Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Kumwa Mowa

Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Kumwa Mowa

Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Kumwa Mowa

TONY, amene watchulidwa munkhani yoyamba ija, bwenzi ali ndi moyo wosangalala akanavomereza kuti anali ndi vuto lomwa mwauchidakwa. Komabe, chifukwa chakuti ankamwa mowa wambiri popanda kudziwika kuti waledzera, ankaona kuti palibe vuto lililonse. N’chifukwa chiyani maganizo a Tony anali olakwika?

Iye ankalephera kuganiza bwino chifukwa chomwa mowa kwambiri. Kaya Tony ankadziwa kapena ayi, ubongo wake unkalephera kugwira bwino ntchito akaledzera. Iye akamwa kwambiri, m’pamenenso ankalephera kudziwa kuti ali ndi vuto lomwa mowa mwauchidakwa.

Chifukwa china chimene chinkachititsa kuti Tony alephere kudziwa kuti anali ndi vutoli chinali choti ankafunitsitsa kuti apitirize kumwa mowa kwambiri. Allen, yemwenso tam’tchula m’nkhani yapita ija, poyamba ankakana zoti ali ndi vuto lomwa mowa mwauchidakwa. Iye ananena kuti: “Sindinkafuna kuti ena adziwe kuti ndimamwa kwambiri mowa ndipo ndinkapereka zifukwa zosonyeza kuti palibe vuto lililonse ndi mmene ndikumwera komanso ndinkakonda kunena kuti sindimwa mowa mwauchidakwa. Ndinkachita zonsezi n’cholinga choti ndisasiye kumwa mowa.” Ngakhale kuti anthu ankaona kuti Tony ndi Allen akumamwa mowa kwambiri, eniakewo ankaona kuti alibe vuto lililonse. Ndipo onsewa anafunika kuyesetsa kuti asinthe khalidwe lawo. Komano kodi anayenera kuchita chiyani?

Yesetsani Kupewa Kumwa Mowa Mwauchidakwa

Anthu ambiri omwe anasiya kumwa mowa mwauchidakwa anatsatira mawu a Yesu akuti: “Ngati diso lako lakumanja limakupunthwitsa, ulikolowole ndi kulitaya. Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse liponyedwe m’Gehena.”​—Mateyo 5:29.

Pamenepa, sikuti Yesu ankalimbikitsa kuti tizidzidula ziwalo koma ankaphunzitsa mfundo yoti tizisiyiratu khalidwe lililonse limene lingawonongetse ubwenzi wathu ndi Yehova. N’zoona kuti zilizonse zimene tingachite pothana ndi vutoli zingatiwawe kwambiri koma zingatithandize kuti tisamaganize kapena kuchita zinthu zimene zingachititse kuti tizimwa mowa mwauchidakwa. Choncho, ngati ena akuuzani kuti mwayamba kumwa mowa mwauchidakwa, yesetsani kuti muchepetse. * Ngati zikuonekeratu kuti simungathe, yesetsani kuti mungosiyiratu kumwa mowa. Ngakhale kuti zimenezi zingakhale zopweteka kwambiri, koma n’zabwino kusiyana ndi kukhala ndi moyo wosalongosoka.

Mwina inuyo sichidakwa, koma kodi mumakonda kumwa mowa kwambiri? Ngati zili choncho, kodi mungachite chiyani kuti muzimwa moyenera?

Zinthu Zimene Zingakuthandizeni

1. Muzipemphera kawirikawiri ndiponso mochokera pansi pa mtima. Baibulo limalangiza anthu amene akufuna kusangalatsa Yehova Mulungu kuti: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Kodi mungatchule zinthu ziti m’pemphero kuti mukhale ndi mtendere wa mumtima umenewu?

Vomerezani moona mtima kuti muli ndi vuto lomwa mowa mwauchidakwa ndipo muziona kuti ndi udindo wanu kuthana ndi vutolo. Muuzeni Mulungu zimene mukufuna kuchita kuti muthane ndi vutolo komanso kuti mupewe mavuto ena ndipo iye adzakuthandizani. Baibulo limati: “Wobisa machimo ake sadzaona mwayi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.” (Miyambo 28:13) Yesu ananenanso kuti tingapemphe kuti: “Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.” (Mateyo 6:13) Ndiyeno kodi mungatani kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi mapemphero anuwo? Nanga mungadziwe bwanji kuti Mulungu wayankha mapemphero anu?

