Kodi N’zotheka Kuyamba Kukhulupirira Mlengi?
Kodi N’zotheka Kuyamba Kukhulupirira Mlengi?
MUNTHU wina yemwe poyamba ankakhulupirira kuti kulibe Mulungu, komanso yemwe abale ake anaphedwa mwankhanza mu ulamuliro wa Anazi, ananena kuti: “Ndinkakwiya kwambiri ndikaganizira kuti mwina kuli Mlengi amene ali ndi mphamvu zoti angathetse mavuto a anthu koma sazigwiritsa ntchito.” Ndipotu pali anthu ambiri amene amaganizanso choncho.
Mwachitsanzo anthu ambiri akakumana ndi mavuto, zimawavuta kukhulupirira Mulungu ndipo ena pofuna kuti mtima wawo ukhale pansi, amangoti kulibe Mulungu. Kodi ndi zifukwa zikuluzikulu ziti zimene zimachititsa anthu ena kuti asamakhulupirire Mulungu? Kodi zinthu zingayende bwino popanda kudalira Mulungu kapena ngati anthu atasiya kupemphera, monga mmene ena amaganizira? Nanga kodi zingatheke kuti anthu amene amakhulupirira kuti kulibe Mulungu, ayambe kukhulupirira Mlengi wathu wachikondi?
Zipembedzo Zalephera
N’zodabwitsa kuti zipembedzo ndi zimene zimalimbikitsa anthu kwambiri kuti azikhulupirira kuti kulibe Mulungu. Katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Alister McGrath, ananena kuti: “Chifukwa chachikulu chimene chikuchititsa anthu ambiri kuti azikhulupirira kuti kulibe Mulungu n’choti amanyansidwa ndi zipembedzo chifukwa zikulephera kulimbikitsa makhalidwe abwino.” Nthawi zambiri anthu amaona kuti zipembedzo ndi zimene zimalimbikitsa nkhondo ndiponso chiwawa. Munthu wina amene amakhulupirira kuti kulibe Mulungu, yemwenso ndi katswiri wa maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba, dzina lake Michel Onfray, anadabwa kuti anthu ena amayesetsa kuchita zabwino pamene ena amachita nkhanza kwambiri, monga za uchigawenga, koma onsewo akutsatira mfundo za m’buku limodzi la chipembedzo.
Anthu ambiri amakhumudwa akakumbukira kuti poyamba anali m’chipembedzo chinachake. Mwachitsanzo, panthawi imene anali msilikali, mnyamata wina wa ku Sweden, dzina lake Bertil anamva mtsogoleri wina wachipembedzo amene ankachititsa mwambo wa mapemphero m’gulu lawo, akunena kuti palibe cholakwika chilichonse ndi kumenya nkhondo. Mtsogoleri wa chipembedzoyu ananena zimenezi pogwira mawu a Yesu akuti onse ogwira lupanga adzawonongedwa ndi lupanga. Iye ananena kuti payenera kukhala winawake woti awononge wogwira lupangayo, choncho asilikaliwo akugwira ntchito ya Mulungu.—Mateyo 26:52. *
Mayi wina dzina lake Bernadette, amene bambo ake anaphedwa ku France, panthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, amakumbukira kuti anakwiya kwambiri ndi zimene wansembe wina ananena pa maliro a msuweni wake wa zaka zitatu. Wansembeyo ananena kuti, “Mulungu watenga mwanayu kuti akakhale mngelo.” Patapita nthawi, Bernadette anabereka mwana wolumala ndipo panthawi imeneyinso, anthu a m’tchalitchi chake sanabwere kudzamuona ndi kumulimbikitsa.
