Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chuma cha M’nyanja Yaikulu ya ku Central America

Chuma cha M’nyanja Yaikulu ya ku Central America

Chuma cha M’nyanja Yaikulu ya ku Central America

NGAKHALE kuti dziko la Nicaragua ndi laling’ono, lili ndi nyanja yotchedwanso Nicaragua, imene ndi yaikulu kwambiri ku Central America konse. Chochititsa chidwi n’chakuti, nyanja ya Nicaragua ikuoneka kuti ndi nyanja yokhayo yopanda mchere imene mumapezeka nsomba zikuluzikulu monga shaki, zopezeka m’nyanja za mchere. Asayansi akukhulupirira kuti nyanjayi inali yolumikizana ndi nyanja ya Pacific koma inadukana chifukwa cha kuphulika kwa chiphalaphala chotentha chapansi nthaka. Pamene mchere wa m’nyanjayi unayamba kutha, nsomba za m’nyanjayi zinayamba kuzolowera madziwo.

Nyanjayi ndi yaikulu makilomita 160 m’litali ndiponso 70 m’lifupi ndipo ndi yokwera mamita pafupifupi 30. Panyanjayi pali zilumba zoposa 400, ndipo pafupifupi zilumba 300 n’zoyandikana kwambiri ndi chilumba chachikulu cha Asese, chomwe chili pafupi ndi tauni ya Granada, imene ili kumpoto kwa nyanjayi. Ndipo zilumbazi zimatchedwa Zilumba za Granada.

Chilumba chachikulu panyanjayi chimatchedwa Ometepe ndipo chili pakati pa nyanjayi. Chilumbachi n’chachikulu makilomita 25 m’litali ndiponso makilomita 13 m’lifupi, ndipo chinapangidwa ndi zitunda ziwiri zolumikizana. Zitundazi zinapangika chifukwa cha kuphulika kwa chiphalaphala chotentha chimene chinatuluka pansi. Chitunda chachitali chotchedwa, Concepción n’chokwera mamita 1,610 kuchokera m’nyanjayi. Chitundachi, chomwe nthawi zina chimaphulika, chili kumpoto kwa chilumba cha Ometepe. Chitunda chinacho chimatchedwa Madera, ndipo n’chokwera mamita 1,394 kuchokera m’nyanja koma chinasiya kuphulika. Chitundachi chili ndi nkhalango zowirira ndiponso dziwe la madzi akuda kwambiri.

Nyanja ya Nicaragua ndi imodzi mwa zinthu zochititsa chidwi m’derali zimene zimakopa alendo. Anthu amabwera kudzaona zinthu zachilengedwe zokongola ndiponso zinthu zambiri yakale zimene zinasungidwa m’derali. Komabe, pali chinthu china chosangalatsa chomwe chili m’gulu la chuma cha nyanja ya Nicaragua chimene tiyenera kuchidziwa.

Midzi ya Pamadzi

Pa Zilumba za Granada pali zomera ndi zinyama zambiri. M’nkhalango za m’derali, zomwe ndi mbali yaikulu ya zilumbazi, nthawi zambiri mumamera maluwa okongola kwambiri. Mphepete mwa nyanjayi, mumapezeka mbalame zokongola monga akakowa, adokowe, nkhwazi ndi abakha a m’madzi. Ndipo m’mitengo ikuluikulu ya mphepete mwa nkhalangozi mumaoneka zisa za mbalame zili petupetu chifukwa cha mphepo yochokera m’nyanjayi.

Koma ku zilumba zina kumakhala anthu. Kumakhala asodzi ndiponso kuli nyumba zogona alendo opeza bwino. Komanso kuli sukulu zingapo ndi manda, malo odyera ndiponso omwera mowa. Zilumbazi zili ngati midzi yapamadzi.

