Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tikamavutika Ndiye Kuti Mulungu Akutilanga?

Kodi Tikamavutika Ndiye Kuti Mulungu Akutilanga?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Tikamavutika Ndiye Kuti Mulungu Akutilanga?

Kodi munayamba mwakumanapo ndi mavuto aakulu amene anakuchititsani kuganiza kuti Mulungu akukulangani? Mavuto ena monga kudwala mwadzidzidzi, kuvulala kwambiri pangozi, kapena imfa yosayembekezereka ya wachibale angatichititse kuganiza kuti Mulungu akutilanga.

Komabe, dziwani kuti Mulungu amafuna kuti anthu azisangalala ndiponso kuti asamavutike. Mfundo imeneyi ikuonekera bwino pa zimene Mulungu anachita atalenga anthu awiri oyambirira. Iye anawaika “m’munda wa Edene,” womwe unali paradaiso ndipo akanakhala ndi moyo wopanda mavuto ena alionse.​—Genesis 2:15.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthuwa anasankha kusamvera Mulungu, ndipo zimenezi zinachititsa kuti ataye mwayi wokhala ndi moyo wosatha ndiponso wopanda mavuto. Zotsatira zake zinali zoipa kwambiri, osati kwa iwo okha komanso kwa ana awo, kuphatikizapo ifeyo. N’chifukwa chiyani zinali choncho? Kuti timvetse mfundo imeneyi tiyeni tiyerekezere zimene zingachitike bambo atalephera kulipira lenti ya nyumba imene akukhala. Zimenezi zingachititse kuti banja lonse lithamangitsidwe m’nyumbamo n’kuyamba kuvutika. Mofanana ndi zimenezi, tonsefe timakumana ndi mavuto chifukwa cha kusamvera kwa Adamu ndi Hava. (Aroma 5:12) Patapita zaka zambiri kuchokera pamene makolo athuwa anachimwa, munthu wina wolungama dzina lake Yobu, ananena kuti ngati mavuto ake ataikidwa “pamuyeso,” ndiye kuti angakhale ‘olemera kuposa mchenga wam’nyanja.’​—Yobu 6:2, 3.

Timakumananso ndi mavuto chifukwa chakuti sitimadziwa zam’tsogolo. Mwachitsanzo, munthu wina womanga ndi kugulitsa nyumba angamange nyumba m’dera limene mumachitikachitika ngozi zamoto. Chifukwa chosadziwa, inuyo mungagule nyumbayo n’kumakhalamo. Kodi zimenezi sizingakhale zoopsa kwa inuyo ndiponso banja lanu? Kodi zingakhale zomveka kunena kuti mavuto amene mungakumane nawowo ndi chizindikiro chosonyeza kuti Mulungu akukulangani? Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”​—Miyambo 14:15.

N’zolimbikitsa kudziwa kuti ngakhale timakumana ndi mavuto, Mulungu wakonza kuti posachedwapa awathetsa. Nthawi imeneyo ikadzafika, inuyo simudzakumananso ndi mavuto, kuona ena akuvutika kapena kumva nkhani zokhudza mavuto. Chisoni, zopweteka, imfa ndiponso kulira zidzatha. (Chivumbulutso 21:4) Ndiponso timalimbikitsidwa tikadziwa kuti Mulungu walonjeza kuti anthu adzamanga nyumba ndi kudzala mbewu. Zinthu zimenezi sizidzaonongeka ndi nkhondo kapena masoka ena. M’malomwake aliyense “adzasangalala nthawi zambiri” ndi ntchito yamanja ake.​—Yesaya 65:21-25.

Komabe, kodi panopo mungatani kuti mulimbane ndi mavuto, pamene mukuyembekezera kuti Mulungu adzawachotseretu? Choyamba, Baibulo limatilangiza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” (Miyambo 3:5) Choncho muyenera kudalirani Mulungu kuti akutsogolereni ndiponso kuti akuthandizeni. Daliraninso kwambiri nzeru zochokera kwa Mulungu zimene zimapezeka m’Baibulo. Zimenezi zidzakuthandizani kuti muzichita zinthu mwanzeru ndiponso mudzapewa mavuto ena.​—Miyambo 22:3.