Nayenso bambo wina dzina lake Ciarán, yemwe anakulira ku Northern Ireland, panthawi imene kunkachitika nkhondo, ankadana kwambiri ndi chiphunzitso chakuti anthu oipa amakapsa kumoto. Chifukwa cha zimenezi, iye ankanena mosapita m’mbali kuti amadana ndi Mulungu amene amaotcha anthuyo ndipo ankachita kunena kuti, “Ngatidi kuli Mulungu, abwere adzandiphe.” Si Ciarán yekha amene amadana ndi ziphunzitso zonyenga zimene matchalitchi amaphunzitsa. Ndiponso zikuoneka kuti ziphunzitso za matchalitchi n’zimene zinachitisa kuti anthu ayambe kukhulupirira kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina. Alister McGrath anafotokozanso kuti Darwin anayamba kukayikira kwambiri kuti kuli Mulungu chifukwa choipidwa ndi chiphunzitso chakuti anthu oipa amakapsa kumoto, osati chifukwa cha zimene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina. McGrath ananenanso kuti chinthu chinanso chimene chinachititsa kuti Darwin azikayikira kuti kuli Mulungu ndi “chisoni chachikulu chimene iye anali nacho chifukwa cha imfa ya mwana wake wamkazi.”
Anthu ena amaona kuti anthu amene amapembedza Mulungu saganiza bwino ndiponso amachita zinthu motengeka. Mayi wina dzina lake Irina,
yemwe ankanyansidwa ndi maulaliki opanda tanthauzo komanso mapemphero ongobwerezabwereza a ku chipembedzo chake, ananena kuti: “Ndinkaona kuti anthu amene amakonda zopemphera saganiza bwino.” Ndipo bambo wina dzina lake Louis, yemwe ankanyansidwa kwambiri ndi nkhanza zimene anthu okonda kupemphera ankachita, anaonanso zinthu zina zoipa kwambiri zimene zipembedzo zinkachita. Iye anati: “Kwa zaka zambiri ndinkangoona kuti zipembedzo ndi zotopetsa koma ndinazindikiranso kuti zipembedzo zingachititse anthu kuchita zinthu zoipa kwambiri. Choncho, ndinayamba kudana kwambiri ndi zipembedzo.”Kodi Zinthu Zingayende Bwino Popanda Kudalira Mulungu?
N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amaona kuti zipembedzo zimachititsa kuti zinthu zisamayende bwino ndiponso kuti anthu azisowa mtendere. Mpaka ena amaona kuti mwina zinthu zingamawayendere bwino popanda kukhala m’chipembedzo ndiponso kudalira Mulungu. Komabe, kodi maganizo amenewa sangabweretse mavuto ena?
Katswiri wina wa maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba, dzina lake Voltaire, yemwe anakhalako m’zaka za m’ma 1700, ankadana kwambiri ndi chinyengo chimene tchalitchi chinkachita m’nthawi imeneyo. Komabe, iye ankaona kuti kukhulupirira Mulungu n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi makhalidwe abwino. Patapita nthawi, katswiri winanso wa maphunziro omwewa, wa ku Germany, dzina lake Friedrich Nietzsche, ankaphunzitsa kuti Mulungu ndi wakufa. Komabe iye ankaopa kuti chiphunzitso chimenechi chingachititse anthu kukhala ndi makhalidwe oipa kwambiri. Koma kodi mantha amenewa anali omveka?
Munthu wina wolemba mabuku, dzina lake Keith Ward, ananena kuti chakumayambiriro kwa nthawi yathu ino, zinthu zoipa monga nkhanza, “zinawonjezeka kwambiri kuposa kale.” Komanso chikhulupiriro choti kulibe Mulungu sichinathandize kuthetsa makhalidwe oipa amene anthu amakhala nawo mwachibadwa, monga kusalolerana. Zimenezi zachititsa anthu ambiri, kuphatikizapo amene amakhulupirira kuti kulibe Mulungu, kuona kufunika kokhulupirira Mulungu.
