Bodza Lachisanu: Mariya Ndi Amayi a Mulungu
Kodi bodzali linayamba bwanji?
Buku lina limati: “Kulambira amayi a Mulungu kunayamba kufala kwambiri pamene . . . anthu ambiri akunja anayamba kulowa Chikhristu. . . . Anthuwa anali atayamba kale kwambiri kulambira ‘mayi wolemekezeka’ ndiponso ‘namwali woyera.’”—The New Encyclopædia Britannica (1988), Voliyumu 16, tsamba 326 ndi 327.
Kodi Baibulo limati chiyani?
Limanena kuti: “Udzakhala ndi pathupi nudzabereka mwana wamwamuna, ndipo udzam’patse dzina lakuti Yesu. Ameneyu adzakhala wamkulu nadzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. . . . Pachifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.”—Luka 1:31-35.
Lembali likusonyeza kuti Mariya anali amayi a “Mwana wa Mulungu,” osati amayi a Mulungu. Ndiponso kodi zikanatheka bwanji kuti Mariya atenge pathupi pa amene ‘m’mwamba mumachepa kumulandira’? (1 Mafumu 8:27) Komanso Mariya sananene kuti anali amayi a Mulungu. Chiphunzitso chakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi n’chimene chinachititsa kuti anthu azikhulupirira kuti Mariya ndi amayi a Mulungu. Chifukwa chonena kuti Mariya ndi Theotokos (mawu achigiriki otanthauza “wobereka Mulungu”), kapena kuti “Amayi a Mulungu,” msonkhano umene unachitikira ku Efeso, mu 431 C.E., unachititsa kuti anthu azilambira Mariya. Anthu a mumzinda wa Efeso, kumene kunachitikira msonkhano wa tchalitchi umenewu, kwanthawi yaitali ankakonda kulambira fano la mulungu wamkazi wotchedwa Atemi amene iwo ankakhulupirira kuti amathandiza anthu ndiponso zinthu zina kuti zizibereka bwino.
Choncho, polambira Mariya, anthu anayambanso kuchita zinthu zina monga kuguba, zimene anthu ankachitika polambira Atemi, amene ankakhulupirira kuti ‘anagwa kuchokera kumwamba.’ (Machitidwe 19:35) Ndipo chinthu china chimene Akhristu anayambanso kuchita ndicho kugwiritsa ntchito mafano a Mariya ndiponso a anthu ena polambira.
Yerekezani ndi mavesi awa: Mateyo 13:53-56; Maliko 3:31-35; Luka 11:27, 28
ZOONA N’ZAKUTI:
Mariya anali amayi a Mwana wa Mulungu, osati amayi a Mulungu. Bodza lakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi linachititsa kuti anthu azilambira Mariya ngati Amayi a Mulungu