Kodi Mboni za Yehova ndi Chipembedzo Chachipolotesitanti?
Zimene Owerenga Amafunsa
Kodi Mboni za Yehova ndi Chipembedzo Chachipolotesitanti?
Chipembedzo cha Mboni za Yehova si chachipolotesitanti. N’chifukwa chiyani tikutero?
Chipolotesitanti chinayambika m’zaka za m’ma 1500 ndi anthu omwe ankafuna kukonza zina ndi zina m’tchalitchi cha Roma Katolika. Mawu akuti “Apolotesitanti” anayamba kugwiritsidwa ntchito pamsonkhano umene unachitikira mumzinda wa Speyer, m’chaka cha 1529 ndipo ankanena za anthu otsatira Martin Luther. Kuyambira nthawi imeneyo, mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za anthu amene amatsatira mfundo ndiponso zolinga za anthu ofuna kukonza zinthu m’tchalitchi cha Katolika. Buku lina lotanthauzira mawu limati Mpolotesitanti ndi “amene ali m’tchalitchi chilichonse chimene chimakana zoti papa ali ndi ulamuliro padziko lonse. Komanso ndi munthu yemwe amakhulupirira kuti chofunika kwambiri kuti munthu adzapulumuke ndi chikhulupiriro basi. Ndi amene amakhulupiriranso kuti Mkhristu aliyense ayenera kukhala wansembe ndiponso kuti Baibulo ndi lokhalo limene lili ndi choonadi.”—Merriam-Webster’s Collegiate Dictionary, 11th Edition.
Mboni za Yehova ndi zosiyana kwambiri ndi matchalitchi achipolotesitanti ngakhale kuti sizivomereza zoti papa ali ndi ulamuliro padziko lonse ndiponso zimakhulupirira kuti Baibulo ndi buku limene lili ndi choonadi. Ndipo buku lina limachita kunena kuti Mboni za Yehova “n’zosiyana kwambiri” ndi zipembedzo zina zonse. (The Encyclopedia of Religion ) Taonani mbali zitatu zimene Mboni za Yehova zimasiyana ndi zipembedzo zina.
Choyamba, ngakhale kuti Apolotesitanti amakana zikhulupiriro zina zachikatolika, atsogoleri awo anatengera mfundo zina zachikatolika, monga chikhulupiriro choti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi komanso choti Mulungu amaotcha anthu kumoto ndiponso choti mzimu sumafa. Koma Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti zikhulupiriro zimenezi sizigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa komanso zimachititsa kuti Mulungu azioneka ngati woipa.—Onani tsamba 4 mpaka 7 m’magazini ino.
Chachiwiri, cholinga cha Mboni za Yehova sikutsutsa ziphunzitso za matchalitchi ena, koma kuphunzitsa choonadi. Mboni za Yehova zimatsatira kwambiri malangizo a m’Baibulo akuti: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse. Ayeneranso kukhala woyenerera kuphunzitsa, wougwira mtima pokumana ndi zoipa, wolangiza mofatsa anthu otsutsa.” (2 Timoteyo 2:24, 25) Mboni za Yehova zimasonyeza kusiyana kwa zimene Baibulo limanena ndi zimene zipembedzo zambiri zimaphunzitsa. Komabe cholinga chawo pochita zimenezi sichikhala kukonza zinthu m’zipembedzozo, koma kuthandiza munthu aliyense wofunitsitsa kuti adziwe zoona zenizeni za Mulungu ndiponso Mawu ake, Baibulo. (Akolose 1:9, 10) Anthu azipembedzo zina akamatsutsa kwambiri zimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa, sizilimbana nawo.—2 Timoteyo 2:23.
Chachitatu, mosiyana ndi Apolotesitanti, omwenso agawikanagawikana m’matchalitchi ambirimbiri, Mboni za Yehova ndi zogwirizana kwambiri padziko lonse lapansi. Ndipo tikanena za zikhulupiriro zawo za m’Baibulo, Mboni za Yehova, zomwe zili m’mayiko oposa 230, zimatsatira malangizo a Paulo akuti ‘muzilankhula chinthu chimodzi.’ N’chifukwa chake palibe magawano pakati pawo, koma ndi ‘zogwirizana bwino lomwe pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.’ (1 Akorinto 1:10) Mboni za Yehova zimayesetsa ‘kusunga umodzi wawo mwa mzimu, ndi mwamtendere monga chomangira chowagwirizanitsa.’—Aefeso 4:3.