Keith Ward ananenanso kuti ndi bwino kukhulupirira Mulungu. Iye anati: “Chikhulupiriro chimathandiza kuti munthu azikhala ndi makhalidwe abwino ndiponso chimam’thandiza kuona kuti ali ndi udindo wosamalira dziko limene Mulungu analenga.” Zimene anthu osiyanasiyana apeza pa kafukufuku wa posachedwapa zasonyeza kuti anthu ambiri opemphera amaona kufunika kokhala ndi mtima wothandiza ena. Ndipo mtima umenewu umathandiza munthu kukhala wachimwemwe. Kafukufuku ameneyu akugwirizana ndi mfundo ya Yesu yakuti: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Munthu wina amene poyamba ankakhulupirira kuti kulibe Mulungu, komanso ankagwira ntchito yothandiza anthu, anachita chidwi kwambiri ndi mmene Baibulo limasinthira moyo wa munthu. Iye ananena kuti: “Ndatha zaka zambirimbiri ndikugwira ntchito yothandiza anthu kusiya khalidwe lawo loipa, koma zimenezi sizinathandize kwenikweni. Komabe, panopo ndadabwa kuona mmene Baibulo limasinthira kwambiri moyo wa munthu. Ndipo munthu akasintha ndiye kuti wasinthiratu.”
Komabe, anthu ena amene amakhulupirira kuti kulibe Mulungu amaona kuti m’malo mothandiza anthu kuti azichitirana chifundo, anthu amene amakhulupirira Mulungu ndi amene amayambitsa nkhondo ndiponso kuchititsa kuti anthu ambiri aphedwe mwankhanza. Anthu amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu angaonenso kuti chikhulupiriro chimathandiza anthu ena kuchita zinthu zabwino, komabe iwo amakayikirabe zoti kuli Mulungu. Koma kodi n’chifukwa chiyani amakayikira?
Zinanso Zimene Zimachititsa Kuti Azikayikira
Anthu ambiri amaphunzitsidwa kuti mfundo yakuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina ndi yoona. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Anila, amene anaphunzira sukulu ku Albania, komwe anthu ambiri amakhulupirira kuti kulibe Mulungu, ananena kuti: “Kusukulu tinaphunzira kuti anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu
ndi osachangamuka ndiponso otsalira. Ngakhale kuti nthawi zambiri tinkaphunzira za zinthu zochititsa chidwi monga zomera ndiponso zinthu zina zamoyo, tinkaona kuti zonsezo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina ndipo maganizo amenewa ankathandiza kuti tizioneka kuti tikugwirizana ndi asayansi.” Komabe panopo iye amavomereza kuti: “Tinkangokhulupirira zimene ankatiphunzitsazo popanda kufufuza bwinobwino.”Anthu ena amalephera kukhulupirira Mulungu chifukwa chokhumudwa ndi zinthu zina. A Mboni za Yehova nthawi zambiri amakumana ndi anthu oterewa akamagwira ntchito yawo yolalikira khomo ndi khomo, pofuna kuthandiza anthu kuti ayambe kukhulupirira zimene Baibulo limalonjeza. Bertil, amene tamutchula poyamba uja, anachezeredwa ndi wa Mboni wina wachinyamata. Ataona wa Mboniyo, Bertil ananena mumtima mwake kuti: ‘Koma ndiye wafika pakhomo pa munthu wolakwikatu.’ Iye ananena kuti: “Ndinamuuza kuti alowe m’nyumba ndipo ndinayamba kumuuza mokalipa kuti ndimakhulupirira kuti kulibe Mulungu, sindikhulupirira Baibulo ndiponso kuti ndimadana ndi zipembedzo.”
Ndiponso bambo wina wa ku Scotland, dzina lake Gus, sankasangalala ndi zinthu zopanda chilungamo zimene zinkachitika. Poyamba ankachita makani ndiponso kutsutsa kwambiri zimene a Mboni za Yehova ankamuphunzitsa. Gus ankafunsa mafunso ofanana ndi amene mneneri wachiheberi, dzina lake Habakuku, anafunsa Mulungu kuti: “Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta?”—Habakuku 1:3.
Kwa nthawi yaitali, anthu akhalanso akuvutika maganizo chifukwa choona ngati Mulungu sizimukhudza anthu akamavutika. (Salmo 73:2, 3) Munthu wina wolemba mabuku wa ku France, dzina lake Simone de Beauvoir, ananena kuti: “Zinali zomveka kukhulupirira kuti kulibe Mulungu kusiyana ndi kukhulupirira kuti alipo koma n’kumaona mavuto ambiri padzikoli.”
