael, anandiuza nzeru yoti ndigule njinga yamoto. Koma kodi ndikanakwanitsa kumakwera njingayo? Monga mmene mukuonera pachithunzichi, njingayi anaipanga mogwirizana ndi mmene ineyo ndilili. Ngakhale kuti kathupi kanga n’kakang’ono kwambiri moti kamalemera makiloglamu 19 okha, njingayi anaikonza bwino kwambiri moti sindivutika n’komwe kuikwera ndiponso kutsika.
Njingayi imandithandiza kuti ndiziyenda ndekha popanda kudalira munthu wina. Motero ndimatha kuyendera anthu ndiponso kuphunzira nawo Baibulo panthawi imene tagwirizana. Kunena zoona ndimasangalala ndikakwera njingayi n’kumamva kamphepo kakuomba pankhope yanga.
Masiku ano ndimakonda kwambiri kucheza ndi anthu m’misewu ndipo anthuwa nthawi zambiri amakhala aulemu. Ndipo ndimasangalala kuthandiza anthu kuphunzira Baibulo. Ndimakumbukira nthawi ina ndikulalikira khomo ndi khomo ndi m’bale wina wamtali. Tinafika pakhoma la mayi wina, yemwe ankandiyang’anitsitsa modabwa ndipo m’baleyo anapereka moni kwa mayiyo. Kenako mayiyo anafunsa m’baleyo kuti, “Kodi mayiwa amatha kulankhula?” Tonse tinafa ndi phwete. Titamaliza kumulalikira, mayiyo anakhulupirira kuti ndimathadi kulankhula.
Masiku ano ndikusangalala ndi moyo ndipo ndimakonda kwambiri Yehova Mulungu. Ndikuthokoza kwambiri mayi anga chifukwa chondiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Ndipo ndikuyembekezera mwachidwi nthawi imene Mulungu adzapanga zinthu ‘zonse kukhala zatsopano,’ zomwe zikutanthauzanso kuti kulumala kwangaku kudzatha.—Chivumbulutso 21:4, 5.
[Mawu Otsindika patsamba 30]
“Ndinavomereza kuti ndili ndi vutoli ndipo sindingathe kuchita zinthu zina. Komabe ndinayamba kuvutika maganizo kwambiri”