Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Nyengo Yoikidwiratu” Yayandikira

“Nyengo Yoikidwiratu” Yayandikira

“Nyengo Yoikidwiratu” Yayandikira

OPHUNZIRA a Yesu ankafunitsitsa kuti mavuto onse athe ngati mmene mneneri Habakuku ankafunira. Atadziwa kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onse padziko lapansi, iwo anafunsa Yesu kuti: “Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu [mu ulamuliro wa Ufumu] ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu chidzakhala chiyani?” (Mateyo 24:3) Poyankha, Yesu ananena kuti Yehova Mulungu yekha ndi amene akudziwa nthawi yeniyeni imene Ufumu wake udzayambe kulamulira padzikoli. (Mateyo 24:36; Maliko 13:32) Komabe, Yesu ndiponso ena mwa aneneri analosera zinthu zimene zidzachitike, zosonyeza kuti nthawiyo yayandikira.​—Onani  bokosi lili kumanjalo.

Kodi simukuvomereza kuti zinthu zimenezi zili paliponse masiku ano? Yesu analoseranso kuti ntchito yophunzitsa anthu Baibulo idzachitika padziko lonse. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.”​—Mateyo 24:14.

Zimenezi n’zimene zikuchitika masiku ano. Mboni za Yehova zikugwira ntchito imeneyi. M’mayiko pafupifupi 236, a Mboni za Yehova oposa 7 miliyoni akuuza anthu zimene Ufumuwo udzachite ndipo akuthandiza anthuwo kuti ayambe kutsatira mfundo za Mulungu, yemwe cholinga chake ndi kuthetsa mavuto osiyanasiyana amene anthu akukumana nawo. Choncho, pitirizani kuphunzira za Ufumu wa Mulungu ndipo mungayembekezere kudzakhala ndi moyo wosatha, m’dziko lopanda mavuto.

[Bokosi patsamba 8]

 Malemba Amene Amanena za Masiku Otsiriza

MATEYO 24:6, 7; CHIVUMBULUTSO 6:4

• Nkhondo zidzachuluka

MATEYO 24:7; MALIKO 13:8

• Zivomezi zikuluzikulu

• Njala

LUKA 21:11; CHIVUMBULUTSO 6:8

• Miliri

MATEYO 24:12

• Kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo

• Kuzirala kwa chikondi

CHIVUMBULUTSO 11:18

• Kuwononga dziko lapansi

2 TIMOTEYO 3:2

• Kukondetsa ndalama

• Kusamvera makolo

• Kudzikonda kwambiri

2 TIMOTEYO 3:3

• Kupanda chikondi chachibadwa

• Kusagwirizanitsika

• Kusadziletsa

• Kusakonda zabwino

2 TIMOTEYO 3:4

• Kukonda zosangalatsa kuposa kukonda Mulungu

2 TIMOTEYO 3:5

• Kuchuluka kwa anthu odzitcha kuti ndi Akhristu

MATEYO 24:5, 11; MALIKO 13:6

• Kuchuluka kwa aneneri onyenga

MATEYO 24:9; LUKA 21:12

• Kuzunzidwa kwa Akhristu oona

MATEYO 24:39

• Anthu osalabadira zimene Baibulo limachenjeza

[Chithunzi patsamba 8]

Mboni za Yehova padziko lonse zikuphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu