Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zingathandize Amishonale Kuti Zinthu Ziwayendere Bwino

Zimene Zingathandize Amishonale Kuti Zinthu Ziwayendere Bwino

Mwambo Womaliza Maphunziro a Gileadi​—Gulu la Nambala 126

Zimene Zingathandize Amishonale Kuti Zinthu Ziwayendere Bwino

LOWERUKA, pa March 14, 2009, gulu la anthu lomwe linali losangalala kwambiri linasonkhana ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, New York. Tsikuli linali lapadera kwambiri chifukwa linali lochita mwambo womaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Anthu omwe anamaliza maphunzirowo anali oti atumizidwe m’mayiko 22, kuti azikagwira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.​—Mateyo 24:14.

Ophunzirawo anali atangomaliza kuphunzira Baibulo mwakathithi kwa miyezi isanu. Maphunzirowa anachitika n’cholinga chowathandiza kuti zinthu zikawayendere bwino pa utumiki wawo wa umishonale. Ndipo patsikuli, iwo anali ndi mwayi winanso woti alandire malangizo ena ofunika kwambiri pa umishonale wawo.

Anthony Morris, yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anali tcheyamani wa mwambowu. Iye anafotokoza kuti Sukulu ya Gileadi yakhala ikuphunzitsa amishonale kuyambira mu 1943. Anafotokozanso kuti kuyambira nthawi imeneyo, amishonale omwe amaliza maphunziro kusukuluyi akhala akuthandiza kwambiri pantchito yolalikira padziko lonse.

M’bale Morris anafotokozanso kuti alembi ndi Afarisi ankanyoza atumwi a Yesu kuti anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” Komabe iwo anazindikira kuti atumwiwo anakwanitsa kulankhula molimba mtima chifukwa ankayenda ndi Yesu. (Machitidwe 4:13) Motero, iye anena kuti zimene amishonalewo anaphunzira n’zowathandiza kulankhula molimba mtima.

Kenako, Robert Ciranko, yemwe ndi wothandizira Bungwe Lolamulira, m’Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku, anakamba nkhani yamutu wakuti, “Musakhale Okondera.” Iye ananena kuti ophunzirawo azikakumana ndi anthu a zikhalidwe ndiponso miyambo yosiyana kwambiri ndi yawo. Komabe, iwo sangakavutike kuwalalikira ngati atakhala ndi maganizo ofanana ndi a Yehova. Lemba la Machitidwe 10:34, limati “Mulungu alibe tsankho,” kapena kuti “Mulungu si wokondera.” (Machitidwe 10:35) Choncho, M’bale Ciranko anafotokoza kuti: “Mukakhala ndi maganizo ngati a Mulungu, n’kumaona munthu aliyense m’gawo lanu kuti Mulungu akhoza kumulandira, zinthu zidzakuyenderani bwino.”

“Muli Ndi Zonse Zofunikira”

Kenako Samuel Herd, yemwenso ndi wa m’Bungwe Lolamulira, anayamba kukamba nkhani yake ndi mawu akuti: “Ena amati ngamila ndi yonyansa, komatu ili ndi zonse zofunikira kuti izitha kukhala bwinobwino m’chipululu.” Iye anafotokoza kuti, mofanana ndi ngamila, amishonale atsopanowo anali ndi zonse zofunikira kuti ntchito yawo ikayende bwino m’madera omwe angawatumize. Ndipo anafotokozanso kuti zinthu zisanu zotsatirazi zingakawathandize kwambiri.

1. Kukonda Yehova. (Mateyo 22:37, 38) Ophunzirawo anasonyeza kale kuti ndi ofunitsitsa kutumikira Yehova.

2. Kusunga mfundo za m’Mawu a Mulungu zomwe aphunzira. Ngamila imasunga chakudya chake m’mafuta omwe amakhala mkati mwa linunda lake. Koma sikuti ngamila imasiya kudya n’kumangodalira chakudya chosungidwa m’linundacho. Nawonso amishonale asamangodalira mfundo zimene anaphunzira ku Sukulu ya Gileadi, koma ayenera kupitiriza kudya chakudya chauzimu.

3. Kukonda anthu. (Mateyo 22:39) Ophunzirawo azimvera chifundo anthu.

4. Mtima wodzipereka. (Salmo 110:3) Amishonalewo akafooka, Yehova adzawalimbitsa powapatsa mphamvu zambiri.​—Yesaya 40:29.