Tsiku lililonse m’mawa, boti limayenda chilumba ndi chilumba kutenga ana opita kusukulu. Pamadutsanso bwato lina limene limakhala ndi zipatso ndi ndiwo zamasamba zogulitsa. Zinthu zina zimene mungaone tsiku ndi tsiku ndi monga azibambo akusodza ndiponso azimayi akuchapa.

Nawo a Mboni za Yehova amakhala otanganidwa pa zilumbazi. Amayendera anthu pabwato kuwauza za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyo 24:14) Koma chifukwa cha mmene derali lilili, panali vuto la malo ochitira misonkhano yophunzirira Mawu a Mulungu. Popeza Baibulo limanena kuti “osaleka kusonkhana kwathu pamodzi,” a Mboni za Yehova anaganiza nzeru yabwino kwambiri, yopanga Nyumba ya Ufumu yoyamba ku Nicaragua yoyandama pamadzi.​—Aheberi 10:25.

Nyumba ya Ufumu Yoyandama Pamadzi

Banja lina la Mboni za Yehova limene limagwira ntchito yolalikira Mawu a Mulungu nthawi zonse, linasamukira ku Zilumba za Granada mu November 2005. Patapita miyezi ingapo, banjali linaitanira anthu kumwambo wokumbukira imfa ya Khristu, ndipo anadabwa kuona kuti pabwera anthu 76. Zimenezi zinachititsa banjalo kuona kuti n’kofunika kuyamba kuchita misonkhano yachikhristu nthawi zonse m’deralo. Popeza malo ochitira misonkhano imeneyi anali osowa, banjalo linaganiza nzeru inayake. Iwo anaganiza zopanga Nyumba ya Ufumu yoyandama imene ingamakokedwe kupita m’madera osiyanasiyana.

Banja lakhama limeneli, lomwe linali lisanakonzepo chinthu choyandama pamadzi, linayamba ntchito yopanga Nyumba ya Ufumuyo. Iwo pamodzi ndi anthu ena 6 anagwira ntchito imeneyi kwa mwezi wathunthu. Popanga Nyumba ya Ufumuyo, iwo anagwiritsa ntchito chithabwa chachikulu chimene pansi pake analumikizapo zitsulo ndi migolo 12 yopanda kathu kuti izitha kuyandama ndipo denga lake linali la chilona. Anthuwa ankapemphera kuti Mulungu adalitse ntchitoyi chifukwa ankaganiza kuti sangakwanitse kukonza Nyumba ya Ufumu yoyandama. Koma inakwanitsadi kukonza Nyumba ya Ufumuyo.

Nyumba ya Ufumu yatsopanoyi anaigwiritsa ntchito koyamba kuchitira msonkhano pa June 10, 2006. Tsiku lotsatira, anaikokera ku mbali ina ya chilumbachi kuti anthu akumenekonso akachitiremo msonkhano ngati womwewu. Pamisonkhano iwiri yonseyi panabwera anthu okwana 48, ngakhale kuti ena mwa anthuwa anayenda ulendo woposa mphindi 30 ndiponso anadutsa m’nkhalango. Anthu onsewa anali osangalala chifukwa chokhala ndi malo awoawo olambiriramo.

Misonkhano ikamachitika m’Nyumba ya Ufumuyi anthu amasangalalanso ndi zinthu zina za m’derali. Iwo amamva kaphokoso ka madzi omwe amayenda, kudutsa m’miyala ndiponso amamva kulira kwa anyani. Anthu okhala pachilumbachi sanachedwe kuzolowera kuona Nyumba ya Ufumuyi ndipo akamaisamutsira kudera lina, anthuwo amakonda kubaibitsa. Mlungu uliwonse anthu oposa 20 amabwera ku Nyumba ya Ufumuyi kudzaphunzira Baibulo ndiponso kucheza ndi abale awo achikhristu. Ndithudi, Nyumba ya Ufumuyi ndi chuma chamtengo wapatali zedi.

