Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi kalembera amene anachititsa kuti Yesu abadwire ku Betelehemu anali wotani?

Uthenga wa Luka umafotokoza kuti Kaisara Augusto atalamula kuti m’madera onse olamulidwa ndi ufumu wa Roma muchitike kalembera, “anthu onse anapita kukalembetsa, aliyense kumzinda wa kwawo.” (Luka 2:1-3) Yosefe, yemwe anali bambo wa Yesu womulera, anali wa ku Betelehemu. Ndipo pomvera lamuloli, Yosefe ndi Mariya anayenda ulendo umene unachititsa kuti Yesu akabadwire ku Betelehemu. Kalembera ameneyu ankathandiza pokhoma misonkho komanso polemba asilikali.

Pamene Aroma ankagonjetsa Aiguputo mu 30 B.C.E., Aiguputo anali atachita kalembera wotereyu kwa zaka zambiri. Akatswiri amaphunziro amakhulupirira kuti Aroma anatengera mmene Aiguputo ankachitira kalembera wawo.

Umboni wosonyeza kuti kalembera wotereyu ankachitika, ndi kalata yolamula kuti m’dzikomo muchitike kalembera ya mu 104 C.E., imene kazembe wachiroma yemwe ankayang’anira dziko la Iguputo analemba. Kalatayi ikusungidwa kunyumba yosungira mabuku ya British Library. Kalatayi imati: “Gaius Vibius Maximus, kazembe wa ku Iguputo (akuti): Poona kuti nthawi yoti kalembera achitike panyumba iliyonse yakwana, ndi bwino kulimbikitsa aliyense kuti amene akukhala dera lina pa zifukwa zilizonse, abwerere kwawo n’cholinga choti akalembetse. Komanso ayenera kuonetsetsa kuti walima bwinobwino munda wake umene anagawiridwa.”

N’chifukwa chiyani Yosefe anaganiza zopatsa Mariya kalata yothetsera ukwati ngakhale kuti anali atangopanga chinkhoswe?

Uthenga Wabwino wa Mateyo umanena kuti Yosefe anadziwa kuti Mariya ali ndi pakati iye ‘ali naye pachitomero.’ Chifukwa chosadziwa kuti Mariya anali ndi pakati “mwa mzimu woyera,” Yosefe ayenera kuti anaganiza kuti Mariya samayenda bwino, choncho anaganiza zom’sudzula.​—Mateyo 1:18-20.

Ayuda ankaona kuti anthu amene achita chinkhoswe n’chimodzimodzi ndi okwatirana. Koma anthuwo sankakhalira limodzi ngati mwamuna ndi mkazi wake mpaka atakwatirana. Chinkhoswe chinali chinthu chapadera kwambiri moti ngati mwamuna wasintha maganizo kapena pazifukwa zina ukwati walephereka, mkaziyo sankaloledwa kukwatiwa mpaka atapatsidwa kalata yothetsera ukwati. Ngati mwamuna wotomera wamwalira, mkaziyo ankaonedwa ngati wamasiye. Ndipo ngati wachita chiwerewere atatomeredwa, ankaonedwa ngati wachita chigololo ndipo ankalandira chilango chophedwa.​—Deuteronomo 22:23, 24.

Zikuoneka kuti Yosefe anaganizira zimene zingachitikire Mariya ngati zitadziwika kuti ali ndi pakati. Ngakhale kuti iye ankaona kuti ayenera kukauza akuluakulu za nkhaniyi, anaganiza kuti amuteteze komanso kuti asam’chititse manyazi. Choncho, anaganiza kuti angomusudzula mwakachetechete. Mayi wosakwatiwa akakhala ndi kalata yothetsera ukwati, chinali chizindikiro choti anakwatiwapo.

[Chithunzi patsamba 16]

Kalata ya mu 104 c.e. ya kazembe Wachiroma, yonena za kalembera

[Mawu a Chithunzi]

© The British Library Board, all rights reserved (P.904)