Iye Amafuna Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino
Yandikirani Mulungu
Iye Amafuna Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino
MAKOLO amene amakonda ana awo amafunitsitsa kuti anawo zinthu ziziwayendera bwino komanso kuti akhale ndi moyo wosangalala. Nayenso Yehova, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino padzikoli. Posonyeza kuti amatikonda, iye amatiuza zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino. Mwachitsanzo, taganizirani mawu amene anauza Yoswa, opezeka pa Yoswa 1:6-9.
Onani chithunzichi ndipo ganizirani mmene zinthu zinalili panthawiyo. Mose atamwalira, Yoswa anakhala mtsogoleri wa Aisiraeli omwe analipo ochuluka kwambiri, mpaka kufika mamiliyoni ochuluka. Panthawiyi, Aisiraeli anali akukonzekera kulowa m’dziko limene Mulungu analonjeza makolo awo. Choncho, Mulungu anapereka malangizo kwa Yoswa omwe akanamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino ngati akanawatsatira. Koma malangizowo sanali othandiza kwa Yoswa yekhayo ayi. Ifenso zinthu zingatiyendere bwino ngati titawatsatira.—Aroma 15:4.
Katatu konse, Yehova anauza Yoswa kuti alimbe mtima ndiponso asachite mantha. (Mavesi 6, 7 ndi 9) N’zodziwikiratu kuti Yoswa anafunika kukhala wamphamvu ndiponso wolimba mtima kuti atsogolere mtundu wa Aisiraeli kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Koma kodi iye anayenera kuchita chiyani kuti akhale wamphamvu ndiponso wolimba mtima?
Malemba ouziridwa akanathandiza Yoswa kukhala wolimba mtima komanso wamphamvu. Tikutero chifukwa Yehova anati: “Usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga.” (Vesi 7) Panthawiyo, n’kutheka kuti Yoswa anali ndi mabuku ochepa chabe a m’Baibulo omwe anali atalembedwa. * Komabe, kungokhala ndi Mawu a Mulungu sikukanapangitsa kuti zinthu zizimuyendera bwino. Koma kuti mawuwo amuthandize, Yoswa anafunika kuchita zinthu ziwiri.
Choyamba, Yoswa anayenera kuika Mawu a Mulungu mumtima mwake. Yehova anamuuza kuti: “Ulingiriremo usana ndi usiku.” (Vesi 8) Buku lina linati: “Pavesili, Mulungu ankalamula Yoswa kuti azikumbukira Chilamulo Chake ‘posinkhasinkha’ ndiponso ‘kuganizira’ zimene wawerengazo.” Kuwerenga ndiponso kusinkhasinkha Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku kukanathandiza Yoswa kuti athane ndi mavuto amene akanakumana nawo.
Chachiwiri, Yoswa anafunika kugwiritsa ntchito zomwe ankaphunzira m’Mawu a Mulungu. Yehova anamuuza kuti: “Usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako.” (Vesi 8) Motero, kuti zinthu zimuyendere bwino, Yoswa anafunika kuchita zinthu zimene Mulungu amafuna. Ndipotu palibe chimene chikanamuyendera akanapanda kumvera Mawu a Mulungu. Munthu aliyense akamachita chifuniro cha Mulungu, zinthu zimamuyendera bwino.—Yesaya 55:10, 11.
Yoswa, yemwe ankalambira Yehova mokhulupirika anamvera malangizo amenewa. Zimenezi zinam’thandiza kuti iye akhale ndi moyo wabwino ndiponso wosangalala.—Yoswa 23:14; 24:15.
Kodi inunso mukufuna kukhala ndi moyo wosangalala ngati wa Yoswa? Yehova amafuna kuti inuyo zinthu zizikuyenderani bwino ndiponso muzisangalala. Koma kungokhala ndi Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, sikokwanira. Mkhristu wina yemwe watumikira Yehova mokhulupirika kwa nthawi yaitali ananena malangizo abwino akuti: “Muziwerenga Baibulo nthawi zonse ndiponso muzigwiritsa ntchito zimene mukuwerengazo.” Ngati mumawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse n’kumatsatira zimene mukuphunzirazo, ndiye kuti ‘mudzakometsera njira yanu’ ngati Yoswa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Zikuoneka kuti mabuku ouziridwa omwe Yoswa anali nawo panthawiyo anali mabuku asanu olembedwa ndi Mose (Genesis, Eksodo, Levitiko, Numeri ndi Deuteronomo), buku la Yobu ndiponso Salmo limodzi kapena awiri.