Komabe, kulephera kwa zipembedzo kufotokoza chifukwa chake pali mavuto amenewa, sikukutanthauza kuti palibiretu amene angafotokoze. Gus ananena kuti pamapeto pake iye anapeza “mayankho othandiza onena za chifukwa chimene Mlengi, amene ndi Wamphamvuyonse, amalolera kuti anthu azivutika. Zimenezi zinandithandiza kwambiri.” *
N’kutheka kuti anthu ena amene amakhulupirira kuti kulibe Mulungu amakayikiranso zoti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina. Iwo angazindikire kuti afunika kukhulupirira Mulungu, mwinanso angamapemphere kwa Mulungu paokha. Tiyeni tione zimene zinachititsa anthu ena okhulupirira kuti kulibe Mulungu komanso ena amene ankakayikira ngati Mulungu alipodi, kuti aganizirenso bwino za nkhaniyi kenako n’kukhala paubwenzi ndi Mlengi wawo.
Kodi Chinawathandiza N’chiyani Kuti Ayambe Kukhulupirira Mlengi?
Mnyamata amene anafika pakhomo pa Bertil uja anamufotokozera momveka bwino kuti pali kusiyana kwambiri pakati pa Akhristu oona ndi anthu amene amangodzitcha kuti ndi Akhristu. Bertil anafotokoza zimene zinamuchititsa chidwi kwambiri kuwonjezera pa mfundo zimene anauzidwa zotsimikizira kuti kuli Mlengi. Iye ananena kuti: “Ndinachita chidwi kwambiri ndi khalidwe la mnyamatayu chifukwa ankaugwira mtima kusiyana ndi khalidwe langa lokonda kuchita makani. . . . Iye ankachita zinthu modekha kwambiri ndipo nthawi zonse ankandibweretsera mabuku ndipo ankakonzekera bwino podzandiphunzitsa.” *
Mayi wina, dzina lake Svetlana, amene ankakhulupirira kwambiri mfundo zachikomyunizimu ndiponso amene ankakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusanduka ku zinthu zina, ankakhulupiriranso kuti zinthu zamoyo zimene zili ndi mphamvu kwambiri ndi zimene ziyenera kupitiriza kukhala ndi moyo. Komabe, iye ankavutika maganizo kwambiri ndi mfundo imeneyi. Ndiponso zimene anaphunzira kusukulu yophunzitsa udokotala zinamusokonezanso maganizo kwambiri. Iye anati: “Panthawi imene tinkaphunzira zoti kulibe Mulungu, tinaphunziranso kuti zamoyo zokhazo zimene zili ndi mphamvu kwambiri n’zimene ziyenera kupitiriza kukhala ndi moyo. Koma panthawi ya phunziro la zamankhwala, tinaphunzira kuti tifunika kuthandiza anthu ofooka.” Iye sankamvetsanso kuti n’chifukwa chiyani anthu, omwe amati anachokera ku anyani, amavutika maganizo pamene anyaniwo savutika n’komwe. Amene anam’thandiza kupeza mayankho a mafunso amenewa ndi munthu amene iye sankamuyembekezera n’komwe. Iye anati: “Agogo anga anandifotokozera kuchokera m’Baibulo kuti anthufe timakumana ndi mavuto amenewa chifukwa choti ndife opanda ungwiro.” Svetlana anasangalalanso kwambiri atadziwa kuchokera m’Baibulo chifukwa chake anthu osalakwa amavutika.
Komanso bambo wina wa ku Scandinavia, dzina lake Leif, ankakhulupirira kwambiri kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina komanso ankaona kuti nkhani za m’Baibulo ndi zongopeka. Komabe, tsiku lina mnzake anamufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti umangokhulupirira zimene ena akuuza popanda kuona zimene Baibulo limanena?” Pofotokoza mmene funsoli linam’khudzira, Leif anati: “Ndinazindikira kuti ndinkangokhulupirira zimenezi popanda kufufuza. . . . Ndikuona kuti munthu amene amakhulupirira kuti kulibe Mulungu angayambe kukhulupirira ngati atadziwa zinthu monga maulosi a m’Baibulo ndiponso kukwaniritsidwa kwake.”—Yesaya 42:5, 9.
