Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1. Pemphani Mulungu Kuti Akuthandizeni

1. Pemphani Mulungu Kuti Akuthandizeni

Zimene Mungachite Kuti Muzimvetsa Baibulo

1. Pemphani Mulungu Kuti Akuthandizeni

Mayi wina wa ku Italy, dzina lake Ninfa, anati: “Nthawi inayake ndinkakonda kuwerenga Baibulo ndisanagone. Ndinkachita zimenezi chifukwa ndinkadziwa kuti ndi Mawu a Mulungu. Ngakhale kuti kuwerenga Baibulo sikunkandisangalatsa, ndinkangoliwerenga kuti ndidziwe zimene Mulungu analemba, chifukwa cholinga changa chinali choti ndiwerenge Baibulo lonse. Poyamba, ndinkamva zonse zimene ndinkawerenga, koma ndinasiya kuliwerenga nditafika m’machaputala ena ovuta kwambiri.”

KODI inunso munakumanapo ndi vuto langati la Ninfa? Anthu ambiri anakumanapo ndi vuto limeneli. Koma monga mmene taonera m’nkhani yoyamba ija, amene analemba Baibulo ndi Yehova Mulungu, ndipo iye amafuna kuti inuyo muzimvetsa bwino Mawu ake. Komano kodi mungatani kuti muzilimvetsa? Choyamba, pemphani Mulungu kuti akuthandizeni.

Anthu ambiri ankaona kuti atumwi a Yesu anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba,” chifukwa sanapite kusukulu za Arabi zophunzitsa zachipembedzo. (Machitidwe 4:13) Komabe, Yesu anawatsimikizira kuti iwo akhoza kumvetsa Mawu a Mulungu. Kodi zimenezi zikanatheka bwanji? Yesu anati: “Mthandizi, mzimu woyera, umene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse.” (Yohane 14:26) Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu umenewu, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito, polenga dziko lapansi ndi zamoyo zonse. (Genesis 1:2) Iye anagwiritsanso ntchito mphamvu imeneyi pouzira anthu okwana 40 kuti alembe maganizo ake m’Baibulo. (2 Petulo 1:20, 21) Ndipo mzimu womwewo ndi umene umathandiza anthu amene amafunitsitsa kumvetsa Baibulo.

Kodi mungatani kuti Mulungu akupatseni mzimu wake woyera? Muyenera kum’pempha muli ndi chikhulupiriro choti akuyankhani. Ndiponso muyenera kum’pempha mosalekeza. Yesu anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. . . . Ngati inu . . . mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:9, 13) Lembali likusonyeza kuti Yehova amapereka mzimu wake woyera mowolowa manja, kwa anthu amene amam’pempha ndi mtima wonse. Mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito imeneyi ingakuthandizeni kumvetsa Mawu a Mulungu amene analembedwa m’Baibulo zaka masauzande ambiri zapitazo. Mzimu wa Mulungu ungakupatseninso nzeru zomwe zingakuthandizeni kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pamoyo wanu.​—Aheberi 4:12; Yakobe 1:5, 6.

Choncho, nthawi zonse mukamawerenga Baibulo, muzipemphera kwa Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera umene ungakuthandizeni kuti mumvetse Mawu ake.