Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Kodi zinatheka bwanji kuti munthu amene anayamba kusuta kwambiri chamba ndi fodya ali mwana, asiye kusuta? Kodi n’chiyani chinathandiza munthu wina yemwe anali m’gulu la zigawenga kuti asiye khalidwe lake losachedwa kupsa mtima ndiponso lodana ndi anthu amitundu ina? Tiyeni tione zimene anthuwa ananena.

ZA MUNTHUYU

DZINA: HEINRICH MAAR

ZAKA: 38

DZIKO: KAZAKHSTAN

POYAMBA: ANALI WA CHAMBA NDI FODYA

KALE LANGA: Ndinabadwira chakummwera m’dziko la Kazakhstan, m’dera lomwe lili pamtunda wa makilomita 120 kuchokera mu mzinda wa Tashkent. Derali limakhala louma ndiponso lotentha kwambiri m’nyengo ya chilimwe mpaka kufika madigiri 45. Koma m’nyengo yozizira, kumazizira kwambiri mpaka kufika pafupifupi madigiri −10 ndipo imeneyi ndi nyengo yabwino kwambiri kulima mphesa ndi chamba.

Makolo anga anachokera ku Germany ndipo anali achikhristu ngakhale kuti sankapita kutchalitchi. Komabe, iwo anandiphunzitsa kuloweza pamtima pemphero la Atate Wathu. Nditafika zaka 14, mayi ndiponso mchemwali wanga wamkulu anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kwa kanthawi ndithu. Nthawi ina ndinamvetsera pamene azimayi awiri a Mboni, amene ankaphunzira Baibulo ndi mayi anga, ankawasonyeza dzina la Mulungu lakuti Yehova m’Baibulo la mayi angawo. Zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri. Komabe patapita nthawi, mayi anasiya kuphunzira Baibulo ndipo chidwi changa pazinthu zauzimu sichinapitirire. Nthawi ina aphunzitsi athu kusukulu anatiuza nkhani zoipa zambiri zokhudza Mboni za Yehova zomwe anthu ankati ndi kagulu kampatuko. Komabe popeza kuti ineyo ndi mchemwali wanga tinasonkhanapo ndi Mboni za Yehova, ndinawauza kuti zimene ankanenazo zinali zabodza.

Ndili ndi zaka 15, ananditumiza kusukulu ku Russia, kukaphunzira ntchito mu mzinda wa Leningrad. Mzindawu tsopano umadziwika ndi dzina lakuti St. Petersburg. Kusukuluko ndinkauza anzanga amene ndinkagona nawo chipinda chimodzi, zochepa zimene ndinkadziwa zokhudza Yehova. Kenako ndinayamba kusuta ndipo ndikapita kwathu ku Kazakhstan, ndinkagula chamba mosavuta ngakhale kuti chinali choletsedwa. Komanso panthawi imeneyo ndimamwa kwambiri mowa ndiponso vinyo amene tinkapanga tokha.

Nditamaliza kuphunzira ntchitoyo, ndinalowa m’gulu la asilikali a dziko la Soviet Union ndipo ndinakhala m’gululi kwa zaka ziwiri. Komabe, ndinkakumbukira mfundo zina ndi zina za m’Baibulo zimene ndinaphunzira ndili mwana. Nthawi zina ndikapeza mpata, ndinkauza asilikali anzanga mfundo zokhudza Yehova ndipo ena akamanena zinthu zabodza zokhudza Mboni za Yehova, ndinkawatsutsa.

Nditamaliza ntchito ya usilikali ndinasamukira ku Germany. Ndili kumalo osungirako anthu akumayiko ena, ndinalandira buku lothandiza kuphunzira Baibulo, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Ndinawerenga bukuli mwachidwi ndipo ndinaona kuti zimene anafotokoza m’bukuli zinali zoona. Komabe, zinali zovuta kuti ndisiye kusuta fodya ndiponso chamba. Kenako, ndinasamukira kufupi ndi mzinda wa Karlsruhe, kumene ndinakumanako ndi munthu wina wa Mboni za Yehova, ndipo anayamba kundiphunzitsa Baibulo.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Kwanthawi yaitali ndinkaona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Ndipo nditawerenga buku lothandiza kuphunzira Baibulo lomwe ndinapatsidwa lija, ndinakhulupiriradi kuti mayankho onse a mafunso ofunika kwambiri pamoyo wathu amapezeka m’Baibulo. Komabe, panapita nthawi yaitali ndithu kuti ndisinthe makhalidwe oipa. Koma lemba la 2 Akorinto 7:1, linandilimbikitsa kuti ndisiye “chilichonse choipitsa cha thupi ndi cha mzimu,” zomwe zinatanthauza kuti ndisiye kusuta chamba ndiponso fodya.

Sindinavutike kusiya kusuta chamba. Koma zinanditengera miyezi 6 kuti ndisiye kusuta fodya. Tsiku lina munthu wa Mboni yemwe ankandiphunzitsa Baibulo uja anandifunsa kuti, “Kodi cholinga cha moyo wako n’chiyani?” Funso limeneli linandipangitsa kuganizira mofatsa za khalidwe langa losuta fodya. Ndinayeserapo maulendo angapo kuti ndisiye kusuta koma zinkandivutabe. Ndiyeno ndinaganiza kuti ndizipemphera kwa Mulungu kuti andithandize kuti ndisasute, m’malo mosuta n’kupempha Mulungu kuti andikhululukire. Koma mu 1993, ndinasankha tsiku loti ndidzasiye kusuta. Ndipo Yehova wandithandiza kwambiri chifukwa kuyambira tsiku limenelo sindinagwirepo ndudu ya fodya.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopa ndili ndi thanzi labwino chifukwa ndinasiya khalidwe losuta chamba ndi fodya lomwe limawonongetsa ndalama ndiponso thanzi. Ndipo tsopano ndili ndi mwayi wogwira nawo ntchito yongodzipereka pa ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ya ku Germany. Ndimasangalala kwambiri chifukwa ndaphunzira kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pamoyo wanga. Kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa kwandithandiza kukhala ndi cholinga pamoyo wanga.