Ciarán, amene tamutchula poyamba uja, anachita nawo za ndale kwa zaka zambiri koma sizinam’thandize kupeza chimwemwe. Pomwe ankaganizira za moyo wake, anakumbukira mfundo yakuti: Mulungu wachikondi ndiponso wamphamvuyonse ndi amene angathetse mavuto padzikoli ndiponso mavuto amene iye akukumana nawo. Chamumtima, iye anati: ‘Ndikulakalaka nditamudziwa Mulungu ameneyu.’ Atathedwa nzeru kwambiri anapemphera kuti: “Ngati mulipo ndipo mukundimva, chonde ndithandizeni kuthetsa mavuto anga ndiponso a anthu onse.” Patapita masiku angapo, munthu wina wa Mboni za Yehova anafika panyumba pake. Wa Mboniyo anafotokoza zimene Baibulo limanena zakuti Satana ndi amene amachititsa kuti olamulira adzikoli azichita zoipa. (Aefeso 6:12) Ciarán anagwirizana nayo mfundo imeneyi ndipo inamulimbikitsa kuti akhale ndi chidwi chofuna kudziwa zambiri. Ataphunzira Baibulo kwa kanthawi, anayamba kukhulupirira kwambiri Mlengi.
Khalani Paubwenzi ndi Mlengi Wanu
Anthu ambiri amakayikira kapena kukana kumene kuti kuli Mlengi chifukwa cha chinyengo cha zipembedzo, ziphunzitso za anthu okhulupirira kuti kulibe Mulungu, monga chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina, ndiponso chifukwa cha kuchuluka kwa mavuto. Komabe, ngati mukufuna, Baibulo lingakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso amene mungakhale nawo. Lingakuthandizeninso kudziwa maganizo a Mulungu omwe ndi “a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.” (Yeremiya 29:11) Ndipo Bernadette, amene mwana wake anabadwa wolumala uja ndiponso ankakayikira kuti kuli Mlengi, chiyembekezo chimenechi chinam’tonthoza ndi kumulimbikitsa kwambiri.
Anthu ambiri amene poyamba ankakhulupirira kuti kulibe Mulungu alimbikitsidwa kwambiri ndi mfundo za m’Baibulo zonena za chifukwa chimene Mulungu walolera kuti anthu azivutika. Ngati mutafufuza zimene Baibulo limanena pankhani zofunika kwambiri ngati zimenezi, inunso mungakhulupirire kuti kunja kuno kuli Mulungu, yemwe “sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Machitidwe 17:27.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Ngati mukufuna kudziwa ngati zili zoyenera kuti Akhristu oona azilowerera nawo m’nkhondo, onani nkhani yakuti, “Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Nawo Nkhondo?” patsamba 29 mpaka 31.
^ ndime 22 Kuti mudziwe chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azivutika, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, patsamba 106 mpaka 114, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 25 Kuti mumve mfundo zothandiza kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa, onani Galamukani! ya September 2006, ndiponso buku lachingelezi lakuti, “Is There a Creator?,” lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Bokosi patsamba 13]
Mafunso Amene Sanayankhidwe ndi Chiphunzitso Chakuti Zamoyo Zinachita Kusanduka
• Kodi zingatheke bwanji kuti moyo uyambike kuchokera ku chinthu china chopanda moyo?—SALMO 36:9.
• N’chifukwa chiyani nyama ndiponso zomera zimabereka mogwirizana ndi mtundu wawo?—GENESIS 1:11, 21, 24-28.
• Ngatidi anthu anachokera ku anyani, n’chifukwa chiyani masiku ano anyani sasanduka anthu?—SALMO 8:5, 6.
• Kodi mtima wofuna kuthandiza ena umene anthu ali nawo ukugwirizana ndi chiphunzitso chakuti zamoyo zamphamvu kwambiri n’zimene ziyenera kupitiriza kukhala ndi moyo?—AROMA 2:14, 15.
• Kodi anthu ali ndi tsogolo lodalirika?—SALMO 37:29.
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Kodi Mulungu yemwe ndi wachikondi, angalenge anthu kuti azivutika?
Chinyengo cha zipembedzo chachititsa kuti anthu ambiri asiye kukhulupirira Mulungu