Zochitika Pachilumba cha Ometepe

Chilumba cha Ometepe chili pamtunda wa makilomita 50 kum’mwera kwa tauni ya Granada. Malo amenewa ndi abwino kukhalako chifukwa kuli zinthu zokongola ndiponso nthaka yake ndi yachonde. Ndipotu pali umboni wosonyeza kuti ulimi wa ku Nicaragua unayambira kudera limeneli. Masiku ano pachilumba cha Ometepe pali anthu okwana 42,000, omwe ndi asodzi ndiponso alimi a mbewu zosiyanasiyana monga chimanga, nthochi ndiponso khofi. M’derali mulinso nyama zakuthengo zambiri. Mulinso mbalame za mtundu wina wake zaphokoso ndiponso mbalame zinazake zokongola, zomwe nthenga zake zimaoneka za buluu ndi zoyera zikamauluka. Komanso kuli anyani oyera nkhope omwe anthu ambiri amasangalala kuwaona.

Anthu a ku Ometepe amasangalalanso ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, umene Mboni za Yehova zimalalikira mwakhama kwambiri pachilumbachi. Kuyambira pa anthu 8 amene anabatizidwa mu 1966, chiwerengero cha Mboni za Yehova ku Ometepe chafika 183, ndipo kuli mipingo inayi yomwe ikukula mofulumira. Mpingo uliwonse uli ndi Nyumba ya Ufumu yakeyake. Ndipo masiku ano, pa anthu 230 aliwonse a pazilumbazi, mmodzi ndi wa Mboni za Yehova.

Kwa zaka zambiri, Mboni za Yehova za ku Ometepe zakhala zikukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, anthu odana ndi Mboni za Yehova anawotcha Nyumba ya Ufumu ya ku Mérida, m’chaka cha 1980. Kenako, Nyumba ya Ufumu ina inamangidwanso mu 1984 ndipo yakhala ikugwiritsidwa ntchito mpaka mu 2003. Koma kenako, anamanganso Nyumba ya Ufumu ina yokongola kwambiri ndipo zimenezi zinabweretsa chimwemwe chodzadza tsaya kwa anthu 60 omwe amasonkhana m’nyumbayi.

Nyumba ya Ufumu yaikulu kwambiri inamangidwa m’tauni ya Moyogalpa. Denga la nyumbayi analitalikitsa kwambiri mbali ina moti anamangako pulatifomu ya malo ochitira misonkhano ikuluikulu. Malowa, ali ndi mipando ndiponso denga. Mboni za Yehova za kuderali komanso anthu ena okhala kufupi ndi nyanja amabwera kudzachita misonkhano kumalowa. Pamisonkhano imeneyi, malo obatizira ophunzira atsopano a Yesu Khristu sasowa chifukwa amangopita ku nyanja ya Nicaragua.​—Mateyo 28:19.

Kodi N’zotheka Kuteteza Chuma cha M’nyanjayi?

Nyanja ya Nicaragua inkaoneka ngati singawonongedwe, mwina chifukwa choti ndi yaikulu. Koma masiku ano nyanjayi ikufunika kutetezedwa chifukwa madzi ake akuwonongedwa ndi alimi ndiponso zinyansi za m’mafakitale. Ndiponso anthu akudula mitengo mwachisawawa ndipo zimenezi zikuchititsa kuti nthaka izikokoloka n’kumakwirira nyanjayi.

Sizikudziwika ngati zimene anthu ndiponso boma likuchita pofuna kuteteza nyanjayi zingathandize. Ngakhale zili choncho, Mlengi adzaonetsetsa kuti chuma chonse chadzikoli, kuphatikizapo nyanja zokongola, zilumba ndiponso nyama zakutchire zochititsa chidwi, zitetezedwe kuti zidzakhale cholowa cha anthu okhulupirika. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:29.

[Chithunzi patsamba 26]

Nyumba ya Ufumu yoyandama yophunziriramo Baibulo