Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiyeni Tikaone Malo Ochititsa Chidwi Osindikizira Mabuku

Tiyeni Tikaone Malo Ochititsa Chidwi Osindikizira Mabuku

Tiyeni Tikaone Malo Ochititsa Chidwi Osindikizira Mabuku

N’KUTHEKA kuti sikoyamba kuti muwerenge magazini ngati ino. Mwina Mboni za Yehova zinayamba zafikapo pakhomo panu n’kukugawirani Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kuti zikuthandizeni kumvetsa bwino Baibulo. Kapenanso munaonapo Mboni za Yehova zikugawira magazini amenewa m’misewu kapena m’misika. Ndipotu magazini a Nsanja ya Olonda oposa 35 miliyoni amafalitsidwa mwezi uliwonse. Magazini amenewa ndi amene amafalitsidwa kwambiri padziko lonse lapansi kuposa magazini ena aliwonse.

Koma kodi munayamba mwadzifunsapo kuti mabuku ndiponso magazine amenewa amachokera kuti ndiponso kuti amapangidwa motani? Mboni za Yehova zili ndi malo ambiri osindikizira mabuku. Koma kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione malo amodzi okha omwe ali ku Wallkill, New York, m’dziko la America. Tikudziwa kuti ambiri mwa anthu amene amawerenga mabuku athu sangakwanitse kukaona malowa ku America. Choncho nkhani ino ndiponso zinthunzi zake zikuthandizani kudziwa zambiri za malowa.

Kuti mabuku asindikizidwe, choyamba pamakhala nkhani yolembedwa. Kenako Dipatimenti Yolemba Nkhani, yomwe ili ku Brooklyn, New York imatumiza nkhanizo kudzera pakompyuta ku Dipatimenti Yojambula Zithunzi. Ndiyeno dipatimentiyi imakonza nkhanizo kuti athe kuzisindikiza. Ku Wallkill, mwezi uliwonse amalandira mipukutu ya mapepala yokwana 1,400, ndipo tsiku lililonse amagwiritsa ntchito mapepala olemera matani 80 kapena 100. Mipukutuyi, yomwe ina imakhala yolemera makilogalamu 1,400, amailowetsa m’makina akuluakulu asanu omwe amakhala ndi zipangizo zosindikizira. Kenako makinawo amasindikiza, kudula ndiponso kupinda mapepala kuti akhale magazini a masamba 32 ngati amene mukuwerengawa. Nangano mabuku amawakonza bwanji? Pali makina apadera omwe amapinda ndi kumata mapepala kuti akhale mabuku. Makina amodzi amakhala ndi mizera iwiri ndipo patsiku limodzi lokha, mzera umodzi ungatulutse mabuku a zikuto zolimba okwana 50,000 kapena mabuku a zikuto zofewa okwana 75,000. Ndiponso patsiku limodzi, mzere winawo ungatulutse mabuku a zikuto zofewa okwana 100,000.

Mu 2008, kumalowa kunasindikizidwa mabuku oposa 28,000,000, ndipo mabuku oposa 2.6 miliyoni mwa mabuku amenewa, anali mabaibulo. M’chaka chomwechi, anasindikizanso magazini okwana 243,317,564. Ku malo amenewa amasungirakonso mabukuwa a m’zinenero 380. Kodi mabukuwa akapangidwa, chimachitika n’chiyani?

Dipatimenti Yotumiza Mabuku imawatumiza ku mipingo ya Mboni za Yehova yokwana 12,754 ya m’dziko la America ndiponso mipingo yokwana 1,369 ya ku Caribbean ndi Hawaii. Ndipo mwezi uliwonse, Dipatimenti Yotumiza Mabuku imatumiza mabuku olemera makilogalamu 14 miliyoni kupita ku mipingo ya m’dziko la America lokha.

Chofunika kwambiri ku malo osindikizira mabukuwa si makina ayi, koma ndi anthu. Anthu oposa 300 amagwira ntchito kumalowa m’madipatimenti osiyanasiyana monga, Yojambula Zinthunzi, Yogawa Nthawi Yosindikizira, Yosindikiza, Yoika Zikuto ndiponso Yotumiza Mabuku. Anthu onsewa salipidwa ndipo ndi a zaka zoyambira 19 mpaka 92.

Anthu ogwira ntchitoyi amakonda kwambiri anthu amene amafunitsitsa kulandira, kuphunzira, kulimbikitsidwa ndiponso kutsogoleredwa ndi mfundo za m’Baibulo zimene zimapezeka m’mabukuwa. Tikukhulupirira kuti inuyo muli m’gulu la anthu amenewa ndipo sitikukayika kuti mabukuwa amakuthandizani kuti mudziwe Yehova Mulungu ndiponso Yesu Khristu, ndipo zimenezi zidzakuthandizani kuti mudzapeze moyo wosatha.​—Yohane 17:3.

[Zithunzi patsamba 16]

[Chithunzi chachikulu patsamba 17]