5. Mphamvu zawo. Mofanana ndi mmene ngamila imasonyezera mphamvu ponyamula munthu kudutsa m’chipululu, amishonalewo ayeneranso “kunyamula” Akhristu anzawo amene ali ndi mavuto auzimu. Ngakhale kuti kuchita zimenezi kungafune nyonga zambiri, amishonalewo angakwanitse chifukwa adakali achinyamata.

Nkhani Zina za Pamwambowu

Michael Burnett, yemwe ndi mphunzitsi wa sukulu ya Gileadi, ananena kuti zipatso za katungulume kapena kuti amondi zinali zina mwa zinthu zamtengo wapatali zimene Yakobo anatumiza monga mphatso kwa mfumu ya ku Iguputo. (Genesis 43:11) Chipatso cha amondi, ngakhale kuti n’chaching’ono zedi, n’chopatsa thanzi kwambiri. Ndipo panthawi imene ophunzirawo ankachita maphunziro awo, zinali ngati kuti akudya zipatso zambiri za amondi. Zina mwa mfundo zimene iwo anaphunzira n’zoti azikwaniritsidwa ndi zimene Yehova amawapatsa ndiponso azikonda malo amene atumizidwa.

Mark Noumair, yemwenso ndi mphunzitsi wa sukulu ya Gileadi, ananena kuti Mawu a Mulungu ali ngati “thumba lodzaza ndi nzeru.” (Yobu 28:18, NW) Tifunika kumasula thumba limeneli kuti tigwiritse ntchito nzeru zake. Ngati amishonalewo ataona kuti zimene akukumana nazo mu utumikiwo n’zosiyana ndi zimene ankayembekezera, angachite bwino kuganizira za mtumwi Paulo. Ophunzira a Yesu anatumiza Paulo ku tauni yakwawo, komwe anakhalako zaka 9, ndipo ankachokera kumeneko n’kumapita kumadera ena. M’malo moganiza kuti iye “ndi chiwiya chosankhika,” ndipo anayenera kukatumikira kudera lina, Paulo anatumikira mwakhama kulikonse kumene anatumizidwa. (Machitidwe 9:15, 28-30) Nthawi zina zingakhale zovuta kuchita zimene Yehova watiuza. Winanso amene anachita zinthu mosanyinyirika anali Yonatani. Iye ankathandiza Davide modzipereka chifukwa ankadziwa kuti Davideyo anali munthu amene Yehova anam’sankha kuti adzakhale mfumu.

M’nkhani yamutu wakuti, “Atumiki a Mulungu Amayankhula Molimba Mtima,” ophunzirawo anachita zitsanzo zosonyeza zinthu zimene ankakumana nazo polalikira panthawi ya maphunzirowo. Ambiri mwa ophunzirawo anapeza anthu ambiri amene anayamba kuphunzira nawo Baibulo. Nkhani yotsatira inali yakuti, “Kuphunzitsidwa ndi Gulu la Yehova,” ndipo inali ndi mbali yomwe anafunsa mafunso amishonale atatu omwe achita utumikiwu kwa nthawi yaitali. Aliyense anafotokoza mmene anaphunzitsidwira kuchita zinthu mogwirizana ndi gulu la Mulungu.

“Mukhale Amishonale Osangalala”

M’bale winanso yemwe ali m’Bungwe Lolamulira, dzina lake Gerrit Lösch, anakamba nkhani yaikulu pamwambowu, yamutu wakuti, “Mukhale Amishonale Osangalala.” Iye ananena kuti zinthu zambiri zimene anthu amaona kuti “n’zosangalatsa” sizibweretsa chimwemwe chenicheni. (Miyambo 14:13; Mlaliki 2:10, 11) Koma anthu amakhala ndi chimwemwe chenicheni akamachita chifuniro cha Mulungu, ngakhale kuti kuchita zimenezi nthawi zina kumavuta. Sukulu ya Gileadi imafunika khama kwambiri, komabe maphunzirowo amathandiza munthu kukhala wosangalala kwambiri.

Pali zinthu zambiri zimene zimathandiza Akhristu oona kukhala osangalala. Choyamba, iwo amalambira Mulungu yemwe ndi wachisangalalo. (Salmo 33:12; 1 Timoteyo 1:11) Chachiwiri, iwo akukhala m’paradaiso wauzimu, ndipo Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa, dziko lonse lapansili lidzakhala paradaiso. Komanso, iwo akudziwa cholinga cha moyowu, chomwe ndi kutumikira ndiponso kutamanda Yehova. Koposa zonsezi, Akhristu oona amakhala osangalala chifukwa amakondedwa ndi Yehova ndiponso Yesu.

