Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizichita Chiyani?

Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizichita Chiyani?

Yandikirani Mulungu

Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizichita Chiyani?

Deuteronomo 10:12, 13

NTHAWI zambiri zimavuta kuti munthu asankhe pakati pa kumvera kapena kusamvera lamulo. Anthu amagonjera monyinyirika munthu wa udindo amene ndi wankhanza ndiponso wokonda kulamula. Komabe, olambira oona amamvera Yehova Mulungu mwakufuna kwawo. N’chifukwa chiyani amatero? Kuti tiyankhe funso limeneli tiyeni tione mawu a Mose opezeka pa Deuteronomo 10:12, 13. *

Ponena mwachidule zimene Mulungu amafuna kuti anthu azichita, Mose anafunsa funso lochititsa chidwi lakuti: “Yehova Mulungu wanu afunanji nanu?” (Vesi 12) Mulungu ali ndi ufulu wotiuza zimene akufuna kuti tizichita. Ndipotu, iye ndi Ambuye Mfumu amene anatipatsa moyo komanso amene amatisamalira. (Salmo 36:9; Yesaya 33:22) Yehova ndi wofunika kumumvera. Komabe, satikakamiza kuti tizimumvera. Kodi amafuna kuti tizichita chiyani? Amafuna kuti ‘tizimumvera mochokera pansi pa mtima.’​—Aroma 6:17.

Kodi nchiyani chingatithandize kuti tizichita zimenezi? Mose anatchula mfundo imodzi, kuti: “Muziopa Yehova Mulungu wanu.” * (Vesi 12) Zimenezi sizikutanthauza kuti tiziopa Mulungu chifukwa cha zoipa zimene zingatichitikire chifukwa chosamumvera, koma tiziopa Mulungu chifukwa choti timamulemekeza. Choncho ngati timakonda kwambiri Mulungu, tidzayesetsa kupewa kuchita zinthu zimene zingamukhumudwitse.

Kodi ndi chifukwa chachikulu chiti chimene chingatichititse kuti tizimvera Mulungu? Mose ananena kuti: ‘Muzikonda ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.’ (Vesi 12) Kukonda Mulungu kumafuna zambiri osati kungomva mu mtima mwathu kuti timamukonda. Buku lina limati: “Mawu achiheberi otanthauza mmene munthu akumvera mu mtima, amatanthauzanso zimene munthu akuchita chifukwa cha zimene akumva mumtima mwake.” Buku lomweli limanenanso kuti kukonda Mulungu kumatanthauza “kuchita zinthu zosonyeza kuti timamukonda.” Zimenezi zikutanthauza kuti ngati timakondadi Mulungu, tidzayesetsa kuchita zinthu zimene tikudziwa kuti zimusangalatsa.​—Miyambo 27:11.

Kodi tizimvera Mulungu mpaka pati? Mose anati: ‘Yendani m’njira zake zonse za Mulungu.’ (Vesi 12) Yehova amafuna kuti tizichita zonse zimene amatiuza kuchita. Koma kodi kumvera m’zinthu zonse kumeneku sikungatilepheretse kusangalala? Ayi, ndithu.

Mulungu adzatidalitsa kwambiri ngati timamumvera mwakufuna kwathu. Mose analemba kuti: ‘Sungani malamulo amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni.’ (Vesi 13) Inde, chilichonse chimene Yehova amatiuza kuti tizichita chimakhala chotikomera kapena kuti chotithandiza. Choncho, sichingatilepheretse kusangalala. Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) N’chifukwa chake anatipatsa malamulo amene angatithandize kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. (Yesaya 48:17) Kuchita zonse zimene Yehova amafuna kuti tizichita kumatithandiza kupewa zokhumudwitsa zambiri panopa ndipo kudzatithandiza kuti mtsogolo muno, tidzapeze madalitso ambiri mu ulamuliro wa Ufumu wake. *

Mukafuna kusankha pakati pa kumvera kapena kusamvera zimene Yehova amakuuzani kuti muzichita, chinthu chanzeru chimene muyenera kuchita ndi kumvera Mulungu ndi mtima wonse ndiponso mwakufuna kwanu. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuyandikira kwa Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi, amene nthawi zonse amakufunirani zabwino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Ngakhale kuti Mose ankauza mawu amenewa Aisiraeli akale, mfundo zake n’zothandiza kwa anthu onse amene akufuna kusangalatsa Mulungu masiku ano.​—Aroma 15:4.

^ ndime 3 M’buku lonse la Deuteronomo, Mose anatsindika mfundo yakuti chinthu chofunika kwambiri kwa anthu onse okhulupirika ndi kuopa Mulungu.​—Deuteronomo 4:10; 6:13, 24; 8:6; 13:4; 31:12, 13.

^ ndime 6 Kuti mumve zambiri pankhaniyi, onani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pamutu 3 wakuti “Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili?” lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.