Ulendo Wopita Kudera la Kutali Kwambiri
Kalata Yochokera ku Russia
Ulendo Wopita Kudera la Kutali Kwambiri
TINANYAMUKA pa kandege kathu mu mzinda wa Yakutsk ndipo pang’ono ndi pang’ono kanayamba kukwera m’mwamba kudutsa m’chigwa cha Tuymaada. Tinadutsa nyanja zambiri za madzi oundana, zina zikuluzikulu ndipo zina zing’onozing’ono. Tinadutsanso mapiri a Verkhoyanskiy, ophimbidwa ndi chipale chofewa, omwe pamwamba pake pankaoneka kunyezimira kwa dzuwa. Titayenda ulendo wa makilomita 900, tinafika m’mudzi wa Deputatskiy.
Ichi chinali chiyambi cha ulendo wanga wopita ku Sakha Republic komwenso kumadziwika kuti Yakutia. Derali ndi lokongola komanso la mapirimapiri, ndipo ndi lalikulu kwambiri kuposa mayiko onse a ku madzulo kwa Ulaya kuwaphatikiza pamodzi. M’nyengo yotentha, ku derali kumatentha madigiri seshasi 40 ndipo m’nyengo yozizira, kumazizira kwambiri mpaka kufika madigiri seshasi -70. Ndiponso m’derali muli zinthu zowolerana za nyama zakufa zikuluzikulu zomwe zinkapezeka kale koma masiku ano sizipezekanso. Ngakhale kuti papita zaka zambiri kuchokera pamene ndinapita ku derali, ndikukumbukira bwino kwambiri timatawuni ting’onoting’ono takumeneko tomwe nthawi zina timakutidwa ndi nkhungu. Ndimakumbukiranso kuwala kwa mlengalenga kochititsa chidwi zedi ndiponso anthu ansangala komanso athanzi a mtundu wa Yakut.
Komatu ulendo wathu sunathere m’mudzi wa Deputatskiy, chifukwa ineyo ndiponso mnzanga yemwe ndinali naye paulendowu tinakonza zopitanso ku midzi ina ingapo. Mudzi woyamba unali wa Khayyr, womwe uli chakumpoto, pamtunda wa makilomita 300, kufupi ndi nyanja ya Laptev, yomwe ili kumpoto kwa Siberia. Koma kodi n’chifukwa chiyani tinakonza zoyenda ulendowu? Chinali chifukwa chakuti panthawi ina m’mbuyomu, mayi wina wa Mboni za Yehova atafika kumidziyi, anapeza anthu ambiri omwe ankafunitsitsa kuphunzira Baibulo, choncho ifeyo tinkafuna kukawalalikira anthu amenewa. Ngakhale kuti pali mtunda wa makilomita 1,000, kuchokera kwathu ku Yakutsk kukafika ku midziyi, ifeyo ndi amene tili pafupi ndi midziyi poyerekeza ndi Mboni za ku madera ena.
Madzulo titafika ku Deputatskiy, tinapeza galimoto yopita ku Khayyr ndipo mwini wake anatiuza kuti tikwere ndipo tilipira ndalama zochepa. Poyamba tinakayikira kukwera galimotoyo titaona kuti ndi yachikale, yakutha zedi ndiponso chifukwa chakuti inkanunkha petulo yekhayekha. Komabe tinaganiza zongokwera galimotoyo ndipo tinanyamuka ngakhale kuti sitinadziwe n’komwe zimene tikumane nazo paulendowo.
Mipando ya m’galimotoyo inali yozizira kwambiri ngati mmene pankazizirira panja. Kenako tinapempha mwiniwakeyo kuti aime ndipo ataima, tinafunafuna zovala za mphepo m’zikwama zathu, n’kuvala. Komabe zimenezi sizinathandize.
Koma dalaivalayo amaoneka kuti samamva kuzizira chifukwa anali atazolowera nyengo ya kuderali.