M’bale Lösch ananenanso kuti, “Mungakhale amishonale osangalala ngati mungaphunzire kukhala okhutira ndi zomwe muli nazo.” Kukondana ndi anthu ena n’kofunikanso kuti amishonale akhale osangalala. Motero, ndibwino kunyalanyaza zimene ena atilakwira, m’malo mozikulitsa. Iye anawalimbikitsa kuti azichitira zabwino anthu ena, azithandiza ofooka ndiponso azikambirana nawo nkhani zolimbikitsa. (Salmo 41:1, 2; Machitidwe 20:35) Amishonalewo angakhalenso osangalala ngati atamagwira nawo mwakhama ntchito yolalikira.​—Luka 11:28.

M’bale Lösch anamaliza nkhani yake ndi mawu akuti: “Pitani monga amishonale osangalala. Muzikapeza nthawi yochita zinthu zina zosangalatsa, koma ntchito yanu yaikulu ikhale kutamanda Yehova, yemwe ndi Mulungu wachisangalalo. Cholinga chanu chikhale kuthandiza anthu ena kuti akhalenso osangalala.”

Atamaliza kupereka moni wochokera m’mayiko osiyanasiyana, M’bale Anthony Morris anapereka zikalata kwa ophunzirawo zosonyeza kuti amaliza maphunziro awo. Kenako, mmodzi mwa ophunzirawo, anawerenga kalata yawo yopita ku Bungwe Lolamulira. M’kalatayo, iwo anayamikira kwambiri gulu la Yehova chifukwa chowapatsa mwayi wochita nawo maphunziro a ku Sukulu ya Gileadi.

Pomaliza, tcheyamani wa mwambowu anafotokoza kuti, “Minyewa imene imalumikiza mafupa” tingaiyerekezere njira imene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amagwiritsa ntchito potsogolera ndiponso kupereka chakudya chauzimu kwa anthu a Yehova. (Akolose 2:18, 19; Mateyo 24:45) Amishonalewo utumiki wawo ungawayendere bwino ngati atamachita zinthu mogwirizana ndi anthu omwe Mulungu wawapatsa udindo wotsogolera m’gulu lake.​—2 Timoteyo 4:5.

[Bokosi patsamba 30]

ZA OPHUNZIRAWO

Chiwerengero cha mayiko amene ophunzira achokera: 6

Chiwerengero cha mayiko amene atumizidwa: 22

Chiwerengero cha ophunzira: 56

Chiwerengero cha mabanja: 28

Avereji ya zaka za kubadwa: 32.8

Avereji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 17.9

Avereji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 13.5

MAYIKO AMENE OPHUNZIRAWA ATUMIZIDWA

Anthu omaliza maphunzirowa anatumizidwa ku mayiko otsatirawa: Benin, Bolivia, Bulgaria, Burkina Faso, Cameroon, Costa Rica, Ghana, Guatemala, Honduras, Kenya, Liberia, Madagascar, Mozambique, Nicaragua, Panama, Paraguay, Peru, Romania, Sierra Leone, South Africa, Togo, ndi Uganda.

[Chithunzi patsamba 31]

Gulu la Nambala 126 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pam’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mumzera uliwonse mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja.

(1) Kirchhoff, K.; Nichols, C.; Guzmán, Y.; Coil, H.; Becker, O.; De Simone, A. (2) Manzanares, A.; Bouvier, E.; Peddle, J.; Mason, H.; Braz, J. (3) Lee, J.; Forte, A.; Boucher, T.; Marsh, A.; Leighton, S.; Glover, M. (4) Kambach, H.; Jones, T.; Ferreira, A.; Morales, J.; Chicas, S.; Davis, B.; Dormanen, E. (5) Dormanen, B.; Nichols, J.; Pacho, T.; Titmas, L.; Bouvier, E.; Kirchhoff, A. (6) Leighton, G.; Pacho, A.; Van Campen, B.; Manzanares, A.; Rivard, A.; Lee, Y.; Titmas, L. (7) Boucher, M.; Coil, K.; Marsh, C.; Guzmán, J.; Jones, W.; Kambach, J. (8) Glover, A.; Ferreira, G.; Mason, E.; Forte, D.; Davis, N.; Chicas, O.; Rivard, Y. (9) Braz, D.; Van Campen, D.; Morales, A.; De Simone, M.; Becker, M.; Peddle, D.