Chipembedzo Chabwino Chimalimbikitsa Anthu Kukhala ndi Makhalidwe Abwino
CHIPEMBEDZO chabwino chimathandiza anthu kuti azikhala ndi maganizo ndiponso makhalidwe abwino. Chimalimbikitsa anthu kuti aziyesetsa kuchita zinthu zoyenera kuti akhale anthu abwino. Kodi tikudziwa bwanji kuti chipembedzo chabwino chimachita zimenezi?
Onani zimene mtumwi Paulo analembera Akhristu a mumzinda wa Korinto, ku Girisi. Mzinda umenewu unali wotchuka ndi makhalidwe oipa. Paulo anachenjeza kuti: “Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.” Ndipo Paulo anaonjezera kuti: “Ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.” (1 Akorinto 6:9-11, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Onani kuti chipembedzo chabwino chinathandiza anthu omwe anali ndi makhalidwe oipa kuti akhale oyera ndiponso olungama pamaso pa Mulungu.
Mosiyana ndi zimenezi Baibulo limachenjeza kuti: “Kudzabwera m’nthawi imene anthu sadzavomera chiphunzitso choona. Mmalomwake adzasonkhanitsa aphunzitsi ambiri kuti azinena zimene makutu awo afuna kumva kuti zigwirizane ndi zofuna zawo zokha.”—2 Timoteyo 4:3, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
Kodi zipembedzo zimene mukuzidziwa zimachita zotani pankhani imeneyi? Kodi zimalimbikitsa anthu kutsatira mfundo za m’Baibulo pankhani ya makhalidwe abwino? Kapena zimanyalanyaza malangizo omveka bwino a m’Mawu a Mulungu, n’kumangouza anthu “zimene makutu awo afuna kumva”?
Kuti mudziwe ngati chipembedzo chinachake chikubala zipatso zabwino, yankhani mafunso otsatirawa.
NKHANI: Ukwati.
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: “Ukwati uzilemekezedwa ndi onse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala okhulupirika, pakuti Mulungu adzaweruza achigololo ndi onse adama.”—Aheberi 13:4, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
FUNSO: Kodi chipembedzochi chimalimbikitsa anthu ake kuti mwamuna ndi mkazi amene akukhalira limodzi azikhala okwatirana mwalamulo?
NKHANI: Kuthetsa ukwati.
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Anthu ena atafunsa Yesu kuti afotokoze chifukwa chimene ukwati ungathere, iye anawayankha kuti: “Aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo.”—Mateyo 19:9, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
FUNSO: Kodi chipembedzochi chimatsatira malangizo a Yesu akuti ukwati ungathe ndipo munthu angakwatirenso pokhapokha ngati wina wachita chigololo?
NKHANI: Chiwerewere.
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: “Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.”—1 Akorinto 6:18, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
“Ngakhale akazi awo anasinthanitsa machitidwe a chibadwidwe pa ukwati ndi machitidwe ena. Chimodzimodzinso amuna analeka Aroma 1:26, 27, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
machitidwe a chikwati ndi akazi ndipo amafunana wina ndi mnzake. Amuna amachita zopusa ndi amuna ena, ndipo analandira mwa iwo okha chilango choyenera chifukwa cha zokhota zawo.”—FUNSO: Kodi chipembedzochi chimaphunzitsa kuti kuchita chiwerewere kapena kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndi tchimo?
NKHANI: Kulimbikitsa anthu ake kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo molimba mtima.
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: “Musayanjane ndi aliyense amene azitcha m’bale koma ali wachigololo, kapena wosusuka, kapena wopembedza mafano, kapena wonamizira anzake, woledzera kapena wopeza ndalama monyenga. Munthu wotere ngakhale kudya, osadya naye pamodzi.” (1 Akorinto 5:11, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Kodi n’chiyani chiyenera kuchitikira anthu amene amati ndi Akhristu koma amapitirizabe kuchita machimo amenewa? Baibulo limati: “Muchotse woipa uja mumpingo mwanu.”—1 Akorinto 5:13, Malembo Oyera.
FUNSO: Kodi chipembedzochi chimachotsa mumpingo munthu aliyense amene akupitirizabe kunyalanyaza mfundo za m’Baibulo?
Kodi ndi chipembedzo chiti chimene chimadziwika kuti chimatsatira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino?