Kodi Muyenera Kuchita Chiyani Mukakhumudwitsidwa?
Kodi Muyenera Kuchita Chiyani Mukakhumudwitsidwa?
ANTHU ambiri amaona kuti kubwezera ndi chinthu chabwino. Zili choncho chifukwa si zachilendo kukwiya winawake akatilakwira. Chifukwa chakuti tinabadwa ndi mtima wodziwa chabwino ndi choipa, timafuna kuti munthu akatilakwira, tikonze. Koma funso n’lakuti, kodi tizikonza bwanji?
N’zoona kuti anthu angatikhumudwitse m’njira zosiyanasiyana monga kutitukwana, kutimenya, kutibera ndi zina zotero. Kodi inuyo mumatani mukalakwiridwa? Masiku ano zikuoneka kuti anthu ambiri amati, “Ndibwezera.”
Mwachitsanzo, ana ambiri a m’makalasi oyambirira a ku sekondale ku America, amasumira aphunzitsi awo powanamizira kuti anawachitira nkhanza. Iwo amachita zimenezi n’cholinga chofuna kubwezera chifukwa choti aphunzitsiwo anawapatsa chibalo. Pulezidenti wa bungwe la aphunzitsi ku New Orleans, dzina lake Brenda Mitchell, anati: “Zimenezi zimachititsa kuti mbiri ya aphunzitsi iipe kwambiri.” Ndipo mbiri yawo imaipabe ngakhale zitadziwika kuti nkhanizo n’zonama.
Komanso anthu ambiri ogwira ntchito amene sakusangalala ndi mabwana awo ndiponso amene achotsedwa ntchito amabwezera mabwanawo powononga kapena kufufuta zinthu za kampani zofunika kwambiri zomwe zili pakompyuta. Anthu ena amaba zinsinsi za kampaniyo ndi kuzigulitsa kapena kuwapatsa anthu ena. Kuwonjezera pa kuba zinthu pakompyuta, nyuzipepala ina inati: “Ogwira ntchito amakonda kubanso katundu wa kampani pofuna kubwezera.” (The New York Times) Pofuna kuthetsa mavuto amenewa, mabwana ambiri amauza alonda kuti aperekeze munthu amene wachotsedwa ntchito ku ofesi yake kuti akachotse zinthu zake zonse kenako n’kum’perekeza kuti achoke pakampanipo.
Koma nthawi zambiri anthu amakonda kubwezera akalakwiridwa ndi anzawo apamtima, odziwana nawo kapenanso achibale awo. Nthawi zambiri amafuna kubwezera wina akawalankhulira mawu opweteka kapena akawachitira zinthu mosawaganizira. Kodi inuyo mumabwezera mnzanu akakulankhulani mokhadzula? Kapena kodi mumaganiza zobwezera wachibale wanu akakukhumudwitsani m’njira inayake? N’zosavuta kubwezera ngati wakukhumudwitsaniyo ali mnzanu kapena wachibale.
Kuipa Kobwezera
Nthawi zambiri anthu amafuna kubwezera kuti mtima wawo ukhale pansi. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti ana a Yakobo, yemwe anali kholo lachiheberi, atamva kuti Sekemu, yemwe anali wachikanani wagwirira mlongo wawo Dina, ‘anapwetekwedwa mtima, nakwiya kwambiri.’ (Genesis 34:1-7) Pobwezera zinachitikazo, ana awiri a Yakobo anakonza chiwembu chopha Sekemu ndi abale ake. Simeoni ndi Levi atapusitsa amuna a mumzinda wina ku Kanani, analowa mumzindawo n’kupha Sekemu ndi amuna onse.—Genesis 34:13-27.