2. Dalirani Mawu a Mulungu. Baibulo limati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, . . . Amathanso kuzindikira malingaliro ndi zolinga za mtima.” (Aheberi 4:12) Anthu ambiri omwe poyamba anali zidakwa aona kuti kuwerenga Baibulo tsiku lililonse ndiponso kusinkhasinkha kwawathandiza kwambiri. Munthu wina woopa Mulungu, yemwe analemba nawo masalmo anati: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m’njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pabwalo la onyoza. Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. . . . Zonse azichita apindula nazo.”​—Salmo 1:1-3.

Allen, yemwe anathana ndi vuto lake lomwa mowa mwauchidakwa chifukwa chophunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anati: “Ndimakhulupirira kuti zikanakhala kuti sindinaphunzire Baibulo ndiponso sinditsatira mfundo zake, zomwe zinandithandiza kuti ndisiye kumwa mowa mwauchidakwa, bwenzi pano nditafa kalekale.”

3. Muzidziletsa. Baibulo limanena kuti anthu ena omwe poyamba anali zidakwa mumpingo wachikhristu anasambitsidwa “ndi mzimu wa Mulungu wathu.” (1 Akorinto 6:9-11) Kodi zimenezo zinatheka bwanji? Njira imodzi inali yoti anathandizidwa kusiya kumwa mowa mwauchidakwa ndiponso kuchita maphwando aphokoso. Iwo anakwanitsa kusiya zimenezi chifukwa chokhala ndi khalidwe lodziletsa lomwe munthu amakhala nalo chifukwa chothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Baibulo limati: “Musamaledzere naye vinyo, mmene muli makhalidwe oipa, koma khalanibe odzala ndi mzimu.” (Aefeso 5:18; Agalatiya 5:21-23) Yesu Khristu analonjeza kuti ‘Atate wakumwamba adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.’ Choncho, “pemphanibe, ndipo adzakupatsani.”​—Luka 11:9, 13.

Anthu omwe akufuna kulambira Yehova movomerezeka angathe kukhala odziletsa ngati amawerenga ndi kuphunzira Baibulo ndiponso kupemphera nthawi zonse mochokera pansi pa mtima. M’malo moganiza kuti simungathe kukhala odziletsa, khulupirirani lonjezo la m’Mawu a Mulungu lakuti: “Iye amene akufesera mzimu adzakolola moyo wosatha ku mzimuwo. Choncho tisaleke kuchita zabwino, pakuti panyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.”​—Agalatiya 6:8, 9.

4. Muzicheza ndi anthu akhalidwe labwino. Baibulo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Uzani anzanu kuti mwatsimikiza mtima kusiya kumwa mowa mwauchidakwa. Komabe, Mawu a Mulungu amachenjeza kuti mukasiya “kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando a phokoso, kumwa kwa mpikisano,” anzanu ena omwe munkamwa nawo ‘sangamvetse, choncho angamakunyozeni.’ (1 Petulo 4:3, 4) Musamacheze ndi anthu amene sakufuna kuti muchepetse kumwa mowa.

5. Dziikireni malire. Baibulo limati: “Musamatengere nzeru za dongosolo lino la zinthu, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Mukalola kuti mfundo za m’Mawu a Mulungu zikuthandizeni kuika malire pankhani ya kumwa mowa, osati anzanu kapena “dongosolo lino la zinthu,” mudzachita zinthu zosangalatsa Mulungu pamoyo wanu. Koma kodi mungadziwe bwanji kuti muyezo wa mowa womwe mwasankhawo ndi wabwino kwa inu?

Ngati mwamwa mowa ndipo mukulephera kuganiza bwino, ndiye kuti mwamwa mopitirira malire anu. Choncho ngati mwasankha kuti muzimwa mowa, ndi bwino kudziikira malire enieni pa kuchuluka kwa mowa umene muzimwa, m’malo moganiza kuti musiya mukaona kuti mwayamba kuledzera. Musalole kuti mtima wosavomereza kuti muli ndi vuto ukulepheretseni kuthana ndi vuto lomwa mowa mwauchidakwa. Ikani malire omwe angakuthandizeni kuti musamwe mowa kwambiri.

6. Muzikana. Baibulo limati: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.” (Mateyo 5:37) Muzikana mwaulemu ngati wina akupitirizabe kukukakamizani kuti mumwe mowa umene iye akukupatsani. Mawu a Mulungu amati: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoleretsa ndi mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.”​—Akolose 4:6.