ZA MUNTHUYU

DZINA: TITUS SHANGADI

ZAKA: 43

DZIKO: NAMIBIA

POYAMBA: ANALI M’GULU LA ZIGAWENGA

KALE LANGA: Ndinakulira m’mudzi winawake wa ku Ohangwena, dera lomwe lili kumpoto kwa dziko la Namibia. Anthu a m’mudziwu anamenyedwa ndiponso kuphedwa panthawi ya nkhondo imene inachitika m’derali cha m’ma 1980. Ndipo m’mudzi mwathu, mnyamata amaonedwa kuti ndi mwamuna weniweni ngati ali wodziwa kumenya anzake. Choncho, ndinaphunzira luso lomenyana.

Nditamaliza sukulu ndinapita kukakhala ndi amalume anga m’tauni yotchedwa Swakopmund yomwe ili m’mphepete mwanyanja. Nditangofika m’derali, ndinalowa m’gulu linalake la achinyamata ochita zauchigawenga. Tinkapita kumalo osiyanasiyana kumene anthu akuda sankaloledwa kupitako monga m’mahotela ndiponso m’malo omwera mowa, n’cholinga choti tikayambitse ndewu. Nthawi zambiri tinkamenyana ndi alonda ndiponso apolisi. Usiku uliwonse ndinkayenda ndi chimpeni chakuthwa chachitali kapena chikwanje chokhapira wina aliyense amene ndingayambane naye.

Tsiku lina usiku tikumenyana ndi gulu lina la zigawenga, ndinatsala pang’ono kuphedwa. Munthu wina wa m’gululo anandizembera kumbuyo ndipo anangotsala pang’onong’ono kundidula mutu. Koma munthu wina wa m’gulu lathu anam’menya mpaka kukomoka. Ngakhale kuti ndinatsala pang’ono kuphedwa, ndinapitirizabe kuchita ndewu. Ndinkati ndikayambana ndi munthu wina, kaya akhale wamwamuna kapena wamkazi, nthawi zonse ineyo ndi amene ndinkayamba kuponya chibakela.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Nthawi ina ndinakumana ndi mayi wina wa Mboni za Yehova ndipo anandiwerengera lemba la Salmo 37. Iye anandiuza kuti m’buku la Chivumbulutso muli malonjezo enanso osangalatsa onena za mtsogolo. Komabe, popeza mayiyo sanandiuze malo enieni omwe pamapezeka malonjezowo, ndinapeza Baibulo, ndipo usiku wa tsiku limenelo ndinawerenga buku lonse la Chivumbulutso. Ndinasangalala kwambiri nditawerenga lonjezo lopezeka pa Chivumbulutso 21:3, 4, lomwe limanena kuti, “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” Mayi uja anabweranso ndi mnzake ndipo ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo.

Zinali zovuta kuti ndisinthe mmene ndimaganizira ndiponso khalidwe langa. Koma nditawerenga pa Machitidwe 10:34, 35, ndinazindikira kuti “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu ulionse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” Ndinayesetsanso kugwiritsa ntchito mfundo yopezeka pa Aroma 12:18, yakuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”

Ndinaphunziranso kuugwira mtima ena akandiputa ndipo ndinasiya kusuta fodya. Nthawi zambiri ndinkapemphera kwa Yehova kuti andithandize, kwinaku ndikugwetsa misozi. Koma poyamba ndinkasutabe fodya chifukwa ndimaganiza kuti ndikusuta ndudu yomaliza, ndipo ndikatha ndimapemphera. Mayi yemwe ankandiphunzitsa Baibulo uja anandithandiza kuona kufunika kopemphera kuti ndisasute fodya. Ndiponso ndinkafunika kupewa kucheza ndi anthu osuta fodya. Komanso ndinatsatira malangizo oti ndiziuza anzanga za kuopsa kosuta fodya. Zimenezi zinathandiza kwambiri kuti anzanga ogwira nawo ntchito asamandipatsenso fodya.

Pamapeto pake ndinakwanitsa kusiya kusuta fodya komanso kucheza ndi anthu amene ndinkachita nawo zinthu zoipa. Nditaphunzira Baibulo kwa miyezi 6, ndinabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndinakhulupirira kuti Mboni za Yehova zimalambira Mulungu moona nditaona kuti zimakondana mosayang’ana mtundu kapena khungu la munthu. Ndipo ngakhale ndisanabatizidwe, munthu wina wa Mboni yemwe anali mzungu anandiitanira kunyumba kwake kuti ndikadye naye chakudya. Sindinakhulupirire zimenezi chifukwa ndinali ndisanakhalepo mwamtendere ndi mzungu, ndipo sizikanatheka n’komwe kudya naye pamodzi. Tsopano zinali zotheka chifukwa ndili m’gulu la anthu okondana kwambiri la padziko lonse.

Kale, alonda ndiponso apolisi anayesetsa kuti asinthe maganizo ndiponso khalidwe langa koma analephera. Koma ndi Baibulo lokha lomwe lili ndi mphamvu zomwe zandithandiza kusintha khalidwe langa ndiponso kuti ndikhale munthu wosangalala.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Nthawi zambiri ndinkapemphera kwa Yehova kuti andithandize, kwinaku ndikugwetsa misozi”