Kodi zimenezi zinathetsa nkhaniyo? Ayi, chifukwa Yakobo atamva zimene ana ake anachita, anawadzudzula kuti: “Mwandisautsa ndi kundinunkhitsa ine mwa anthu okhala m’dzikomu, . . . [ndipo] adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.” (Genesis 34:30) Inde, m’malo mothetsa nkhaniyo, kubwezera kunangokulitsa vutolo. Tsopano Yakobo ndi banja lake ankakhala mwamantha ndipo anayenera kusamala poopa anthu a m’mizinda yoyandikana nawo amene anakwiya ndi zimene zinachitikazo. Zikuoneka kuti pofuna kupewa zimenezi, Mulungu analangiza Yakobo ndi banja lake kuti asamukire ku Beteli.—Genesis 35:1, 5.
Zimene zinachitika Dina atagwiriridwa zikutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri. Mfundo yake ndi yakuti: Kubwezera kumayambitsa mavuto ena chifukwa munthu akabwezera, anthu enanso amam’bwezera ndipo zimenezi sizithera pomwepo. N’chifukwa chake pa Chichewa pali mwambi wakuti: Choipa chitsata mwini.
Kubwezera Sikutha
Kuganizira kwambiri zimene tingachite pofuna kubwezera wina akatilakwira n’koipa kwambiri. Pankhani imeneyi, buku lina linati: “Mkwiyo ndi woipa kwambiri. Ungawononge nthawi ndi mphamvu zanu mukamangoganizira zimene zinachitikazo ndiponso mmene mungabwezerere.” (Forgiveness—How to Make Peace With Your Past and Get On With Your Life) N’chifukwa chake Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Nsanje ivunditsa mafupa.”—Miyambo 14:30.
N’zoona kuti munthu sangasangalale ngati akusunga chakukhosi. Wolemba nkhani mu
nyuzipepala ina anati: “Ngati mukuganiza kuti ‘kubwezera n’kwabwino,’ tangoonani nkhope za anthu amene amakonda kubwezera ngati zili zosangalala.”Taganizirani zimene zakhala zikuchitika m’madera ambiri padzikoli kumene anthu amadana chifukwa chosiyana zipembedzo ndiponso mitundu. Nthawi zambiri, munthu mmodzi akaphedwa anthu amabwezera pophanso anthu ena, ndipo zimenezi sizimatha. Mwachitsanzo, m’dziko lina zigawenga zitaphulitsa bomba n’kupha achinyamata 18, mzimayi wina akulira anakuwa kuti: “Tibwezera ndipo tiwakhaulitsa!” Zikatere, anthu amapitirizabe kuphana ndipo anthu ambiri amalowerera.
“Diso Kulipa Diso”
Anthu ena amati amabwezera chifukwa cha zimene Baibulo limanena. Iwo amati, “Kodi Baibulo silimatchula mfundo yakuti ‘diso kulipa diso, dzino kulipa dzino’?” (Levitiko 24:20) Mawu akuti “diso kulipa diso” angaoneke ngati akulimbikitsa anthu kuti azibwezera. Komabe, ndi mawu oletsa kubwezera. N’chifukwa chiyani tikutero?
Ngati munthu wachiisiraeli wapweteka mnzake ndi kum’chotsa diso, m’Chilamulo munali chilango choyenera. Komabe, munthu amene wapwetekedwayo si amene ankapereka chilango kwa munthuyo kapena achibale ake. Chilamulo chinkanena kuti munthuyo akatule nkhaniyo kwa anthu oyenerera omwe anali oweruza kuti akaweruze nkhaniyo. Kudziwa lamulo lakuti munthu wachiwawa kapena wolimbikitsa zachiwawa anayenera kulangidwa mofanana ndi mmene wapwetekera mnzakeyo, kunkathandiza kwambiri kuti anthu asamabwezerane. Komanso pali zifukwa zina.
