Kodi Timadziwa Bwanji Kuti Mulungu Amatikonda Kwambiri?
Kodi Timadziwa Bwanji Kuti Mulungu Amatikonda Kwambiri?
NGATI Mulungu amatikonda, n’chifukwa chiyani pali mavuto chonchi? Kuyambira kale anthu akhala akufunsa funso lofunika kwambiri limeneli. Mwina mungavomereze kuti mukamakonda munthu winawake, mumafuna kuti munthuyo asamavutike ndipo ngati ali m’mavuto, mumayesetsa kumuthandiza. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri akamaona kuchuluka kwa mavuto padzikoli amaganiza kuti Mulungu satikonda. Choncho ndi bwino kuti tione kaye umboni wotsimikizira kuti Mulungu amatikonda kwambiri.
Zinthu Zimene Analenga Zimatsimikizira Kuti Mulungu Amatikonda
Yehova Mulungu ndi ‘amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhalamo.’ (Machitidwe 4:24) Tikamaganizira zimene Yehova analenga, sitingakayikire kuti iye amatikonda. Mwachitsanzo, taganizirani zinthu zimene zimakusangalatsani kwambiri. Kodi mumakonda chakudya chinachake? Yehova akanatha kungolenga mtundu umodzi wachakudya kuti tisafe ndi njala. Koma iye analenga zakudya zamitundumitundu kuti tizisankha tokha. Kuwonjezera pa zimenezi, Yehova analenga mitengo, maluwa ndiponso malo osiyanasiyana kuti tizisangalala.
Taganiziraninso mmene tinalengedwera. Timatha kuseka kapena kuchita zinthu zoseketsa, kusangalala ndi nyimbo komanso kuchita chidwi ndi zinthu zokongola. Zimenezi sizofunika kuti tikhale ndi moyo koma ndi mphatso zimene Mulungu anatipatsa kuti tizisangalala. Ndiponso taganizirani anzanu. Palibe munthu amene sasangalala kucheza kapena kukumbatirana ndi munthu amene amakondana naye. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti kukonda ena ndi mphatso yochokera kwa Mulungu yemwe amatikonda. Popeza Mulungu anatilenga kuti tizitha kukonda ena, zimenezi zikutsimikizira kuti iye ndi wachikondi.
Baibulo Limatitsimikizira Kuti Mulungu Amatikonda
Baibulo limanena kuti Mulungu ndiye chikondi. (1 Yohane 4:8) Timaona umboni woti amatikonda pa zimene analenga komanso m’Mawu ake, Baibulo. Mwachitsanzo, m’Baibulo muli mfundo zotithandiza kuti tikhale ndi moyo wabwino, limatilimbikitsa kusachita zinthu motayirira komanso limatichenjeza kuipa kwa uchidakwa ndiponso dyera.—1 Akorinto 6:9, 10.
M’Baibulo mulinso malangizo otithandiza kukhala bwino ndi ena, monga kukondana, kulemekezana ndiponso kuchitirana chifundo. (Mateyo 7:12) Limaletsa makhalidwe amene amabweretsa mavuto. Makhalidwe amenewa ndi monga umbombo, miseche, nsanje, chigololo ndiponso kupha anthu. Ndipotu zikanakhala kuti aliyense amatsatira malangizo abwino kwambiri a m’Baibulo, bwenzi padzikoli pali mavuto ochepa kwambiri.
Umboni wamphamvu kwambiri wosonyeza kuti Mulungu amatikonda ndi zimene anachita popereka Mwana wake, Yesu ngati dipo lotiwombola kumachimo. Lemba la Yohane 3:16 limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” Choncho, Yehova anakonzeratu njira yothetsera imfa ndiponso mavuto onse.—1 Yohane 3:8.
Ndithudi, pali umboni wambiri wosonyeza kuti Yehova amatikonda. N’chifukwa chake iye sasangalala akamaona anthu akuvutika. Iye adzathetsa mavuto onse. Koma kodi tingadziwe bwanji mmene Mulungu adzathetsere mavutowa? Baibulo limayankha funso limeneli.
[Chithunzi patsamba 4]
Kukonda ena ndi mphatso yochokera kwa Mulungu yemwe amatikonda