7. Pemphani kuti ena akuthandizeni. Pemphani kuti anzanu ena omwe angakulimbikitseni kuti musamamwe mowa kwambiri akuthandizeni ndiponso akulimbikitseni mwauzimu. Baibulo limati: “Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m’ntchito zawo. Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake.” (Mlaliki 4:9, 10; Yakobe 5:14, 16) Bungwe lina la ku America loona zoti anthu asamamwe mwauchidakwa linati: “Nthawi zina zingakhale zovuta kuti muchepetse kumwa mowa. Choncho pemphani kuti abale ndiponso anzanu akuthandizeni kuthana ndi vuto lomwa mowa mwauchidakwa.”​—National Institute on Alcohol Abuse and Alcoholism.

8. Musasinthe zimene mwatsimikiza kuchita. Baibulo limati: “Khalani ochita zimene mawu amanena, osati ongomva chabe, ndi kudzinyenga ndi malingaliro onama. Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro laufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.”​—Yakobe 1:22, 25.

Zimene Mungachite Kuti Muthane ndi Vuto la Uchidakwa

Sikuti aliyense amene amamwa kwambiri mowa ndiye kuti ndi chidakwa. Koma ena amayamba kumwa kwambiri ndiponso kawirikawiri moti satha kukhala osamwa. Popeza kuti anthu omwe ndi zidakwa amadalira mowa pamoyo wawo, amafunika kuthandizidwa mwapadera, osati kungodalira thandizo lauzimu komanso kungokhala ndi mtima wofunitsitsa kusiya mowa. Allen ananena kuti: “Nditasiya kumwa mowa, ndinadwala kwambiri. Zimenezi zinandichititsa kudziwa kuti ndinafunika kupita kuchipatala kuwonjezera pa thandizo lauzimu limene ndinkalandira.”

Anthu ambiri omwe amamwa mowa mwauchidakwa amafunika kupita kuchipatala kuti athane ndi vuto lawolo. * Ena amafunika kugonekedwa m’chipatala kuti achire matenda amene amabwera munthu akasiya kumwa mowa mwauchidakwa. Komanso kuti alandire mankhwala othandiza kuti asiye kulakalaka kwambiri mowa ndiponso kuti awathandize kuti asafunenso kumwa mowa. Mwana wa Mulungu amene ankachita zozizwitsa ananena kuti: “Anthu amphamvu safuna wochiritsa, koma odwala ndi amene amam’funa.”​—Maliko 2:17.

Ubwino Wotsatira Malangizo a Mulungu

Malangizo othandiza omwe amapezeka m’Baibulo ndi ochokera kwa Mulungu woona, amene amatifunira zabwino. Amafuna kuti tizisangalala panopa komanso kuti zinthu zizitiyendera bwino kwa moyo wathu wonse. Allen watha zaka 24 atasiya mowa ndipo ananena kuti: “Ndinasangalala kudziwa kuti ndikhoza kusintha khalidwe komanso ndinaphunzira kuti Yehova ankafunitsitsa kundithandiza kuti ndisinthe khalidwe langa loipa ndipo . . . ” Allen anadukiza kaye kulankhula pofuna kudzigwira kuti asalire chifukwa chokumbukira nthawi imene ankamwa mowa mwauchidakwayo. Kenako iye anapitiriza kuti, “Kungoti, . . . zimandilimbikitsa kwambiri ndikakumbukira kuti Yehova amatimvetsa ndiponso amatisamalira komanso kutithandiza.”

Choncho, ngati mukulephera kusiya khalidwe lomwa mowa mwauchidakwa, musaganize kuti ndinu wolephera kapena kuti simungathenso kuthana ndi vutolo. Allen komanso anthu ena ambirimbiri analinso ndi vuto ngati lanu ndipo anachepetsa kumwa mowa komanso ena anangosiyiratu. Iwo sadandaula kuti anasiya mowa ndiponso inuyo simudzadandaula.

Kaya mwasankha kuti muzimwa mowa pang’ono kapena mwasankha zongosiyiratu, tsatirani malangizo a Mulungu akuti: “Bwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”​—Yesaya 48:18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Onani bokosi lakuti,  “Kodi Ndimamwa Mowa Mwauchidakwa?” patsamba 8.

^ ndime 24 Pali zipatala zambiri ndiponso malo ena othandizira anthu amene ali ndi vuto lomwa mowa mwauchidakwa. Nsanja ya Olonda sisankhira anthu mankhwala. Aliyense ayenera kufufuza bwino za mankhwala n’kusankha yekha mankhwala amene satsutsana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 8]

 Kodi Ndimamwa Mowa Mwauchidakwa?