Lamulo lobwezerali lisanaperekedwe, Yehova Mulungu anauza Mose kuti auze mtundu wa Isiraeli kuti: “Usamamuda m’bale wako mumtima mwako. . . . Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi.” (Levitiko 19:17, 18) Choncho, mfundo yakuti “diso kulipa diso, dzino kulipa dzino” tiziiona mogwirizana ndi mfundo zonse za m’pangano la Chilamulo, limene Yesu ananena mwachidule m’malamulo awiri akuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse,” ndi lakuti “Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyo 22:37-40) Ndiye kodi Akhristu oona azitani ngati alakwiridwa?
Khalani Amtendere
Baibulo limati Yehova ndi “Mulungu wa mtendere” ndipo limalimbikitsa anthu amene amamulambira kuti ‘aziyesetsa kupeza mtendere ndi kuusunga.’ (Aheberi 13:20; 1 Petulo 3:11) Koma kodi zimenezi zimathandiza?
Panthawi ya utumiki wake wapadziko lapansi, Yesu anachitiridwa zinthu zambiri zachipongwe monga kulavuliridwa, kukwapulidwa, kuzunzidwa ndi adani ake, kuperekedwa ndi wophunzira wake, ndiponso kuthawidwa ndi otsatira ake. (Mateyo 26:48-50; 27:27-31) Kodi iye anatani? Mtumwi Petulo analemba kuti: “Pamene anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.”—1 Petulo 2:23.
Mtumwi Petulo anati: “Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa.” (1 Petulo 2:21) Inde, Akhristu akulimbikitsidwa kutsatira Yesu ndiponso kuchita zimene Yesu anachita pomwe anthu ankamuzunza. Ponena za nkhani imeneyi, Yesu pa ulaliki wake wa paphiri ananena kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani; kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wa kumwamba.”—Mateyo 5:44, 45.
Kodi anthu amene amatsanzira chikondi cha Khristu amatani akalakwiridwa kapena ngati akuganiza kuti wina wawalakwira? Lemba la Miyambo 19:11 limati: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.” Iwo amatsatiranso malangizo akuti: “Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:21) Izitu n’zosiyana kwambiri ndi mtima wobwezera umene ndi wofala kwambiri masiku ano. Chikondi chimene Akhristu oona amakhala nacho chimawathandiza kupewa khalidwe lobwezera ndiponso chimawathandiza ‘kukhululukira cholakwa,’ chifukwa chikondi “sichisunga zifukwa.”—1 Akorinto 13:5.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti ena akatichitira zachiwawa kapena akatiwopseza, tizingokhala osachitapo chilichonse? Ayi, sichoncho. Paulo ponena kuti, “Pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino,” sankatanthauza kuti Mkhristu azingololera chilichonse n’cholinga choti afere chikhulupiriro chake. Ngati ena akufuna kutipweteka, tili ndi ufulu wodziteteza. Ndiponso ngati mwachitiridwa zachiwawa kapena katundu wanu wabedwa, mungadziwitse apolisi. Ngati yemwe wakulakwirani ndi mnzanu wa kuntchito kapena kusukulu, mungakasume kwa anthu oyenerera kuti akuthandizeni.—Aroma 13:3, 4.
Komabe, dziwani kuti n’zovuta kupeza chilungamo chenicheni m’dziko loipali. Ndipo anthu ambiri ayesetsa kwa moyo wawo wonse kuti apeze chilungamo, koma alephera ndipo zimenezi zimangowachititsa kuti aziwawidwa mtima ndiponso azikhala okwiya nthawi zonse.
Satana amafuna kuti anthu azibwezerana zoipa n’cholinga choti azidana. (1 Yohane 3:7, 8) Choncho ndi bwino kuti tizikumbukira mawu a m’Baibulo akuti: “Okondedwa, musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu; pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’” (Aroma 12:19) Tikasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova, timapewa kuwawidwa mtima, kukwiya ndiponso chiwawa.—Miyambo 3:3-6.
[Mawu Otsindika patsamba 22]
“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse” ndiponso “Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha”
[Zithunzi patsamba 23]
Chikondi “sichisunga zifukwa.”—1 Akorinto 13:5