Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Akufunafuna Malangizo Othandiza

Anthu Akufunafuna Malangizo Othandiza

Anthu Akufunafuna Malangizo Othandiza

MASIKU ano kuli malangizo ambiri moti ndi anthu savutika kuwapeza. Ndipo padziko lonse, anthu opanga ndi kugulitsa mabuku opereka malangizo pa nkhani zosiyanasiyana akuchulukirachulukira. Mabukuwa akupangidwa ndiponso kugulitsidwa kwambiri m’mayiko monga Britain, United States, Japan ndiponso ku Latin America. Komanso malangizowa akufalitsidwa kwambiri m’mavidiyo, m’misonkhano ndiponso mapulogalamu a pa TV. Malangizowa amawakonza m’njira yoti munthu athe kuthana ndi mavuto payekha, popanda kufunsa akatswiri a zamaganizo, ankhoswe kapena atsogoleri a chipembedzo. Kodi malangizowa amakhala okhudza nkhani zotani?

Ena mwa malangizo amene amapezeka kwambiri m’mabukuwa ndi okhudza zimene munthu angachite kuti akhale ndi moyo wosangalala, zimene anthu okwatirana angachite kuti azikondana kwambiri komanso mmene angalerere bwino ana. Nkhani zina zimene zimapezekanso kwambiri m’mabukuwa ndi zothandiza anthu ovutika maganizo, achisoni komanso amene banja lawo latha. Komanso anthu ambiri amafuna malangizo okhudza zimene angachite kuti athane ndi vuto la kudya kwambiri, kusuta ndiponso uchidakwa. Koma kodi malangizowa amakhala othandizadi? Nthawi zina amathandiza ndithu, koma nthawi zambiri sathandiza. Choncho tingachite bwino kwambiri kuganizira mozama chenjezo la m’Baibulo lakuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”​—Miyambo 14:15.

Dziwani kuti mabuku opereka malangizowa ndi osiyana kwambiri ndi mabuku amene amathandiza munthu kuphunzira luso linalake monga kujambula zithunzi, kuwerengera masamu kapena kuphunzira chinenero. Mabuku ophunzitsa munthu luso linalake angakhale othandiza ndiponso otsika mtengo poyerekezera ndi kuphunzira luso limeneli kusukulu. Koma monga mmene tafotokozera, mabuku opereka malangizo pankhani za bizinesi, zam’banja, za kulera ana komanso zothandiza munthu kukhala ndi mtendere wamumtima, amakhala osiyana kwambiri ndi mabuku ophunzitsa munthu luso linalake. Mabuku a malangizo amalimbikitsa anthu kuti azikhala moyo winawake kapena kuti azitsatira mfundo zinazake. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi amene akupereka malangizowa ndi ndani? Kodi iye amawatenga kuti?’

Nthawi zina, akatswiri olemba mabukuwa amalemba nkhani zawo asanapeze umboni wokwanira. Ena angalembe nkhani zimene anthu angakonde kumva chifukwa amadziwa kuti apeza ndalama zambiri. Mwachitsanzo m’dziko linalake, makampani opanga mabukuwa amapeza ndalama zoposa madola 8 biliyoni chaka chilichonse.

Kodi Mabukuwa Ndi Othandizadi?

Anthu akamawerenga mabuku opereka malangizowa, amayembekezera kuti apeza mfundo zothandiza. Koma nthawi zina malangizo ake amakhala ovuta kuwamvetsa chifukwa kawirikawiri amangolimbikitsa mfundo yakuti: ‘Chofunika n’kungokhulupirira kuti malangizowa akuthandizani, ndipo adzakuthandizanidi. Ndipotu chilichonse chimene mungafune mungachipeze, kaya ndi ndalama, thanzi labwino ndiponso banja losangalala, bola kungokhulupirira basi.’ Kodi malangizo oterewa angakhaledi othandiza? Kodi angakuthandizeni kuthana ndi mavuto anu?

Mwachitsanzo, ganizirani za ena mwa mabuku otchuka kwambiri monga opereka malangizo pankhani za m’banja komanso a mmene munthu angakhalire bwino ndi ena. Kodi mabukuwa amathandizadi anthu kukhala ndi mabanja olimba ndiponso osangalala? Nthawi zambiri sathandiza. Munthu wina yemwe anawerenga mabuku ena onena za chikondi, omwe anayenda malonda kwambiri ku Latin America, ananena kuti mabukuwa “amalangiza anthu zimene angachite kuti azikondana kwambiri ndiponso kuti asamadziderere.” Wolemba wake anafotokoza kuti munthu amene akukhalabe m’banja limene silikuyenda bwino ndiye kuti sakudzifunira zabwino. Pamenepa, wolembayo ankatanthauza kuti chinthu chofunika kwambiri n’choti munthu azichita zinthu zoti zizimuyendera, m’malo molimbana ndi kuthetsa mavuto m’banjamo.

N’zoona kuti mabukuwa angakhale ndi malangizo ena othandiza. Koma nthawi zambiri malangizowa amakhala oipa. Mwachitsanzo, katswiri wolemba mabuku otere angapereke malangizo abwino kwambiri pankhani inayake, koma iye angapereke malangizo achabechabe pankhani inanso. Choncho zingakhale zovuta kutsatira malangizo ambirimbiri omwenso nthawi zambiri amatsutsana. Nangano kodi mungadalire malangizo a ndani? Dzifunseni kuti: ‘Kodi munthu amene analemba malangizowa anafufuza kaye bwinobwino kapena anangolemba maganizo ake? Kodi analemba zinthu zimenezi chifukwa chokonda chuma kapena kufuna kutchuka?’

Buku limodzi lopereka malangizo, lomwe ndi lakale kwambiri koma likugwirabe ntchito masiku ano, ndi Baibulo. Lili ndi malangizo a nkhani zosiyanasiyana kuphatikizapo nkhani zimene zimalembedwa m’mabuku a malangizo. Ndipo lathandiza anthu ambiri kutsatira malangizo akuti: “Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu . . . ndi kuvala umunthu watsopano.” (Aefeso 4:23, 24) Baibulo limatipatsa nzeru zimene zimatithandiza kuzindikira chimene chimachititsa mavuto athu komanso mmene tingawathetsere. Koposa zonse, limatipatsanso zifukwa zomveka bwino zimene zingatithandize kuchita zinthu zoyenera. M’nkhani yotsatirayi tikambirana zimenezi.