Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Yabwino Kwambiri Yothetsera Mavuto Onse

Njira Yabwino Kwambiri Yothetsera Mavuto Onse

Njira Yabwino Kwambiri Yothetsera Mavuto Onse

MAVUTO ali ponseponse padzikoli ndipo pali anthu ambiri achifundo amene amathandiza anzawo akakhala pamavuto. Mwachitsanzo, madokotala amagwira ntchito usiku ndi usana kuthandiza anthu odwala kapena ovulala. Anthu monga apolisi, akuluakulu aboma ndiponso azachipatala amayesetsa kuthetsa kapena kuchepetsako mavuto amene anthu akukumana nawo. N’zoona kuti iwo angathandize munthu yemwe ali pavutolo koma n’zosatheka kuti athetse mavuto padziko lonse. Palibe munthu kapena bungwe limene lingachite zimenezi. Koma Mulungu yekha ndi amene adzathetse mavuto padziko lonse.

Umboni wa zimenezi timaupeza m’Baibulo, m’buku la Chivumbulutso, lomwe limati: “[Mulungu] adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Taganizirani kuchuluka kwa anthu amene adzasangalale ndi zimenezi. Lembali likusonyeza kuti cholinga cha Mulungu ndi kuthetsa mavuto onse. Iye adzachita zimenezi pothetsa nkhondo, njala, matenda, anthu onse oipa ndiponso kupanda chilungamo. Palibe munthu amene angakwanitse kuchita zimenezi.

Zimene Ufumu wa Mulungu Udzachite

Mulungu adzakwaniritsa zimene walonjeza kudzera mwa Yesu Khristu, yemwe ndi wamphamvu kwambiri kuposa zolengedwa zina zonse. Nthawi idzafika yoti Yesu alamulire dziko lonse monga Mfumu popanda wopikisana naye. Anthu sadzalamulidwanso ndi mafumu, mapulezidenti kapena andale. Koma adzalamulidwa ndi Mfumu imodzi ndiponso boma limodzi, lomwe ndi Ufumu wa Mulungu.

Ufumu umenewo udzathetsa maboma onse a anthu. Kale kwambiri, Baibulo linalosera kuti: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Anthu padziko lonse adzakhala ogwirizana mu Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma lomwe lizidzachita zinthu mwachilungamo.

Yesu ali padziko lapansi ananena maulendo ambiri za Ufumu umenewu. Anautchula m’pemphero la Ambuye pamene amalangiza ophunzira ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mateyo 6:10) Palembali, Yesu anasonyeza kuti Ufumu ndi umene udzachititse kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. Ndipo cholinga cha Mulungu ndi kuthetseratu mavuto padziko lonse.

Boma la Mulungu limene lizidzachita zinthu mwachilungamo, lidzabweretsa madalitso omwe maboma a anthu sangakwanitse. Kumbukirani kuti Yehova anapereka Mwana wake ngati dipo kuti anthu adzapeze moyo wosatha. Ufumu wa Mulungu, womwe ndi wachilungamo, ukamadzalamulira, pang’ono ndi pang’ono anthu adzayamba kukhala angwiro. Ndiyeno n’chiyaninso chidzachitike? Baibulo limati Yehova ‘adzameza imfa ku nthawi yonse ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pankhope zonse.’​—Yesaya 25:8.

Ena angafunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani Mulungu sakuthetsa mavuto mpaka pano? Kodi akudikira chiyani?’ Yehova akanatha kuchita zimenezi kalekale. Iye akanatha kuthetsa mavutowo kapenanso kutiteteza kuti tisamakumane nawo. Koma iye walola kuti mavutowa apitirire, osati chifukwa chodzikonda, koma kuti athandize ana ake a padziko lapansi. Makolo omwe amakonda ana awo amalolera kuti anawo avutike ngati akudziwa kuti mavutowo adzawathandiza kwambiri anawo kukhala ndi tsogolo labwino. N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Iye ali ndi zifukwa zomveka zimene walolera kuti anthu avutike kwa kanthawi ndipo anafotokoza zifukwa zimenezo m’Baibulo. Zifukwazo zimakhudza zinthu monga ufulu wosankha zochita umene anthu ali nawo, uchimo komanso kutsimikizira kuti Yehova yekha ndi amene ali woyenera kulamulira. Baibulo limafotokozanso kuti Satana, yemwe ndi woipa kwambiri, waloledwa kuti alamulire dzikoli kwa kanthawi. *

Ngakhale kuti panopa sitingathe kufotokoza zifukwazo, pali mfundo ziwiri zimene zingatilimbikitse ndiponso kutipatsa chiyembekezo. Mfundo yoyamba ndi yakuti: Yehova adzatidalitsa kwambiri moti tidzaiwala zoti tinkavutika. Ndipotu Mulungu amatilonjeza kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.” (Yesaya 65:17) Mulungu adzathetseratu mavuto onse amene abwera chifukwa cholola kuti zoipa zipitirire kwa kanthawi.

Mfundo yachiwiri ndi yakuti: Mulungu ali ndi nthawi yosasinthika yakuti adzathetse mavuto a anthu. Kumbukirani kuti mneneri Habakuku anafuna kudziwa kuti Yehova adzalola za chiwawa kuchitika mpaka liti. Yehova anamuuza kuti: “Masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu . . . afika ndithu, osazengereza.” (Habakuku 2:3) M’nkhani yotsatirayi, tiona umboni wotsimikizira kuti “nyengo yoikidwiratu” imeneyi yayandikira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Kuti mumve zambiri pankhani ya chifukwa chake Mulungu walola kuti anthu azivutika, onani mutu 11 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 7]

Malemba Amene Amasonyeza Kuti M’tsogolomu Zinthu Zidzakhala Bwino

NKHONDO SIDZAKHALAPONSO:

“Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa padziko lapansi. Aletsa nkhondo kumalekezero a dziko lapansi.”​—Salmo 46:8, 9.

AKUFA ADZAUKA:

“Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”​—Machitidwe 24:15.

PADZAKHALA CHAKUDYA CHOKWANIRA:

“M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.”​—Salmo 72:16.

SIPADZAKHALANSO MATENDA:

“Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”​—Yesaya 33:24.

ANTHU OIPA SADZAKHALAPONSO:

“Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”​—Miyambo 2:22.

PADZAKHALA CHILUNGAMO:

“Taonani mfumu [Yesu Khristu] idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo [mwachilungamo].”​—Yesaya 32:1.

[Zithunzi patsamba 7]

Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto athu onse