Dzifunseni kuti:

• Kodi panopa ndikumamwa mowa kwambiri kuposa kale?

• Kodi ndikumamwa kawirikawiri kuposa kale?

• Kodi panopa ndikumafuna kuti mowa wake uzikhala wamphamvu kwambiri?

• Kodi ndikumamwa mowa n’cholinga choti ndiiwale mavuto?

• Kodi mnzanga kapena wachibale wina wandichenjezapo kuti ndikumwa mowa kwambiri?

• Kodi ndakumanapo ndi mavuto panyumba, kuntchito kapena paulendo chifukwa chomwa mowa mwauchidakwa?

• Kodi zikumandivuta kutha mlungu umodzi ndisanamwe mowa?

• Kodi sindisangalala anthu ena akamakana kumwa mowa?

• Kodi ndimabisira anthu ena kuchuluka kwa mowa umene ndimamwa?

Ngati pamafunso amenewa mwayankha funso limodzi kapena angapo kuti inde, ndiye kuti mukufunika kusintha.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 9]

Chitani Zinthu Mwanzeru Pankhani ya Kumwa Mowa

Musanamwe mowa, dzifunseni kuti:

Kodi ndikuyeneradi kumwa mowa?

Malangizo: Munthu amene amalephera kudziletsa ayenera kupeweratu kumwa mowa.

Kodi ndizimwa mowa wochuluka bwanji?

Malangizo: Dziwani pamene muyenera kusiyira kumwa mowa musanayambe kuledzera.

Kodi ndizimwa nthawi yanji?

Malangizo: Musamwe mowa n’kuyendetsa galimoto kapena kugwira ntchito inayake imene imafuna kusamala kwambiri. Musamwe mowa kenako n’kupita kolambira Mulungu; musamwe mowa ngati muli ndi pakati komanso ngati mukulandira chithandizo cha mankhwala a matenda enaake.

Kodi ndizikamwera kuti?

Malangizo: Pamalo amene pali anthu amakhalidwe abwino; musamwere kwanokha pofuna kuti ena asakuoneni; musamwere pamalo pamene pali anthu omwe amadana ndi mowa.

Kodi ndizimwa ndi ndani?

Malangizo: Ndi anzanu kapena abale anu omwe ali ndi makhalidwe abwino. Musamwe mowa ndi zidakwa.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 10]

Mawu a Mulungu Anamuthandiza Kusiya Uchidakwa

Bambo wina wa ku Thailand dzina lake Supot anali chidakwa. Poyamba, iye ankakonda kumwa madzulo basi. Koma pang’ono ndi pang’ono anayamba kumamwanso m’mawa ndi masana. Iye ankamwa mowa n’cholinga choti aledzere. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo ataphunzira kuti Yehova Mulungu sasangalala ndi anthu amene amamwa mowa mwauchidakwa, Supot anasiya kumwa mowa. Koma patapita kanthawi, anayambiranso kumwa ndipo banja lake linakhumudwa kwambiri.

Komabe, Supot anali akukondabe Yehova ndipo ankafunitsitsa kuti azimutumikira m’njira yoyenerera. Akhristu anzake anapitiriza kumuthandiza ndipo iwo anauza mkazi ndi ana ake kuti azicheza naye kwambiri komanso kuti asasiye kumuthandiza. Nthawi imeneyo, mawu osapita m’mbali a pa 1 Akorinto 6:10 onena kuti ‘zidakwa sizidzalowa mu ufumu wa Mulungu,’ anamuthandiza kwambiri kuona kuti kumwa mowa mwauchidakwa ndi nkhani yaikulu. Supot anazindikira kuti anayenera kuyesetsa kuthana ndi vuto lakelo.

Panthawi imeneyi Supot anaganiza zongosiyiratu kumwa mowa. Pamapeto pake mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, Mawu a Mulungu, banja lake komanso mpingo, Supot anathana ndi vuto lake lauchidakwa. Anthu a m’banja lake anasangalala kwambiri iye atabatizidwa posonyeza kuti wadzipereka kuti atumikire Mulungu. Masiku ano Supot amasangalala kwambiri chifukwa ali paubwenzi wabwino ndi Mulungu womwe ankaufunitsitsa kwambiri pamoyo wake. Tsopano iye amagwiritsa ntchito nthawi yake pophunzitsa anthu Mawu a Mulungu.