Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amakwaniritsa Malonjezo

Amakwaniritsa Malonjezo

Yandikirani Mulungu

Amakwaniritsa Malonjezo

YOSWA 23:14

KODI zimakuvutani kukhulupirira anthu ena? N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu ambiri sakhulupirirana. Ngati munthu wina yemwe munkamukhulupirira kwambiri anakukhumudwitsanipo, mwina pokunamizani kapena polephera kukwaniritsa zimene anakulonjezani, mungasiye kumukhulupirira. Komabe, pali winawake yemwe mungamukhulupirire ndipo sangakukhumudwitseni ngakhale pang’ono. Lemba la Miyambo 3:5 limatilimbikitsa kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse.” N’chifukwa chiyani Yehova ali woyenera kumukhulupirira choncho? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione mawu a Yoswa, yemwe anali munthu wokhulupirira kwambiri Yehova, opezeka pa Yoswa 23:14.

Taganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Yoswa, yemwe analowa m’malo mwa Mose ngati mtsogoleri wa Aisiraeli, anali atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 110. Pa nthawi yonse ya moyo wake, iye anaona zinthu zambiri zodabwitsa zimene Yehova anachitira Aisiraeli, monga kuwapulumutsa modabwitsa pa Nyanja Yofiira, zaka 60 m’mbuyomo. Ndiyeno pa nthawi imene Yoswa ankaganizira zomwe zinachitika pamoyo wake, anaitanitsa ‘akuluakulu, akulu, oweruza ndi akapitawo,’ achiisiraeli. (Yoswa 23:2) Zimene iye analankhula nawo zinasonyeza nzeru za munthu wachikulire ndiponso kuti anali ndi chikhulupiriro.

Yoswa anawauza kuti: “Taonani, lerolino ndirikumuka njira ya dziko lonse lapansi.” Mawu akuti “njira ya dziko lonse lapansi” ndi mawu ophiphiritsa, otanthauza imfa. Pamenepa, Yoswa amatanthauza kuti, “Ndatsala pang’ono kufa.” Atadziwa kuti watsala pang’ono kumwalira, Yoswa ayenera kuti ankakhala nthawi yaitali akuganizira za moyo wake. Kodi iye anawauza chiyani anthuwo potsanzikana nawo?

Yoswa anapitiriza kuti: “Pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasowapo mawu amodzi.” Awatu ndi mawu a munthu yemwe ankakhulupirira kwambiri Mulungu. N’chifukwa chiyani ananena mawu amenewa? Ataona zonse zimene Mulungu anachita, Yoswa anadziwa kuti nthawi zonse Yehova amakwaniritsa zimene walonjeza. * Pamenepa mfundo ya Yoswa inali yakuti: Aisiraeli asamakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova adzakwaniritsa zimene anawalonjeza.

Poikira ndemanga lemba la Yoswa 23:14, buku lina linanena kuti: “Fufuzani malonjezo onse a m’Baibulo, kenako fufuzani zochitika za m’dzikoli; ndipo funsani munthu aliyense kuti akuuzeni pamene Mulungu sanakwaniritse kapena kuiwala malonjezo ake.” Ngati munthu angakwanitse kuchita kafukufuku ameneyu, adzafikabe pamfundo yofanana ndi imene Yoswa anapeza yakuti: Yehova salephera kukwaniritsa zimene walonjeza.​—1 Mafumu 8:56; Yesaya 55:10, 11.

M’Baibulo muli zinthu zambiri zimene Mulungu analonjeza ndipo zinakwaniritsidwa, kuwonjezera pa zimene inuyo mwakhala mukuona zikukwaniritsidwa. Mulinso zinthu zabwino kwambiri zimene Yehova analonjeza zonena za tsogolo lathu. * Yesetsani kuti muone nokha malonjezo amenewa m’Baibulo. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuona kuti Mulungu, yemwe amakwaniritsa malonjezo, ndi woyeneradi kumukhulupirira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Taonani ena mwa malonjezo amene Yoswa anaona akukwaniritsidwa. Yehova adzapatsa Aisiraeli dziko lawolawo. (Yerekezerani Genesis 12:7 ndi Yoswa 11:23.) Yehova adzalanditsa Aisiraeli m’dziko la Iguputo. (Yerekezerani Eksodo 3:8 ndi Eksodo 12:29-32.) Yehova adzasamalira anthu ake.​—Yerekezerani Eksodo 16:4, 13-15 ndi Deuteronomo 8:3, 4.

^ ndime 6 Kuti mudziwe zambiri za malonjezo okhudza tsogolo lathu amene Mulungu walonjeza, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pamutu 3, 7 ndi 8. Bukuli limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.