Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Rahabi Anamvetsera Uthenga

Rahabi Anamvetsera Uthenga

KALEKALE, zaka 3,500 zapitazo kunali mzinda wina wotchedwa Yeriko, m’dziko la Kanani. Mu mzindawu, munkakhala mtsikana wina dzina lake Rahabi. Iye anabadwa panthawi imene Mose anatsogolera Aisiraeli kutuluka mu ukapolo ku Iguputo ndi kuwoloka pouma pa Nyanja Yofiira. Rahabi anamva zozizwitsa zimenezi ngakhale kuti zinachitika kutali ndi kumene iye ankakhala, komanso kunalibe mawailesi, ma TV kapena Intaneti. Kodi ukudziwa kuti anamva bwanji zimenezi?​— *

N’zosakayikitsa kuti anthu a paulendo ankakonda kukamba nkhani yokhudza zozizwitsa zimenezi. Pamene Rahabi ankakula, ankakumbukirabe zimene Yehova anachitira anthu ake. Komanso iye anamva zozizwitsa zina zokhudza Aisiraeli. Atatha zaka 40 ali m’chipululu, iwo analowa m’dziko la Kanani ndipo Mulungu ankawathandiza kugonjetsa adani awo. Tsopano Rahabi anamva kuti Aisiraeli amanga msasa patsidya pa mtsinje wa Yorodano.

Tsiku lina madzulo, alendo awiri anabwera kudzafuna malo ogona kunyumba ya Rahabi. Iwo ankadziwa kuti kunyumbaku kunali kogona alendo ndipo iye anawalandira. Koma usikuwo, mfumu ya mzindawo inamva kuti azondi achiisiraeli alowa mu mzindawo ndipo ali ku nyumba ya Rahabi. Choncho, mfumuyo inatumiza anthu kwa Rahabi, n’kumuuza kuti atulutse azondi amene anali m’nyumba yake. Kodi ukudziwa kuti Rahabi anali atadziwa kale kuti alendowo anali ndani?​— Nanga ukudziwa zimene iye anachita?​—

Pamene mfumu inkatumiza anthu kuti akafufuze za alendowo, Rahabi anali atadziwa kale kuti alendowo anali azondi achiisiraeli. Choncho, iye anawabisa padenga la nyumba yake n’kuuza anthu omwe anatumidwa ndi mfumuwo kuti: “Inde, amunawo anandifikira . . . ndipo mmene akadati atseke pachipata, kutada, anatuluka amunawo.” Ndiyeno Rahabi anawalimbikitsa anthuwo kuti ‘awalondole.’

Kodi ukuganiza kuti Rahabi anabisa azondiwo chifukwa chiyani?​— Iye anauza azondiwo kuti: “Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli. . . . Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m’Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka mu Iguputo.” Rahabi anali atamvanso nkhani zina zokhudza mmene Mulungu anathandizira Aisiraeli kugonjetsa adani awo.

Yehova anasangalala kwambiri chifukwa Rahabi anateteza azondiwo, monga mmene Baibulo limanenera pa lemba la Aheberi 11:31. Yehova anasangalalanso pamene Rahabi anapempha azondiwo kuti: ‘Ndakukomerani mtima ndipo mundilonjeze kuti pamene mukuwononga Yeriko, mudzapulumutsa makolo anga ndiponso abale anga.’ Azondiwo analonjeza kuti adzachita zimenezo ngati Rahabi atatsatira malangizo awo. Kodi ukudziwa malangizo amene azondiwo anamuuza?​—

Azondiwo anati: ‘Tenga chingwe chofiira ichi ndi kuchimanga pawindo la nyumba yako ndipo abale ako onse akhale m’nyumbamo. Ukachita zimenezi, aliyense sadzawonongedwa.’ Rahabi anachitadi zimene azondiwo anamuuza. Kodi ukudziwa zimene zinachitika?​—

Aisiraeli anafika kunja kwa mpanda wa Yeriko. Kwa masiku 6, iwo ankazungulira mzindawo mwakachetechete kamodzi patsiku. Koma patsiku la 7, anazungulira mzindawo maulendo 7 ndipo kenako anafuula kwambiri. Atatero, makoma a mzindawo anagwa kupatulapo nyumba yomwe inali ndi chingwe chofiira pawindo. Ndipo Rahabi ndi banja lake anapulumuka.​—Yoswa 2:1-24; 6:1-5, 14, 15, 20-25.

Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Rahabi anachita?​— Iye anamvetsera uthenga wokhudza zimene Mulungu ankachita poteteza anthu ake. Komanso Rahabi anathandiza anthu a Yehova pamene anali ndi mpata wochita zimenezo. Ndithudi, Rahabi anasankha kutumikira Yehova ndi anthu ake. Kodi iweyo udzachitanso chimodzimodzi?​— Ndikukhulupirira kuti udzatero.

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi ana, kamzereka n’kokuuzani kuti muime kuti anawo ayankhe funsolo.