Kenako iye anatifunsa kuti: “Kodi munaonapo kuwala kodabwitsa komwe kumaoneka kumpoto?” Ineyo nditamuuza kuti sindinaonepo kuwalako, iye anaimika galimoto ndipo tonse tinatuluka panja. Kwa kanthawi ndithu tinaiwaliratu zoti kunja kukuzizira moti tinangoti chilili n’kumayang’anitsitsa mwachidwi kuwala kwa mitundu yosiyanasiyana komwe kunkaoneka ngati kuli pafupi kwambiri.Titafika pamalo ena m’mamawa, galimoto yathu inatitimira m’madzi oundana koma tinathandizana ndi dalaivalayo kuitulutsa. Tinatitimiranso kambirimbiri mu msewu wa madzi oundana wopita ku Khayyr. Dzuwa litatuluka m’pamene ndinazindikira kuti sitinkayenda m’misewu koma m’mitsinje ya madzi oundana. Pamapeto pake tinafika ku Khayyr cha m’ma 12 koloko masana, titayenda kwa maola okwana 16 kuchokera ku Deputatskiy. Tinkayembezera kuti tidwala chifukwa choti tinazizidwa kwambiri, koma kutacha tinadzuka tili bwinobwino ngakhale kuti ineyo ndinkamva dzanzi m’zala za kumiyendo basi. Choncho kuti dzanzi lisiye, anthu akumeko anandipatsa mafuta kuti ndipake m’zalazo.
Monga mmene mukudziwira, nthawi zambiri ifeyo ndi amene timayendera anthu m’makomo mwawo tikamalalikira. Koma anthu a ku Khayyr atangomva kuti tafika, iwo ndi amene anatitsatira kumene tinafikirako. Kwa milungu iwiri ndi theka imene tinakhala m’derali, tsiku lililonse tinkaphunzira ndi anthu Baibulo. Ndipo nthawi zina tinkachita zimenezi kuyambira m’mamawa mpaka pakati pa usiku. Tinasangalala kuonana ndi anthu ambiri ansangala ndiponso odziwa kulandira alendo omwenso anali ndi chidwi kwambiri ndi Mawu a Mulungu. Amayi ambiri achikulire a mtundu wa Yakut ankatiuza kuti: “Timakhulupirira kuti kuli Mulungu ndipo kubwera kwanu kudera la kutali ngati kuno, ndi umboni wa zimenezi.”
Tinasangalalanso kwambiri ndi chikhalidwe cha anthu a kuderali. Mwachitsanzo, iwo amaunjika zibulumwa za madzi oundana m’mphepete mwa nyumba zawo, ngati m’mene anthu amasungira nkhuni. Akafuna madzi, amangoika chigulumwa chimodzi m’poto n’kuchitereka pamoto kuti chisungunuke. Anthu a m’derali anatikonzera nsomba yokoma kwambiri yotchedwa chir yomwe imapezeka m’nyanja ya Arctic. Nsombayi akangoipha amaiumitsa ndi madzi oundana, n’kuilezaleza kenako amainyika mu mchere wosakaniza ndi tsabola ndipo amaidya yosaphika. Anthuwa ankakondanso kutiuza za zinthu zakale kwambiri zomwe zinawolerana zimene zimapezeka m’derali. Zina mwa zinthu zimenezi ndi mitengo komanso nyanga za njovu za mtundu winawake.
Nditachoka ku Khayyr, ndinapita ku midzi ina ya kutali kwambiri ya ku Yakutia, kukayendera anthu omwe ankafuna kuphunzira Baibulo, ndipo nthawi zambiri ndinkayenda pandege. Anthuwa ndi ansangala ndiponso achikondi kwambiri. Nthawi ina ndinakumana ndi kamnyamata kenakake komwe kanazindikira kuti ineyo ndimachita mantha ndikakwera ndege. Choncho pofuna kundilimbikitsa, kamnyamatako kanandilembera khadi n’kujambulapo mpheta ziwiri ndiponso ndege ndipo analembapo mawu akuti: “Inu a Sasha, mukakwera ndege musamawope kuti mugwa. Mateyo 10:29.” Zinandikhudza mtima kwambiri nditawerenga lembali pomwe pali mawu a Yesu onena za mpheta akuti: “Palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa.”
M’nkhani ino ndangofotokoza zinthu zochepa chabe zimene ndinasangalala nazo ku Yakutia. Ndikaganizira derali, lomwe ndi lozizira kwambiri ndiponso lamapirimapiri, ndimakumbukira anthu ochititsa chidwi ndiponso ansangala amene ndinawapeza kumeneku.
[Zithunzi patsamba 25]
Anthu a mtundu wa Yakut ndi ansangala ndiponso odziwa kulandira alendo