Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pamene Ananena Kuti Iye ndi Atate Ake Ndi Amodzi?

Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pamene Ananena Kuti Iye ndi Atate Ake Ndi Amodzi?

Panthawi ina Yesu anati: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” (Yohane 10:30) Ena amagwiritsa ntchito lembali polimbikitsa chiphunzitso choti Yesu, Atate ndiponso Mzimu Woyera amapanga Mulungu mmodzi. Komano kodi Yesu ankatanthauza zimenezo ponena mawu amenewa?

Tiyeni tione nkhani yonse m’chaputala chomwe muli lembali. Mu vesi 25, Yesu ananena kuti ntchito zimene iye ankachita, ankazichita m’dzina la Atate wake. Kenako, mu vesi 27 mpaka 29 anafotokoza za nkhosa zophiphiritsira zomwe Atate wake anamupatsa. Zikanakhala kuti iye ndiponso Atate ake ndi munthu mmodzi, mfundo ziwirizi zikanakhala zosamveka. M’malomwake, pamenepa Yesu ankatanthauza kuti, ‘Atate wanga ndi ineyo ndife anthu ogwirizana kwambiri moti palibe amene angandilande nkhosa za Atate, monga mmenenso zilili kuti palibe amene angawalande Atate nkhosazi.’ Zimenezi zili ngati mwana akuuza adani a bambo ake kuti, ‘Ngati mukulimbana ndi bambo anga, ndiye kuti mukulimbana ndi ineyo.’ Choncho, munthu sanganene kuti mawu amenewa akutanthauza kuti mwana ndiponso bambo akewo ndi munthu mmodzi. Koma angathe kuona kuti anthu awiriwa amagwirizana kwambiri.

Pali chifukwa chinanso chomwe tinganenere kuti Yesu ndiponso Atate wake, omwe ndi Yehova Mulungu, ndi “amodzi.” Iwo amagwirizana kwambiri pa zolinga, mfundo ndiponso zokonda zawo. Ndipo mosiyana ndi Satana Mdyerekezi komanso Adamu ndi Hava, Yesu sanaganizepo zofuna kumadzilamulira yekha. Iye anafotokoza kuti: “Mwanayo sangachite chilichonse chongoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita. Pakuti zilizonse zimene Atateyo amachita, Mwana amachitanso zofananazo.”​—Yohane 5:19; 14:10; 17:8.

Komabe kugwirizana kumeneku sikukutanthauza kuti Mulungu ndi Mwana wake, Yesu, ndi munthu mmodzi. Iwo ndi anthu awiri osiyana. Aliyense ali ndi umunthu wakewake. Yesu amaganiza ndiponso kuona zinthu mogwirizana ndi umunthu wake komanso anakumana ndi zinthu zosiyanasiyana pamoyo wake, monga munthu payekha. Ndiponso, iye ali ndi ufulu wosankha zinthu. Komabe iye amasankha kugonjera zimene Atate wake amafuna. N’chifukwa chake palemba la Luka 22:42, Yesu anati: “Chifuniro chanu chichitike, osati changa.” Mawu amenewa akanakhala opanda tanthauzo zikanakhala kuti iye sangathe kusankha zinthu, zosiyana ndi za Atate wake. Ndipo zikanakhala kuti Yesu ndiponso Atate wake ndi munthu mmodzi, n’chifukwa chiyani Yesu ankapemphera kwa Mulungu? Nanga n’chifukwa chiyani iye ananena modzichepetsa kuti panali zinthu zina zimene sankazidziwa, koma Atate wake yekha?​—Mateyo 24:36.

Anthu a m’zipembedzo zambiri amalambira milungu yomwe amaisonyeza kuti imakangana komanso kumenyana ndi achibale awo. Mwachitsanzo, nthano ina ya Chigiriki imafotokoza kuti mulungu winawake, dzina lake Cronus, analanda ufumu bambo ake, a Uranus. Nthanoyo imanenanso kuti kenako Cronus anapha ana ake n’kuwadya. Zimenezitu n’zosiyana kwambiri ndi Yehova Mulungu ndiponso Mwana wake, Yesu, omwe amagwirizana kwambiri chifukwa chokondana mochokera pansi pa mtima. Chikondi chimenecho chimatichititsanso kuti tiziwakonda kwambiri. Ndipotu ifeyo tili ndi mwayi wosaneneka, wogwirizana ndi anthu awiri amenewa, omwe ndi apamwamba kwambiri m’chilengedwe chonse. Yesu anapempherera otsatira ake kuti: ‘Ndikupemphera kuti onsewa akhale amodzi, mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana wina ndi mnzake, kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife.’​—Yohane 17:20, 21.

Choncho, pomwe Yesu ananena kuti: “Ine ndi Atate ndife amodzi,” sankanena za chiphunzitso chovuta kumva chakuti iye, Atate ndiponso Mzimu Woyera ndi Mulungu mmodzi. M’malomwake ankatanthauza kuti iyeyo ndiponso Atate wake ndi ogwirizana kwambiri.